Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 4:1-25

  • Mdyelekezi ayesa Yesu (1-11)

  • Yesu ayamba kulalikila ku Galileya (12-17)

  • Yesu aitana ophunzila ake oyamba (18-22)

  • Yesu alalikila, kuphunzitsa, ndi kucilitsa (23-25)

4  Kenako mzimu unatsogolela Yesu ku cipululu, ndipo kumeneko Mdyelekezi anamuyesa. 2  Atasala kudya kwa masiku 40 usana ndi usiku, anamva njala. 3  Kenako Woyesayo anamuyandikila n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi isanduke mitanda ya mkate.” 4  Koma iye anamuyankha kuti: “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha ai, koma ndi mau alionse ocokela m’kamwa mwa Yehova.’”* 5  Kenako Mdyelekezi anamutengela ku mzinda woyela, ndipo anamukwezeka pamwamba penipeni pa* kacisi 6  ndi kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, dziponyeni pansi, cifukwa Malemba amati: ‘Iye adzalamula angelo ake za inu,’ ndipo ‘Iwo adzakuwakhani m’manja mwao, kuti phazi lanu lisagunde mwala.’” 7  Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amatinso: ‘Usamuyese Yehova* Mulungu wako.’” 8  Mdyelekezi anatengelanso Yesu ku phili lalitali kwambili n’kumuonetsa maufumu onse a padziko ndi ulemelelo wao. 9  Kenako anamuuza kuti: “Zinthu zonsezi ndikupatsani mukagwada pansi ndi kundilambilako kamodzi kokha.” 10  Koma Yesu anamuuza kuti: “Coka Satana! Cifukwa Malemba amati: ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenela kum’lambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’” 11  Pamenepo Mdyelekezi anamusiya, ndipo angelo anabwela ndi kuyamba kum’tumikila. 12  Tsopano Yesu atamva kuti Yohane wamangidwa, anacoka n’kupita ku Galileya. 13  Ndiponso atacoka ku Nazareti anapita kukakhala ku Kaperenao kumbali kwa nyanja, m’madela a Zebuloni komanso Nafitali. 14  Izi zinakwanilitsa mau amene anakambidwa kudzela mwa mneneli Yesaya akuti: 15  “Inu anthu okhala m’dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, m’mbali mwa mseu wopita ku nyanja, kutsidya lina la Yorodano, Galileya wa anthu a mitundu ina, 16  anthu okhala mu mdima anaona kuwala kwakukulu, ndipo anthu okhala m’dela la mthunzi wa imfa, kuunika kunawawalila.” 17  Kucokela nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikila kuti: “Lapani, cifukwa Ufumu wa kumwamba wayandikila.” 18  Iye akuyenda m’mbali mwa Nyanja ya Galileya anaona amuna awili a pacibale, Simoni wochedwa Petulo, ndi Andireya m’bale wake, akuponya ukonde pa nyanja, popeza anali asodzi. 19  Ndiyeno anawauza kuti: “Nditsatileni, ndipo ine ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20  Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde ao n’kumutsatila. 21  Atacoka pamenepo, anaona amuna enanso awili a pacibale, Yakobo mwana wa Zebedayo ndi m’bale wake Yohane. Iwo anali m’bwato pamodzi ndi Zebedayo tate wao akusoka maukonde ao ndipo anawaitana. 22  Nthawi yomweyo anasiya bwatolo ndi atate ao n’kumutsatila. 23  Kenako anazungulila m’cigao conse ca Galileya. Iye anali kuphunzitsa m’masunagoge ao ndi kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu, komanso kucilitsa anthu matenda a mtundu ulionse ndi zofooka zilizonse. 24  Mbili yonena za iye inamveka mu Siriya yense, moti anthu anamubweletsela odwala matenda osiyana-siyana ndi zopweteka zina. Anamubweletselanso ogwidwa ndi ziwanda, akhunyu, komanso ofa ziwalo, ndipo anawacilitsa. 25  Pa cifukwa ici, makamu a anthu ocokela ku Galileya, ku Dekapole,* ku Yerusalemu, ku Yudeya, ndi kutsidya lina la Yorodano anamutsatila.

Mau a m'Munsi

^ Kapena kuti, “pamwamba pa mpanda wa.”
^ Kapena kuti, “ku Cigao ca Mizinda 10.”