Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 13:1-58
-
MAFANIZO ONENA ZA UFUMU (1-52)
-
Wofesa mbeu (1-9)
-
Cifukwa cake Yesu anali kusewenzetsa mafanizo (10-17)
-
Kufotokoza tanthauzo la wofesa mbeu (18-23)
-
Tiligu ndi namsongole (24-30)
-
Kanjele ka mpilu ndi zofufumitsa (31-33)
-
Kusewenzetsa mafanizo kunakwanilitsa ulosi (34, 35)
-
Kufotokoza tanthauzo la tiligu ndi namsongole (36-43)
-
Cuma cobisika ndi ngale yamtengo wapatali (44-46)
-
Khoka (47-50)
-
Cuma catsopano komanso cakale (51, 52)
-
-
Yesu akanidwa kwao (53-58)
13 Tsiku limenelo Yesu anacoka pa nyumbayo n’kukakhala pansi m’mbali mwa nyanja.
2 Ndiyeno khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye moti anakwela m’bwato n’kukhala pansi, ndipo anthu onsewo anaimilila m’mbali mwa nyanjayo.
3 Kenako anayamba kuwauza zinthu zambili mwa mafanizo, kuti: “Tamvelani! Munthu wina anapita kukafesa mbeu.
4 Pamene anali kufesa mbeuzo, zina zinagwela m’mbali mwa mseu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya.
5 Zina zinagwela pa miyala pomwe panalibe dothi lokwanila, ndipo zinamela mwamsanga cifukwa nthaka inali yosazama.
6 Koma dzuwa litatentha zinawauka, ndipo zinafota cifukwa zinalibe mizu.
7 Mbeu zina zinagwela pa minga, ndipo mingazo zitakula, zinalepheletsa mbeuzo kukula.
8 Koma mbeu zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zinayamba kubala zipatso, mbeu iyi zipatso 100, ina 60, inanso 30.
9 Ali ndi matu amve.”
10 Conco ophunzila ake anabwela ndi kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciani mumalankhula nao mwa mafanizo?”
11 Poyankha iye anati: “Inu mwapatsidwa mwai womvetsa zinsinsi za Ufumu wa kumwamba, koma iwo sanapatsidwe mwai umenewo.
12 Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambili, ndipo adzakhala ndi zoculuka, koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo.
13 Ndiye cifukwa cake ndimalankhula nao mwa mafanizo. Pakuti kuona amaona, koma kuona kwao n’kopanda phindu, ndipo kumva amamva koma kumva kwao n’kopanda phindu komanso samvetsa tanthauzo lake.
14 Ndipo ulosi wa Yesaya ukukwanilitsidwa pa iwo. Ulosiwo umati: ‘Kumva mudzamva ndithu, koma simudzamvetsa tanthauzo lake. Kuona mudzaona ndithu, koma simudzazindikila zimene mukuona.
15 Pakuti anthu awa aumitsa mitima yao, ndipo amva ndi matu ao koma osacitapo kanthu, komanso atseka maso ao. Acita zimenezi kuti asaone ndi maso ao komanso kuti asamve ndi matu ao. Zotulukapo zake n’zakuti samvetsa tanthauzo lake m’mitima yao n’kutembenuka kuti ine ndiwacilitse.’
16 “Koma inu ndinu odala cifukwa maso anu amaona, ndipo matu anu amamva.
17 Pakuti ndithu ndikukuuzani, aneneli ambili komanso anthu olungama anali kulakalaka kuona zimene inu mukuona, ndi kumva zimene inu mukumva.
18 “Tsopano mvetselani tanthauzo la fanizo la munthu wofesa mbeu uja.
19 Munthu aliyense akamva mau a Ufumu koma osamvetsa tanthauzo lake, woipayo amabwela n’kucotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Izi ndizo mbeu zimene zinagwela m’mbali mwa mseu.
20 Mbeu zofesedwa pa miyala ndi munthu amene amamva mau, n’kuwalandila mwacimwemwe nthawi yomweyo.
21 Ngakhale n’conco, mauwo sazika mizu mwa iye,* koma amapitiliza kwa kanthawi. Ndipo cisautso kapena mazunzo akabwela cifukwa ca mauwo, amapunthwa nthawi yomweyo.
22 Mbeu zofesedwa pa minga ndi munthu amene amamva mau, koma nkhawa za nthawi ino* komanso cinyengo camphamvu ca cuma, zimalepheletsa mbeuzo kukula, ndipo sizibala zipatso.
23 Koma mbeu zogwela pa nthaka yabwino ndi munthu amene amamva mau ndi kumvetsa tanthauzo lake, amene amabaladi zipatso, uyu zipatso 100, wina 60, komanso wina 30.”
24 Iye anawauzanso fanizo lina. Anati: “Ufumu wa kumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbeu yabwino m’munda wake.
25 Anthu ali m’tulo, mdani wake anabwela n’kufesa namsongole m’munda wa tiliguwo, kenako anapita.
26 Mmelawo utakula ndi kutulutsa ngala, nayenso namsongole anaonekela.
27 Conco akapolo a mwinimunda uja anabwela n’kumufunsa kuti, ‘Ambuye, sipaja munafesa mbeu yabwino m’munda mwanu? Nanga namsongole wacokela kuti?’
28 Poyankha iye anawauza kuti, ‘Munthu wina wodana nane ndiye anacita zimenezi.’ Akapolowo anamufunsa kuti, ‘Ndiye kodi tipite tikamuzule namsongoleyo?’
29 Iye anawayankha kuti, ‘Ai, kuopela kuti pozula namsongoleyo, mungazulile pamodzi ndi tiligu.
30 Zilekeni zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola, ndipo m’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti: Coyamba sonkhanitsani namsongole n’kumumanga mitolo-mitolo kuti akatenthedwe, kenako sonkhanitsani tiligu n’kumuika m’nkhokwe yanga.’”
31 Iye anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wa kumwamba uli ngati kanjele ka mpilu kamene munthu anatenga n’kukabzala m’munda wake.
32 Kanjele kameneka ndikakang’ono kwambili pa mbeu zonse. Koma kamakula kuposa mbeu zonse za kudimba n’kukhala mtengo, moti mbalame za mumlengalenga zimapeza malo okhala m’nthambi zake.”
33 Anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wa kumwamba uli ngati zofufumitsa zimene mai wina anatenga n’kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zikulu-zikulu zopimila, ndipo mtanda wonsewo unafufuma.”
34 Yesu analankhula zinthu zonsezi ndi khamulo mwa mafanizo. Ndithudi sanalankhule nao popanda kusewenzetsa mafanizo,
35 kuti mau amene ananenedwa kudzela mwa mneneli akwanilitsidwe, akuti: “Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mafanizo. Ndidzalengeza zinthu zimene zakhala zobisika kucokela pa ciyambi.”*
36 Ndiyeno atauza khamu la anthulo kuti lizipita, analowa m’nyumba. Ophunzila ake anabwela kwa iye n’kunena kuti: “Tifotokozeleni tanthauzo la fanizo lija la namsongole m’munda.”
37 Iye anawayankha kuti: “Wofesa mbeu yabwino ndi Mwana wa munthu;
38 ndipo mundawo ndi dzikoli. Mbeu yabwino ndi ana a Ufumu, koma namsongole ndi ana a woipayo,
39 ndipo mdani amene anafesa namsongoleyo ndi Mdyelekezi. Nthawi yokolola ndiyo cimalizilo ca nthawi ino,* ndipo okololawo ndi angelo.
40 Conco monga mmene namsongole amamusonkhanitsila pamodzi ndi kumutentha pamoto, ndi mmenenso zidzakhalila pa cimalizilo ca nthawi ino.*
41 Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake amene adzacotsa mu Ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa kuphatikizapo anthu osamvela malamulo,
42 ndipo adzawaponya mu ng’anjo ya moto. Kumeneko azikalila ndi kukukuta mano.
43 Pa nthawiyo olungama adzawala kwambili ngati dzuwa mu Ufumu wa Atate wao. Ali ndi matu amve.
44 “Ufumu wa kumwamba uli ngati cuma cobisika m’munda, cimene munthu wina anapeza n’kucibisa. Ndipo cifukwa ca cimwemwe cimene anali naco, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.
45 “Komanso Ufumu wa kumwamba uli ngati wamalonda woyenda-yenda amene anali kufuna-funa ngale zabwino.
46 Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali anapita, ndipo mwamsanga anagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula ngaleyo.
47 “Ndiponso Ufumu wa kumwamba uli ngati khoka lalikulu limene linaponyedwa m’nyanja, ndipo linasonkhanitsa nsomba za mitundu-mitundu.
48 Litadzala analikokela ku mtunda, ndipo atakhala pansi anasonkhanitsa nsomba zabwino n’kuziika m’madengu, koma zoipa anazitaya.
49 Ndi mmenenso zidzakhalila pa mapeto a nthawi ino.* Angelo adzapita n’kukacotsa oipa pakati pa olungama,
50 ndipo adzawaponya mu ng’anjo ya moto. Kumeneko azikalila ndi kukukuta mano.
51 “Kodi mwamvetsa tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde.”
52 Ndiyeno anawauza kuti: “Poti zili telo, mphunzitsi aliyense wa anthu amene waphunzitsidwa za Ufumu wa kumwamba, ali ngati mwininyumba amene amatulutsa zinthu zatsopano komanso zakale mosungila cuma cake.”
53 Yesu atatsiliza kuwauza mafanizo amenewa anacoka kumeneko.
54 Atafika m’dela la kwao anayamba kuphunzitsa anthu m’sunagoge wao, moti anthuwo anadabwa kwambili ndipo anati: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti nzelu ndi nchito zamphamvu zimenezi?
55 Kodi ameneyu si mwana wa kalipentala uja? Kodi mai ake si Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni, ndi Yudasi?
56 Komanso alongo ake onse sitili nao konkuno? Nanga zonsezi anazitenga kuti?”
57 Conco anayamba kupunthwa cifukwa ca iye. Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneli salemekezedwa kwao kapena panyumba pake, koma kwina.”
58 Cotelo sanacite nchito zambili zamphamvu kumeneko cifukwa ca kusowa cikhulupililo kwao.
Mau a m'Munsi
^ Kapena kuti, “mauwo samufika pa mtima.”
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Ma Baibo ena amati, “kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.

