Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 6:1-34
6 “Samalani kuti musamacite zabwino* pamaso pa anthu kuti akuoneni, cifukwa mukatelo simudzalandila mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba.
2 Conco pamene mukupeleka mphatso zacifundo,* musamalize lipenga mmene amacitila anthu acinyengo m’masunagoge ndi m’miseu, kuti anthu awatamande. Ndithu ndikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yao yonse.
3 Koma inu mukamapeleka mphatso zacifundo, musalole kuti dzanja lanu lamanzele lidziwe zimene dzanja lanu lamanja likucita,
4 kuti mphatso zanu zacifundo zikhale zamseli. Mukatelo, Atate wanu amene akuona zimene zikucitika kuseliko adzakudalitsani.
5 “Komanso mukamapemphela, musamacite mmene anthu acinyengo amacitila, cifukwa iwo amakonda kupemphela ataimilila m’masunagoge ndi pamphambano za miseu ikulu-ikulu kuti anthu awaone. Ndithu ndikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yao yonse.
6 Koma iwe ukafuna kupemphela, uzilowa m’cipinda cako kwawekha ndipo uzipemphela kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatelo, Atate amene amaona zimene zikucitika kuseliko adzakudalitsa.
7 Popemphela, usamanene mau amodzi ndi amodzi, mmene amacitila anthu amitundu ina, cifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu adzawamvela akaculukitsa mau.
8 Conco musakhale ngati iwo cifukwa Atate wanu amadziwa zimene mukufunikila ngakhale musanam’pemphe n’komwe.
9 “Koma inu muzipemphela motele:
“‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.*
10 Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba cimodzi-modzinso pansi pano.
11 Mutipatse cakudya ca lelo,
12 ndipo mutikhululukile macimo athu* mmenenso ife takhululukila amene anatilakwila.*
13 Ndiponso tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa,* koma mutilanditse* kwa woipayo.’
14 “Pakuti mukamakhululukila anthu zolakwa zao, nayenso Atate wanu wa kumwamba adzakukhululukilani.
15 Koma ngati simukhululukila anthu zolakwa zao, nayenso Atate wanu sadzakukhululukilani zolakwa zanu.
16 “Mukamasala kudya, lekani kuonetsa nkhope zacisoni, monga mmene acinyengo aja amacitila. Pakuti iwo amaipitsa nkhope zao* kuti aonekele kwa anthu kuti akusala kudya. Ndithu ndikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yao yonse.
17 Koma iwe ukamasala kudya, uzidzola mafuta kumutu ndi kusamba kumaso
18 kuti usaonekele kwa anthu kuti ukusala kudya, koma kwa Atate wako yekhayo amene ali kosaoneka. Ukatelo, Atate wako amene akuona zimene zikucitika kuseliko adzakudalitsa.
19 “Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi pamene njenjete ndi nguwe zimaononga, komanso pomwe mbala zimathyola n’kuba.
20 Koma mudziunjikile cuma kumwamba, kumene njenjete ndi nguwe siziononga, komanso kumene mbala sizithyola n’kuba.
21 Pakuti kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko.
22 “Nyale ya thupi ndi diso. Conco, ngati diso lako ndi lolunjika pa cinthu cimodzi,* thupi lako lonse lidzawala.
23 Koma ngati diso lako ndi ladyela,* thupi lako lonse lidzacita mdima. Ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi mdima wandiweyani!
24 “Palibe angakhale kapolo wa ambuye awili, cifukwa adzadana ndi mmodzi n’kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi n’kunyoza winayo. Simungatumikile Mulungu komanso Cuma pa nthawi imodzi.
25 “Pa cifukwa cimeneci ndikukuuzani kuti: Lekani kudela nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya ciani kapena mudzamwa ciani, kapenanso za matupi anu kuti mudzabvala ciani. Kodi moyo si wofunika kuposa cakudya, komanso thupi kuposa cobvala?
26 Yang’anitsitsani mbalame za mumlengalenga. Sizifesa mbeu ai, kapena kukolola, kapenanso kututila m’nkhokwe. Koma Atate wanu wa kumwamba amazidyetsa. Kodi inu sindinu ofunika kwambili kuposa mbalame?
27 Ndani wa inu angatalikitse moyo wake ngakhale pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa?
28 Komanso n’cifukwa ciani mukudela nkhawa za zobvala? Phunzilam’poni kanthu pa mmene maluwa a kuchile amakulila. Sagwila nchito, kapena kupanga nsalu.
29 Koma ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemelelo wake wonse sanabvalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.
30 Tsopano ngati umu ndi mmene Mulungu amabvekela zomela zakuchile, zimene zimangokhalapo lelo mawa n’kuziponya pamoto, kodi iye sadzakubvekani kuposa pamenepo a cikhulupililo cocepa inu?
31 Conco musamade nkhawa kuti, ‘Tidzadya ciani?’ kapena, ‘Tidzamwa ciani?’ kapenanso kuti, ‘Tidzabvala ciani?’
32 Pakuti anthu a mitundu ina akufuna-funa mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wa kumwamba akudziwa kuti mufunikila zinthu zonsezi.
33 “Cotelo pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba ndi cilungamo cake, ndipo zinthu zina zonsezi zidzaonjezedwa kwa inu.
34 Conco musamade nkhawa ndi za mawa, cifukwa mawa lidzakhala ndi nkhawa zake. Zobvuta za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.
Mau a m'Munsi
^ Kucokela ku Cigiriki, “musamacite cilungamo canu.”
^ Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Kapena kuti, “dzina lanu lionedwe kuti ndi lopatulika; lionedwe kuti ndi loyela.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “mutikhululukile nkhongole zathu.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “amene ali nafe nkhongole.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “Ndiponso musatilowetse m’mayeselo.”
^ Kapena kuti, “mutipulumutse.”
^ Kapena kuti, “iwo amaleka kudzisamalila.”
^ Kapena kuti, “diso lako limaona bwino.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “loipa.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “wake ndi mkono umodzi.”

