Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 19:1-30
19 Yesu atatsiliza kulankhula zimenezi, anacoka ku Galileya n’kupita ku madela akumalile kwa Yudeya, ku tsidya lina la Yorodano.
2 Khamu lalikulu la anthu linamutsatila, ndipo iye anawacilitsa kumeneko.
3 Ndiyeno Afarisi anabwela kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka mwamuna kusudzula mkazi wake pa cifukwa ciliconse?”
4 Yesu anayankha kuti: “Kodi simunawelenge kuti amene analenga anthu pa ciyambi anawalenga mwamuna ndi mkazi,
5 n’kunena kuti: ‘Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya atate ake ndi amai ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiliwo adzakhala thupi limodzi’?
6 Conco iwo salinso awili koma thupi limodzi. Cotelo, cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.”
7 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga n’cifukwa ciani Mose analamula kuti mwamuna azipeleka cikalata ca cisudzulo kwa mkazi wake n’kumuleka?”
8 Iye anawauza kuti: “Mose anakulolani kusudzula akazi anu cifukwa ca unkhutukumve wanu. Koma sizinali conco kucokela pa ciyambi.
9 Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosudzula mkazi wake, osati pa cifukwa ca ciwelewele,* n’kukwatila mkazi wina, wacita cigololo.”
10 Ndiyeno ophunzila ake anati: “Ngati umu ndi mmene zilili pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, cili bwino kusakwatila.”
11 Iye anawauza kuti: “Si anthu onse amene angathe kucita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatsoyo.
12 Pakuti ena sakwatila cifukwa anabadwa telo, ndipo ena sakwatila cifukwa anacita kufulidwa. Koma ena anasankha kukhala osakwatila cifukwa ca Ufumu wa kumwamba. Amene angathe kutelo acite zimenezi.”
13 Kenako anthu anamubweletsela ana aang’ono kuti awaike manja ndi kuwapemphelela, koma ophunzila ake anawadzudzula.
14 Komabe Yesu anawauza kuti: “Alekeni anawo abwele kwa ine musawaletse, cifukwa Ufumu wa kumwamba ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.”
15 Ndipo ataika manja ake pa iwo anacoka kumeneko.
16 Tsopano munthu wina anapita kwa iye n’kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi n’ciani cabwino cimene ndiyenela kucita kuti ndikapeze moyo wosatha?”
17 Yesu anamuyankha kuti: “N’cifukwa ciani ukundifunsa za cimene cili cabwino? Pali mmodzi yekhayo wabwino. Koma ngati ufuna kukapeza moyo wosatha, uzitsatila malamulo a Mulungu nthawi zonse.”
18 Iye anamufunsa kuti: “Malamulo ati?” Yesu anati: “Usaphe munthu, usacite cigololo, usabe, usapeleke umboni wonama,
19 uzilemekeza atate ako ndi amai ako, komanso uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”
20 Mnyamatayo anayankha kuti: “Ndakhala ndikutsatila malamulo onsewa, nanga n’cianinso cina cimene ndikupelewela?”
21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ufuna kukhala wangwilo,* pita ukagulitse zinthu zako, ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatelo udzakhala ndi cuma kumwamba. Kenako ubwele udzakhale wotsatila wanga.”
22 Mnyamatayo atamva zimenezi, anacoka ali wacisoni cifukwa anali ndi katundu wambili.
23 Pamenepo Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti cidzakhala cobvuta munthu wolemela kulowa mu Ufumu wa kumwamba.
24 Komanso ndikukuuzani kuti n’capafupi ngamila kulowa pa diso la singano, kusiyana n’kuti munthu wolemela akalowe mu Ufumu wa Mulungu.”
25 Ophunzilawo atamva zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anati: “Ndiye pali amene angadzapulumuke ngati?”
26 Yesu anawayang’anitsitsa n’kuwauza kuti: “Kwa anthu izi n’zosathekadi, koma kwa Mulungu zinthu zonse n’zotheka.”
27 Ndiyeno Petulo poyankha anati: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu zonse n’kukutsatilani, kodi tidzapeza ciani?”
28 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa mpando wake wacifumu waulemelelo, inu amene mwanditsatila mudzakhala pa mipando 12 yacifumu, n’kumaweluza mafuko 12 a Isiraeli.
29 Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, atate, amai, ana, kapena minda cifukwa ca dzina langa, adzalandila zoculuka kuwilikiza maulendo 100, komanso adzapeza moyo wosatha.
30 “Koma ambili amene ndi oyamba adzakhala othela, ndipo othela adzakhala oyamba.

