Cinyanja
Kodi Baibo Inalosela Ciani za Mesiya?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt masa. 14-15

FUNSO 6

Kodi Baibo Inalosela Ciani za Mesiya?

ULOSI

“Iwe Betelehemu Efurata, . . . mwa iwe mudzatuluka munthu amene ndidzamusankhe kuti akhale wolamulila mu Isiraeli.”

Mika 5:2

KUKWANILITSIKA KWAKE

“Yesu atabadwa ku Betelehemu wa ku Yudeya m’masiku a Herode mfumu, okhulupilila nyenyezi ocokela Kum’mawa anabwela ku Yerusalemu.”

Mateyo 2:1

ULOSI

“Iwo akugawana zobvala zanga, ndipo akucita maele pa zobvala zanga.”

Salimo 22:18

KUKWANILITSIKA KWAKE

“Asilikaliwo atamukhomelela Yesu pa mtengo, anatenga zobvala zake zakunja n’kuzigawa panai . . . Koma cobvala camkatico cinalibe msoko. Cinali nsalu imodzi kucokela pamwamba mpaka pansi. Conco asilikaliwo anauzana kuti: ‘Tisacing’ambe cobvalaci, m’malomwake tiyeni ticite maele kuti tidziwe amene angacitenge’”

Yohane 19:23, 24

ULOSI

“Amateteza mapfupa onse a munthu wolungamayo. Ndipo palibe pfupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.”

Salimo 34:20

KUKWANILITSIKA KWAKE

“Atafika pa Yesu anapeza kuti wafa kale, conco iwo sanathyole miyendo yake.”

Yohane 19:33

ULOSI

“Iye anabayidwa cifukwa ca zolakwa zathu.”

Yesaya 53:5

KUKWANILITSIKA KWAKE

“Mmodzi wa asilikaliwo analasa Yesu m’nthiti ndi mkondo, ndipo nthawi yomweyo magazi ndi madzi anatuluka.”

Yohane 19:34

ULOSI

“Iwo anandilipila ndalama 30 zasiliva.”

Zekariya 11:12, 13

KUKWANILITSIKA KWAKE

“Pambuyo pake mmodzi wa atumwi 12 aja wochedwa Yudasi Isikariyoti, anapita kwa ansembe aakulu n’kuwafunsa kuti: ‘Mudzandipatsa ciani ndikamupeleka kwa inu?’ Iwo anamulonjeza ndalama 30 za siliva.”

Mateyo 26:14, 15; 27:5