Cinyanja
Kodi Mulungu Ndiye Amacititsa Kuti Anthu Azibvutika?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt tsa. 18

FUNSO 8

Kodi Mulungu Ndiye Amacititsa Kuti Anthu Azibvutika?

“Nʼzosatheka kuti Mulungu woona acite zoipa, kapena kuti Wamphamvuyonse acite zinthu zolakwika.”

Yobu 34:10

“Munthu akakhala pamayeselo asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.”

Yakobo 1:13

“Muzimutulila nkhawa zanu zonse, cifukwa amasamala za inu.”

1 Petulo 5:7

“Yehova sakucedwa kukwanilitsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonela kuti akucedwa. Koma akuleza nanu mtima cifukwa sakufuna kuti munthu aliyense akaonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”

2 Petulo 3:9