Cinyanja
Mau oyamba a mu Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba Opatulika
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt tsa. 39

Mau oyamba

Malemba Opatulika anauzilidwa ndi Mulungu ndipo analembedwa mu Ciheberi, Ciaramu, komanso mu Cigiriki. Kuti anthu a “mitundu yonse” apindule ndi Mau a Mulungu, Malemba afunika kumasulilidwa m’zinenelo zambili. (Mateyo 24:14) Mabuku 27 kucokela pa Mateyo kufika pa Cibvumbulutso amachedwa “Malemba a Cigiriki a Cikhristu.” Zili conco cifukwa Malembawa analembedwa koyamba m’Cigiriki ndi Akhristu amene anauzilidwa ndi mzimu woyela m’zaka 100 C.E zoyambilila.

Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba a Cigiriki a Cikhristu inatulutsidwa koyamba mu Cingelezi mu 1950. Mipukutu imene inagwilitsidwa nchito kwambili pomasulila Baibo iyi ndi mipukutu ya Westcott ndi Hort Greek, yomwe ndi yodziwika kwambili ndipo imagwilizana kwambili ndi mipukutu yakale ya Cigiriki. Pomasulila Malemba a Cigiriki a Baibo ya Dziko Latsopano, anayesetsa mwakhama kumasulila mokhulupilika. Baibo ino ya Cinyanja yamasulilidwa potengela Baibo ya Dziko Latsopano ya Cingelezi ya mu 2013.

Dzina lapadela la Mulungu lakuti Yehova, likupezeka maulendo 237 m’Baibo ino ya Dziko Latsopano ya Malemba a Cigiriki a Cikhristu. Baibo ino yabwezeletsa dzina la Yehova m’malo ake onse oyenela m’Malemba Opatulika. Zili conco cifukwa ca kufunika kwa kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu ndiponso kufunika kwa aliyense kuti aziitanila pa dzinalo kuti akapulumuke.—Mateyo 6:9; Aroma 10:13.

Dzina lakuti Baibo ya Dziko Latsopano, ndi yozikika pa lonjezo la Mulungu lakuti adzabweletsa dziko latsopano lacilungamo limene lidzapindulila mtundu wonse wa anthu. (2 Petulo 3:13) Amene anamasulila Baibo iyi amakonda Mulungu, amene ndi Mlembi wa Malemba Opatulika. Conco iwo anauona kukhala udindo wapadela kumasulila mau ake ndi zigamulo zake. Ndipo anayesetsa kucita zimenezi molondola. Pemphelo lathu n’lakuti Baibo iyi ithandize awelengi amaganizo abwino amene ali ndi colinga cofuna ‘kudziwa coonadi molondola.’—1 Timoteyo 2:4.