A3
Zimene Zinacitika Kuti Baibo Isungike Mpaka Pano
Mlembi komanso Mwiniwake wa Baibo ndiye anapangitsa kuti isungike. Ndiye anacititsanso kuti mau ali pansipa alembedwe m’Baibo:
“Mau a Yehova adzakhalapo mpaka muyaya.”—1 Petulo 1:25.
Mfundo imeneyi ndi yoona ngakhale kuti palibe mipukutu yapoyamba ya Malemba a Ciheberi ndi a Ciaramu a kapena Malemba a Cigiriki a Cikhristu amene apulumuka kufika pano. Ndiye tingatsimikize motani kuti uthenga umene uli m’Baibo ndi wofanana ndi umene unali m’mipukutu youzilidwa yoyambililayo?
OKOPELA MALEMBA ANATHANDIZA KUTETEZA MAU A MULUNGU
Cimodzi cinathandiza kuteteza Malemba a Ciheberi n’cakuti Mulungu analamula anthu ake kuti azikopela Malemba. b Mwacitsanzo, Yehova analangiza mafumu a Ciisiraeli kuti azilemba makope ao-ao a Cilamulo. (Deuteronomo 17:18) Kuonjezela apo, Mulungu anapatsa Alevi udindo wosunga Cilamulo komanso kuciphunzitsa kwa anthu. (Deuteronomo 31:26; Nehemiya 8:7) Ayuda atabwelako ku ukapolo wa ku Babulo, panakhazikitsidwa gulu la alembi (Soferimu) kuti azikopela Malemba. (Ezara 7:6, mau a m’munsi) M’kupita kwa nthawi, alembiwo anapanga makope ambili a mabuku 39 a Malemba a Ciheberi.
Kwa zaka zambili, alembiwa anali kukopela mabukuwa mosamala kwambili. M’zaka za m’ma 500 C.E. mpaka 1500 C.E., gulu la alembi a Ciyuda amene anali kudziwika kuti Amasoreti, anapitiliza kugwila nchitoyi yokopela malemba. Mpukutu wakale kwambili umene Amasoreti anakopela, ndi wa Leningrad Codex, ndipo anamaliza kuulemba ca m’ma 1008/1009 C.E. Komabe, capakati pa zaka za m’ma 1900, mipukutu pafupifupi 220 ya Baibo kapena zidutswa zake zinapezeka pakati pa mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. Mipukutu imeneyi inalembedwa zaka zoposa 1,000, mpukutu wa Leningrad Codex usanalembedwe. Tikayelekezela zimene zili m’mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ndi zimene zili mu mpukutu wa Leningrad Codex, timapeza mfundo yofunika iyi: Ngakhale kuti mipukutu ya ku Nyanja Yakufa imasiyanako kalembedwe ndi mpukutu wa Leningrad Codex, kusiyana kumeneku sikusintha uthenga wake.
Nanga bwanji za mabuku 27 a Malemba a Cigiriki a Cikhristu? Mabuku amenewo analembedwa koyamba ndi ena mwa atumwi a Yesu Khristu komanso Akhristu ena oyambilila. Potengela zimene alembi a Ciyuda anali kucita, Akhristu oyambililawo anakopela mabukuwa. (Akolose 4:16) Ngakhale kuti wolamulila wina wa Ciroma dzina lake Diocletian komanso anthu ena anayesetsa kuononga zolemba zonse za Akhristu oyambilila, zidutswa zakale masauzande komanso mipukutu yasungika mpaka pano.
Mabuku a Cikhristu anamasulilidwanso m’zinenelo zina. Kumasulila koyambilila kwa Baibo kunacitika m’zinenelo zakale kwambili monga Ciameniya, Cikoputiki, Ciitiopiya, Cijojiya, Cilatini, komanso Cisiriya.
KUSANKHA MALEMBA A CIHEBERI KOMANSO A CIGIRIKI OTI AMASULILIDWE
Si mipukutu yonse ya m’Baibo imene inali ndi mau ofanana. Ndiye tingadziwe bwanji mau amene anali m’mipukutu yoyambilila?
Izi tingaziyelekezele ndi mphunzitsi amene wauza ophunzila 100 kuti akopele caputala cimodzi ca buku. Ngakhale kuti caputala coyambililaco casowa, kuyelekezela zimene zili m’makope 100, kungathandize munthu kudziwa zimene zinali m’caputala coyambililaco. Ngakhale kuti wophunzila aliyense angalakwitse polemba, n’zokaikitsa kuti onse angalakwitse zofanana. Mofananamo, akatsiwili akayelekezela zidutswa komanso makope masauzande amene alipo, amatha kuzindikila zimene okopela analakwitsa komanso kudziwa mau amene anali m’mipukutu yoyambilila.
“Tinganene motsimikiza kuti palibe buku lina lakale lomwe linakopeledwa molondola kwambili ngati mipukutu ya Malemba a Ciheberi”
Kodi n’ciani cingatithandize kukhala otsimikiza kuti mfundo zimene zili m’Baibo zinamasulilidwa molondola kucokela ku mipukutu yoyambilila? Ponena za Malemba a Ciheberi, katswili wina dzina lake William H. Green anati: “Tinganene motsimikiza kuti palibe buku lina lakale limene linakopeledwa molondola kwambili ngati mipukutu ya Malemba a Ciheberi.” Ponena za Malemba a Cigiriki a Cikhristu, amene amadziwikanso kuti Cipangano Catsopano, katswili wina wa Baibo dzina lake F. F. Bruce analemba kuti: “Pali umboni woculuka wakuti mabuku a Cipangano Catsopano anamasulilidwa molondola kwambili kuposa mabuku wamba. Komabe anthu sakaikila nʼkomwe zomwe zili mʼmabuku wambawo.” Iye anakambanso kuti: “Mabuku a Cipangano Catsopano akanakhala kuti ndi mabuku wamba, anthu sakanakaikila kuti mabukuwa anamasulilidwa molondola.”
Caputala 40 ca buku la Yesaya kucokela mʼmipukutu ya ku Nyanja Yakufa (mipukutuyi inalembedwa kuyambila mu 125 B.C.E. mpaka 100 B.C.E.)
Tikayelekezela ndi mipukutu ya Ciheberi imene inapezeka pambuyo pa zaka 1,000, zimene zikusiyana ndi zinthu zingʼono-zingʼono, maka-maka masipeling’i
Caputala 40 ca buku la Yesaya kucokela mu Aleppo Codex, womwe ndi mpukutu wofunika wa Ciheberi wa Amasorete umene unalembedwa ca mʼma 930 C.E.
Malemba a Ciheberi: Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba a Ciheberi (1953-1960) inamasulilidwa kucokela ku Baibo ya Rudolf Kittel yochedwa Biblia Hebraica. Kucokela nthawiyo, mʼMalemba ena a Ciheberi okonzedwanso monga Biblia Hebraica Stuttgartensia ndi Biblia Hebraica Quinta, aonjezelamo mfundo zina zimene azipeza posacedwapa kucokela mʼmipukutu ya ku Nyanja Yakufa komanso mʼmipukutu ina yakale. Mau amene ali mʼmabukuwa akufanana ndi amene ali mu Leningrad Codex ndipo anaikamonso mau amʼmunsi amene akuonetsa mau amene anasewenzetsa mʼmabuku kapena mʼmipukutu ina ngati Pentatuke wa Cisamariya, mipukutu ya ku Nyanja Yakufa, Baibo ya Cigiriki ya Septuagint, ma Targum a Ciaramu, Baibo ya Cilatini ya Vulgate, ndi Baibo ya Cisiriya la Peshitta. Pamene Baibo ya Dziko Latsopano inali kukonzedwanso, anaona zimene zili mu Biblia Hebraica Stuttgartensia komanso mu Biblia Hebraica Quinta.
Malemba a Cigiriki: Cakumapeto kwa zaka za mʼma 1800, akatswili a Baibo omwe ndi B. F. Westcott komanso F.J.A. Hort, anayelekezela mipukutu ya Baibo komanso zidutswa zimene zinalipo pa nthawiyo. Iwo anacita zimenezi pamene anali kulemba Malemba a Cigiriki omwe anali kuona kuti ndi ofanana kwambili ndi malemba oyambilila. Capakati pa zaka za mʼma 1900, Komiti Yomasulila Baibo ya Dziko Latsopano inasewenzetsa zimene akatswili awiliwa analemba pomasulila Baibo ya Dziko Latsopano. Anasewenzetsanso mipukutu yopangidwa ndi gumbwa yomwe akuganiza kuti ndi ya zaka za mʼma 100 ndi 200 C.E. Kungocokela nthawiyo, pakhala pakupezeka mipukutu yambili yagumbwa. Kuonjezela apo, Malemba ena ngati amene analembedwa ndi Nestle ndi Aland komanso a United Bible Societies, amaonetsa zimene akatswili a Baibo apeza posacedwapa. Zina zimene anapeza pofufuzapo, zagwilitsidwa nchito mʼBaibo ino.
Malinga ndi zimene zili mʼmabuku amenewo, nʼzoonekelatu kuti mavesi ena a mʼMalemba a Cigiriki amene ali mʼma Baibo akale monga King James Version, anacita kuonjezeledwa ndi anthu ena amene anali kukopela malemba ndipo sanali mbali ya Malemba ouzilidwa. Koma popeza kuti kugawa mavesi amene ali mʼma Baibo ambili kunacitika mʼzaka za mʼma 1500, kucotsa mavesi amenewa panopa kwacititsa kuti ma Baibo ambili akhale opanda mau m’mavesi ena. Mavesi ake ndi Mateyo 17:21; 18:11; 23:14; Maliko 7:16; 9:44, 46; 11:26; 15:28; Luka 17:36; 23:17; Yohane 5:4; Macitidwe 8:37; 15:34; 24:7; 28:29; ndi Aroma 16:24. MʼBaibo ino pamavesi amene anacotsedwawo taikapo mau a mʼmunsi.
Ponena za mau omaliza aatali a mu Maliko 16 (vesi 9-20), mau omaliza aafupi a mu Maliko 16, komanso mau amene ali pa Yohane 7:53–8:11, nʼzodziwikilatu kuti mavesiwa mulibe mʼmipukutu yoyambilila. Conco mʼBaibo ino sitinaikemo mau amene anaonjezeledwawo. c
Mau ena asinthidwa kuti agwilizane ndi zimene akatswili a Baibo akuona kuti zikugwilizana ndi zimene zili mʼmipukutu yoyambilila. Mwacitsanzo, malinga ndi zimene mipukutu ina imanena, lemba la Mateyo 7:13 limati: “Lowani pa geti yopanikiza, cifukwa mseu wotakasuka ukupita ku cionongeko, ndipo geti yake ndi yaikulu.” Mu Baibo ya Dziko Latsopano yakale munalibe mau akuti “geti yake.” Koma titafufuza mʼmipukutu, tinapeza umboni wakuti mau akuti “geti yake” analimo mʼmipukutu yoyambilila. Conco mauwa anaikidwa mʼBaibo ino. Pali zinthu zambili zofanana ndi zimenezi zomwe zakonzedwa. Koma zimene zasinthazi ndi zinthu zingʼono-zingʼono ndipo sizikusintha uthenga wopezeka mʼMau a Mulungu.
Mpukutu wagumbwa wa 2 Akorinto 4:13–5:4 umene unalembedwa ca mʼma 200 C.E.
a M’nkhani ino tizingowachula kuti Malemba a Ciheberi.
b Cifukwa cimodzi cimene cinali kucititsa kuti azikopela malemba cinali cakuti mipukutu yoyambilila inapangidwa ndi zinthu zimene zikhoza kuonongeka.
c Kuti mudziwe cifukwa cake tikunena kuti malemba amenewa anacita kuonjezelamo, onani mau a m’munsi mu Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba Opatulika ya Malifalensi, imene inatulutsidwa mu 1984.

