Kodi m’Baibo Muli Nkhani Zotani?
M’Baibo muli uthenga, kapena kuti mau a Mulungu omwe ndi ofunika kwa ife lelolino. Baibo imationetsa mmene tingakhalile ndi umoyo wabwino komanso zimene tingacite kuti tikondweletse Mulungu. Imayankhanso mafunso otsatila:
MMENE MUNGAPEZELE MAVESI M’BAIBO
M’Baibo muli mabuku ang’ono-ang’ono okwanila 66. Ili ndi zigao ziwili. Cigao coyamba ndi Malemba a Ciheberi ndi Ciaramu (ena amati “Cipangano Cakale”), ndipo cigao caciwili ndi Malemba a Cigiriki (ena amati “Cipangano Catsopano”). Buku lililonse m’Baibo lili ndi macaputala ndi mavesi. Mukapeza lemba, nambala yotsatizana ndi dzina la bukulo ndi caputala, ndipo nambala kapena manambala otsatila ndi vesi kapena mavesi. Mwacitsanzo, Mateyo 1:1 ikutanthauza Mateyo caputala 1, vesi 1.

