June

Lolemba, June 1

June

Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.—Sal. 86:5.

Pali madalitso amene timapeza panopa chifukwa cha nsembe ya Khristu. Mwachitsanzo, Yehova amatikhululukira machimo athu chifukwa cha nsembeyi. Ife si oyenera kutikhululukira koma iye amafuna kuchita zimenezo. (Sal. 103:​3, 10-13) Anthu ena amadziona kuti ndi osayenera kukhululukidwa ndi Yehova. Zoona n’zakuti tonsefe si oyenera kukhululukidwa. Mtumwi Paulo anazindikira kuti iye sanali “woyenera kutchedwa mtumwi.” Koma ananenanso kuti: “Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili mmene ndililimu.” (1 Akor. 15:​9, 10) Tikalapa machimo athu Yehova amatikhululukira. Sikuti amachita zimenezo chifukwa chakuti ndife oyenera kukhululukidwa, koma chifukwa chakuti amatikonda. Mukayamba kudziona ngati achabechabe, muzikumbukira kuti Yehova anapereka dipo kuti lithandize anthu ochimwa omwe alapa, osati anthu amene sachimwa.—Luka 5:32; 1 Tim. 1:15. w25.01 26-27 ¶3-4

Munthu wokoma mtima zinthu zimamuyendera bwino, koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.—Miy. 11:17.

Sitingathe kulamulira zimene ena angalankhule kapena kuchita. Koma tingathe kudzilamulira mmene tingachitire zinthu. Ndipotu njira yabwino imakhala kukhululuka. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa timakonda Yehova ndipo iye amafuna kuti tizikhululuka. Nthawi zambiri ngati sitikhululuka, tingachite zinthu mosaganiza bwino komanso zingakhudze thanzi lathu. (Miy. 14:​17, 29, 30) Tikasiya kusunga chakukhosi, timateteza mtima wathu kuti tisamakwiye pochita zinthu ndi ena. Tikatero timakhala kuti tadzichitira chinthu china chabwino kwambiri, chomwe ndi kusiya kuganizira zomwe zachitikazo n’kuyambiranso kusangalala. Kodi mungatani kuti musapitirize kukwiya? Njira imodzi ndi kudzipatsa nthawi yokwanira kuti mtima wanu ukhale m’malo. Munthu amene wavulala akapatsidwa mankhwala pamafunika nthawi yokwanira kuti balalo lipole. Ifenso tingafunike nthawi yokwanira kuti tithe kukhululukira munthu kuchokera pansi pa mtima. (Mlal. 3:3; 1 Pet. 1:22) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhululukira ena. w25.02 16-17 ¶8-11

Chakudya chotafuna ndi cha anthu aakulu mwauzimu.Aheb. 5:14.

Chitsanzo cha mfundo zoyambirira ndi nkhani yokhudza kulapa, chikhulupiriro, ubatizo ndi kuuka kwa akufa. (Aheb. 6:​1, 2) Zimenezi ndi zina mwa mfundo zoyambirira zimene Akhristu amazikhulupirira. N’chifukwa chake mtumwi Petulo anafotokoza mfundo zimenezi pamene ankalalikira gulu limene linasonkhana pa Pentekosite. (Mac. 2:​32-35, 38) Tiyenera kuvomereza mfundo zoyambirira zimenezi kuti tikhale ophunzira a Khristu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anachenjeza kuti munthu aliyense amene amakana chiphunzitso cha kuuka kwa akufa wakana zinthu zonse zimene Akhristu amakhulupirira. (1 Akor. 15:​12-14) Koma sitiyenera kukhala okhutira ndi mfundo zoyambirira zokha za choonadi. Mosiyana ndi mfundo zoyambirira, chakudya chotafuna chimaphatikizapo malamulo a Yehova komanso mfundo zake zimene zimatithandiza kumvetsa maganizo ake. Kuti tipindule ndi chakudya chotafunachi, tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu, kuwaganizira mozama komanso kuwagwiritsira ntchito pa moyo wathu. Tikamachita zimenezi timaphunzira kusankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova. w24.04 5 ¶12-13

Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Chiweruzo.—Mat. 12:41.

Mulungu anakumbutsa Yona kuti anthu a ku Nineve ‘sankadziwa kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika.’ (Yona 1:​1, 2; 3:10; 4:​9-11) Pambuyo pake, Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo chimenechi pophunzitsa anthu zokhudza chilungamo ndi chifundo cha Yehova. Kodi anthu a ku Nineve ‘adzauka pa chiweruzo’ chiti? Yesu anaphunzitsa kuti anthu ena “adzauka kuti aweruzidwe.” (Yoh. 5:29) Iye ankanena za Ulamuliro [Wake] wa Zaka 1,000, pomwe anthu ‘olungama ndi osalungama omwe adzaukitsidwe.’ (Mac. 24:15) Kwa anthu osalungama, kumeneku kudzakhala ‘kuuka kuti aweruzidwe.’ Izi zikutanthauza kuti Yehova ndi Yesu azidzaona ngati anthuwo akumvera komanso kutsatira zimene adzaphunzitsidwe. Mwachitsanzo, ngati anthu ena a ku Nineve adzakane kulambira Yehova, adzaweruzidwa kuti asakhalenso ndi moyo. (Yes. 65:20) Koma anthu onse amene adzasankhe kulambira Yehova mokhulupirika, adzaweruzidwa kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale.—Dan. 12:2. w24.05 5 ¶13-14

Mwana wa munthu anabwera kudzafunafuna ndiponso kudzapulumutsa anthu osochera.—Luka 19:10.

Yesu anasonyeza bwino kuti Atate wake ndi wachifundo. (Yoh. 14:9) Zimene iye ankalankhula komanso kuchita zinasonyeza kuti Yehova, yemwe ndi wokoma mtima, amakonda anthu ndipo amafuna kuwathandiza kuti azimumvera komanso kumutumikira ngakhale kuti ndi ochimwa. Yesu amafuna kuti anthu ochimwa alape n’kuyamba kumutsatira. (Luka 5:​27, 28) Yesu ankadziwa kuti adzapereka moyo wake monga nsembe. Mobwerezabwereza iye anauza otsatira ake kuti adzaperekedwa m’manja mwa adani komanso kupachikidwa pamtengo wozunzikirapo. (Mat. 17:22; 20:​18, 19) Iye ankadziwa kuti nsembe yake idzachotsa machimo a dziko. Yesu anaphunzitsanso kuti akadzapereka moyo wake, ‘adzakokera anthu osiyanasiyana’ kwa iye. (Yoh. 12:32) Anthu ochimwa angasangalatse Yehova ngati amavomereza Yesu kukhala Mbuye wawo komanso kutengera chitsanzo chake. Iwo akamachita zimenezi pamapeto pake ‘adzamasulidwa ku uchimo.’ (Aroma 6:​14, 18, 22; Yoh. 8:32) Choncho mofunitsitsa komanso molimba mtima, Yesu analolera kufa imfa yowawa kuti atipulumutse.—Yoh. 10:​17, 18. w24.08 5 ¶11-12

Choyamba uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.Maliko 13:10.

Taganizirani mmene munamvera mutamva koyamba choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Munaphunzira kuti Atate wanu wakumwamba amakukondani, amafuna kuti mukhale m’banja lake la anthu omwe amamulambira, adzathetsa mavuto ndi zopweteka zonse, mukhoza kukhala ndi chiyembekezo chodzaonananso ndi okondedwa anu omwe anamwalira ndi zinanso zambiri. (Maliko 10:​29, 30; Yoh. 5:​28, 29; Aroma 8:​38, 39; Chiv. 21:​3, 4) Mfundo za choonadi zomwe munaphunzirazi zinakufikani pamtima. (Luka 24:32) Munkakonda kwambiri zimene munkaphunzirazo moti munkafunitsitsa kuuza aliyense. (Yerekezerani ndi Yeremiya 20:9.) Kunena zoona, tikamakonda mfundo za m’Baibulo ndi mtima wonse, timafunitsitsa kuuza aliyense zomwe taphunzira. (Luka 6:45) Timamva ngati ophunzira a Yesu, omwe anati: “Sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Timakonda kwambiri choonadi moti timafunitsitsa kuuza ena za choonadicho mmene tingathere. w24.05 15 ¶5; 16 ¶7

Tumikirani Yehova mokondwera.Sal. 100:2.

Monga anthu a Yehova, timalalikira chifukwa timakonda Atate wathu wakumwamba ndipo timafuna kuthandiza anzathu kuti amudziwe. Koma ena sasangalala akamagwira ntchito yolalikira. Chifukwa chiyani? Ena amakhala ndi manyazi komanso amadzikayikira. Enanso zimawavuta kupita kunyumba za anthu asanaitanidwe. Ena amaopa kuti anthu sakawalandira ndipo enanso amaopa kuti zimene angalankhule zingakhumudwitse anzawo. Abale ndi alongo ambiri zimawavuta kuyamba kulankhula ndi anthu za uthenga wabwino. Kodi inunso nthawi zina simumasangalala ndi ntchito yolalikira? Ngati ndi choncho, musataye mtima. Ngati mumadzikayikira, ndi umboni woti ndinu wodzichepetsa ndipo simumafuna kuti anthu aziganizira kwambiri za inuyo komanso simufuna kukangana ndi ena. Ndipotu palibe amene amafuna kukhumudwitsa ena makamaka pamene akuyesetsa kuwachitira zabwino. Atate wanu wakumwamba amadziwa bwino mavuto omwe mumakumana nawo ndipo amafunitsitsa kukuthandizani.—Yes. 41:13. w24.04 14 ¶1-2

Anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.—Miy. 11:2.

Mukamawerenga Baibulo, muzisankha zolinga zingapo zimene mungazikwaniritse m’malo moyesetsa kuti mugwiritse ntchito nthawi imodzi mfundo zonse zimene mwapeza. Mungayese kuchita izi: Muzilemba zimene mukufuna kusintha ndipo kenako muzisankha chimodzi kapena ziwiri zimene mungayambirire, n’kusiya zinazo kuti mudzazichite pa nthawi ina. Ndiye kodi mungayambe ndi zolinga ziti? Mungayambe ndi cholinga chimene mukuona kuti ndi chosavuta kuchikwaniritsa. Kapena mungayambe ndi zinthu zimene mukuona kuti mukufunika kusintha kwambiri. Mukapeza cholinga chimene mukufuna kuchikwaniritsa muzifufuza m’mabuku athu. Muzipempherera cholinga chanucho ndipo muzipempha Yehova kuti akupatseni “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.” (Afil. 2:13) Kenako muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo. Mukayesetsa kukwaniritsa cholinga chanu choyamba zidzakulimbikitsani kuti muyambenso kusintha zinthu zina. Ndipotu mukakwanitsa kusintha khalidwe linalake, zidzakhalanso zosavuta kuti musinthe zinthu zina. w24.09 6 ¶13-14

Mwasonyeza kuti ndinu oyera mʼmbali zonse pa nkhani imeneyi.—2 Akor. 7:11.

Mwina mumakhumudwa ndi zimene munachita m’mbuyo zomwe zinakhumudwitsa ena. Ndiye kodi n’chiyani chomwe chingakuthandizeni? Muzichita zonse zimene mungathe kuti mukonze zinthu komanso kupepesa mochokera pansi pa mtima. Muzipempha Yehova kuti athandize anthu onse amene anakhudzidwa ndi zimene munachita. Iye angathandize inuyo komanso anthu omwe munawakhumudwitsawo kuti mupirire ndiponso muyambirenso kukhala ndi mtendere. Muziphunzirapo kanthu pa zimene munalakwitsa ndipo muzilola kuti Yehova azikugwiritsani ntchito mmene iyeyo akufunira. Taganizirani chitsanzo cha mneneri Yona. M’malo mopita ku Nineve komwe Mulungu anamutuma, Yona analowera kwina. Yehova anamudzudzula ndipo iye anaphunzirapo kanthu pa zimene analakwitsa. (Yona 1:​1-4, 15-17; 2:​7-10) Yehova sanasiye kumugwiritsa ntchito Yona. Anamupatsanso mwayi woti apite ku Nineve ndipo pa nthawiyi Yona anamvera. Iye sanalole kuti kudzimvera chisoni pa zimene analakwitsa kumulepheretse kuchita zimene Mulungu anamutuma.—Yona 3:​1-3. w24.10 8-9 ¶10-11

Choncho lapani ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwere kuchokera kwa Yehova.—Mac. 3:19.

Yehova akakhululuka machimo athu, sikuti amangowakhwatcha koma amawafafaniza. Ngongole ikakhwatchidwa, anthu amangodula mzere papepala limene panalembedwa ngongoleyo koma zimene zinalembedwazo zimatha kumaonekabe. Koma kufafaniza n’kosiyana kwambiri ndi zimenezi. Kuti timvetse zimenezi tiyenera kukumbukira kuti inki yakale inkapangidwa ndi zinthu zosavuta kufufuta. Munthu ankatha kutenga kansalu konyowa n’kufufuta zimene walemba. Choncho ngongole ikafafanizidwa, sinkaonekanso. Munthu sankatha kuonanso zimene zinalembedwa. Zinkangokhala ngati panalibenso ngongole. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova samangokhwatcha machimo athu, koma amawafafaniza.—Sal. 51:9. w25.02 10 ¶11

Usapse mtima nʼkuchita zoipa.—Sal. 37:8.

Anthu ena akatichitira zopanda chilungamo, timadziwa kuti Yehova akudziwa zoona zake za nkhaniyo. Kudziwa kuti Yehova adzakonza zinthu, kungatithandize kuti tipirire zinthu zopanda chilungamo zimene zatichitikira. Kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova kungatithandize kuti tisapitirize kukhala okwiya. Kukwiya kungachititse kuti tichite zinthu mosaganiza bwino, tisakhale osangalala komanso tingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. N’zoona kuti sitingathe kutsanzira Yesu ndendende. Nthawi zina tingalankhule kapena kuchita zinthu zomwe tingadzanong’oneze nazo bondo. (Yak. 3:2) Ndipo zopanda chilungamo zina zingatipweteke kapena kutidetsa nkhawa kwa moyo wathu wonse. Ngati izi ndi zimene zinakuchitikirani, dziwani kuti Yehova amadziwa mmene mukumvera. Ndipo Yesu, amene anachitiridwanso zopanda chilungamo, amamvetsa mmene mukumvera. (Aheb. 4:​15, 16) Timayamikira kuti Yehova amatipatsanso malangizo amene angatithandize ngati tachitiridwa zopanda chilungamo. w24.11 6 ¶12-13

Zimene Mulungu akufuna kuti muzichita ndi zakuti muzisonyeza chikhulupiriro mwa amene anamutuma.Yoh. 6:29.

Kukhulupirira Yesu n’kofunika kuti munthu “akhale ndi moyo wosatha.” Ndipotu Yesu anali atanenapo zimenezi m’mbuyomo. (Yoh. 3:​16-18, 36; 17:3) Ayuda ambiri sanavomereze mfundo yatsopano yomwe Yesu anaphunzitsa yokhudza ‘zimene Mulungu ankafuna kuti iwo azichita.’ Iwo anamufunsa kuti: “Ndiye inuyo muchita chizindikiro chotani kuti ife tichione nʼkukukhulupirirani?” (Yoh. 6:30) Ayudawo anafotokoza kuti m’nthawi ya Mose makolo awo analandira mana chomwe chinali ngati chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku. (Neh. 9:15; Sal. 78:​24, 25) N’zoonekeratu kuti iwo ankangoganizira zopeza chakudya basi. Sanafunse Yesu kuti awafotokozere zomwe ankatanthauza pomwe anatchula za “chakudya chenicheni chochokera kumwamba” ngati mana, chomwe chikanawathandiza kukhala ndi moyo. (Yoh. 6:32) Iwo ankaganizira kwambiri zimene angapeze moti ananyalanyaza choonadi chimene Yesu ankafuna kuwaphunzitsa. w24.12 5-6 ¶10-11

Amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.—Aheb. 3:4.

Mwana wanu akamaphunzira sayansi kusukulu akhoza kuzindikira kuti m’chilengedwechi muli malamulo amene amachititsa kuti zinthu zizioneka mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mitengo yambiri imaoneka mofanana. Pamakhala thunthu, nthambi kenako masamba. Kaonekedwe kameneka kamapezekanso m’zinthu zina m’chilengedwe. Koma kodi ndi ndani amene anaika malamulo amene amathandiza kuti zinthu zizioneka zokongola chonchi? Nanga ndi ndani amene anazilenga? Pamene mwana wanu akuganizira mayankho a mafunso amenewa, m’pamenenso amayamba kukhulupirira kwambiri kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. Pa nthawi ina mukhoza kumufunsa kuti, “Ngati Mulungu ndi amene anatilenga, kodi sizingakhale zomveka kuti iye ndi amene ayenera kutipatsa malangizo otithandiza kuti tizisangalala?” Kenako mungamuuze kuti malangizo amenewa amapezeka m’Baibulo. w24.12 16 ¶8

Mbiri yamvekatu kuti pakati panu pakuchitika chiwerewere ndipo chiwerewere chake ndi choti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.—1 Akor. 5:1.

Mouziridwa, mtumwi Paulo analemba kalata ndipo anapereka malangizo oti munthu wochimwa achotsedwe mumpingo. (1 Akor. 5:13) Kodi Akhristu okhulupirika ankayenera kuchita naye bwanji munthuyo? Paulo anawauza kuti ‘asiye kugwirizana’ naye. Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Iye anafotokoza kuti lamulo limeneli linkaphatikizapo kuti “ngakhale kudya naye munthu wotereyu” n’kosayenera. (1 Akor. 5:11) Kudya limodzi ndi munthu kungachititse kuti tiyambe kucheza naye. Apa n’zoonekeratu kuti Paulo ankatanthauza kuti Akhristu sankayenera kucheza ndi munthuyo. Zimenezi zikanateteza anthu mumpingo kuti asasokonezedwe ndi makhalidwe ake oipa. (1 Akor. 5:​5-7) Kuwonjezera pamenepo, kusiya kucheza naye kukanathandiza munthuyo kuzindikira kuti watalikirana kwambiri ndi Yehova komanso kuti achite manyazi n’kulapa. w24.08 15 ¶4-5

Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.—Yoh. 3:16.

Chaka chilichonse, Aisiraeli ankakhala ndi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Pa tsikuli, mkulu wa ansembe ankapereka nsembe za nyama m’malo mwa anthu onse. Komabe nsembe za nyamazo sizinkaphimbiratu machimo popeza kuti nyama n’zotsika poyerekezera ndi anthu. Koma Aisiraeli akalapa n’kupereka nsembe zimene Mulungu ankafunazi, iye ankawakhululukira machimo awo. (Aheb. 10:​1-4) Nsembe zomwe ankaperekazo zinkakumbutsa Aisiraeli kuti iwo ndi ochimwa. Koma Yehova anakonza njira yoti aphimbiretu machimo a anthu. Iye anakonza zoti Mwana wake “aperekedwe nsembe kamodzi kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri.” (Aheb. 9:28) Yesu anapereka “moyo wake dipo kuti awombole anthu ambiri.”—Mat. 20:28. w25.02 4 ¶9-10

Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.Mat. 26:41.

Yesu ananena kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Mat. 26:41b) Ponena zimenezi, iye anasonyeza kuti ankamvetsa kuti anthufe si angwiro. Koma mawu akewanso ndi chenjezo loti tizipewa kudzidalira. Usiku womwewo asananene mawu amenewa, ophunzira ake anali atasonyeza kudzidalira ponena kuti sadzasiya Mbuye wawo. (Mat. 26:35) Iwo anali ndi zolinga zabwino koma sankadziwa kuti sizikanakhala zophweka kuchita zimenezi ngati zinthu zikanavuta kwambiri. Choncho Yesu anawachenjeza powauza zimene zili mulemba lalero. N’zomvetsa chisoni kuti ophunzirawo analephera kukhala maso. Yesu atamangidwa, iwo anachita mantha ndipo anamuthawa. Chifukwa chakuti sanali maso ophunzirawo anachita ndendende zimene ananena kuti sangachite, zomwe ndi kumusiya Yesu.—Mat. 26:56. w24.07 14 ¶1-2

Tinagwirizanitsidwa ndi Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake.—Aroma 5:10.

Adamu ndi Hava anataya mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Atate wawo. Poyamba, Adamu ndi Hava anali m’banja la Mulungu. (Luka 3:38) Koma chifuwa choti sanamvere Yehova, iwo anathamangitsidwa m’banjali, ndipo pa nthawiyi anali asanabereke ana. (Gen. 3:​23, 24; 4:1) Popeza kuti ife ndi anawo, tiyenera kugwirizanitsidwanso ndi Yehova. (Aroma 5:​10, 11) Kunena kwina, tiyenera kukhala pa ubwenzi wabwino ndi iye. Mogwirizana ndi zimene buku lina linanena, mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kugwirizanitsa,” angatanthauze “kupanga munthu amene anali mdani wako kukhala mnzako.” Koma n’zochititsa chidwi kuti Yehova ndi amene anayamba kuchitapo kanthu kuti zimenezi zitheke. Kodi anachita chiyani? Anakonza zoti machimo athu aphimbidwe n’cholinga choti anthu ochimwafe tikhalenso naye pa ubwenzi wabwino. Pochita izi panafunika kusinthanitsa chinthu ndi chinthu china chomwe ndi chofanana nacho. Zimenezi zimathandiza kuti chinthu chimene chatayika kapena kuwonongedwa, chibwezeretsedwe. w25.02 3-4 ¶7-8

Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa nʼkupulumuka.—2 Akor. 7:10.

Paulo ananena kuti ‘kudzudzulidwa ndi anthu ambiri kunali kokwanira kwa munthu,’ yemwe ankachita chiwerewere ndi amayi ake omupeza. (2 Akor. 2:​5-8) M’mawu ena tingati chilangochi chinathandiza munthu ameneyu, yemwe m’buyomo anagona ndi mayi ake omupeza. (1 Akor. 5:1) Kodi chinamuthandiza bwanji? Chinamuthandiza kuti alape. (Aheb. 12:11) Choncho Paulo analangiza mpingowo kuti: “Mukhululukireni ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza” ndipo “mumutsimikizire kuti mumamukonda.” Onani kuti Paulo ankafuna kuti mpingowo uchite zambiri osati kungomulola kuti abwerere m’gulu la Yehova. Paulo ankafuna kuti zolankhula komanso zochita zawo zimutsimikizire munthuyo kuti amukhululukira ndipo amamukonda. Zimenezi zikanasonyeza kuti iwo amulandiranso mumpingo. w24.08 15 ¶4; 16-17 ¶6-8

Munkanyozedwa ndiponso kuzunzidwa pagulu.—Aheb. 10:33.

Mtumwi Paulo analankhula motsimikiza chifukwa ankadziwa zimene zimafunika kuti munthu apirire. Anakumbutsa Akhristu kuti akamapirira mayesero sayenera kudzidalira okha, koma kudalira Yehova. Paulo akanatha kunena molimba mtima kuti: “Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.” (Aheb. 13:6) Panopa abale athu ena akuzunzidwa. Tikhoza kuwathandiza powapempherera, komanso nthawi zina kuwapatsa zimene akufunikira. Komabe Baibulo limanena momveka bwino kuti “onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) Choncho tonsefe tiyenera kukonzekera zimene tingakumane nazo m’tsogolo. Tiyeni tipitirize kukhulupirira Yehova ndipo tisamakayikire kuti adzatithandiza kupirira mayesero alionse omwe tingakumane nawo. Pa nthawi yake, iye adzathetsa mavuto onse omwe atumiki ake akukumana nawo.—2 Ates. 1:​7, 8w24.09 13 ¶17-18

Anthu ambiri a ku Korinto, amene anamva uthenga wabwino, anayamba kukhulupirira nʼkubatizidwa.—Mac. 18:8.

Kodi n’chiyani chinathandiza anthu a ku Korinto kuti abatizidwe? (2 Akorinto 10:​4, 5) Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera womwe ndi wamphamvu, zinawathandiza kuti asinthe kwambiri zinthu pa moyo wawo. (Aheb. 4:12) Anasiya makhalidwe oipa monga kuledzera, kuba komanso kugonana kwa pakati pa amuna ndiponso akazi okhaokha. (1 Akor. 6:​9-11) Onani kuti ngakhale kuti anthu ena a ku Korinto analowerera kwambiri m’makhalidwe oipa, iwo sanaone kuti n’zovuta kuti asinthe n’kukhala Akhristu. Iwo anayesetsa kuchita khama kuti apitirizebe kuyenda panjira yopanikiza yomwe ndi yopita ku moyo wosatha. (Mat. 7:​13, 14) Kodi inunso mukulimbana ndi khalidwe linalake loipa lomwe lingakulepheretseni kubatizidwa? Dziwani kuti simuyenera kugonja. Muzipempha Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera kuti ukuthandizeni kuti musamalakelake zinthu zoipa. w25.03 6 ¶15-17

Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu.—Yak. 1:5.

Yehova amatiuza kuti adzatipatsa nzeru zomwe zingatithandize kudziwa ngati zomwe tikufuna kuchita zingamusangalatse. Iye amapereka nzeru zimenezi “mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” Mukapemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni, muzichita chidwi kuti muone mmene akuyankhira pemphero lanulo. Tiyerekeze kuti muli pa ulendo ndipo mwasochera, ndiye mukufunsa munthu wina wa kuderalo kuti akuthandizeni. Kodi munganyamuke asanakuyankheni? Ayi simungachite zimenezo. Mudzamvetsera mwachidwi akamakufotokozerani mmene mungayendere. Mofanana ndi zimenezi, mukapempha Yehova kuti akupatseni nzeru, muzifufuza malamulo ndi mfundo za m’Baibulo zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyo. Mwachitsanzo, poganizira ngati mungapite kumacheza enaake, mungaganizire zimene Baibulo limanena pa nkhani ya maphwando oipa, kugwirizana ndi anthu oipa komanso kufunika koika zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’malo mwa zofuna zathu.—Mat. 6:33; Aroma 13:13; 1 Akor. 15:33. w25.01 16 ¶6-7

Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala.—Yes. 65:13.

Ulosi wa Yesaya umasonyeza kuti pali kusiyana kwambiri pakati pa anthu omwe ali m’paradaiso wauzimu ndi amene sali m’paradaisoyu. Yehova amapereka mowolowa manja kwa atumiki ake zonse zomwe amafunikira kuti apitirize kukhala naye pa ubwenzi. Amatipatsa mzimu woyera, Mawu ake komanso chakudya chauzimu chochuluka n’cholinga choti ‘tizidya, . . . tizimwa, . . . [komanso] tizisangalala.’ (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 22:17.) Koma anthu omwe amakhala kunja kwa paradaisoyu ‘amakhala ndi njala . . . , amakhala ndi ludzu . . . , [komanso] amachita manyazi.’ Iwo sapeza zinthu zimene zingawathandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. (Amosi 8:11) Yehova amapereka mowolowa manja kwa anthu ake zinthu zimene amafunikira, kuphatikizapo chakudya chauzimu. (Yow. 2:​21-24) Iye amachita zimenezi kudzera m’Baibulo, mabuku ofotokoza Baibulo, webusaiti yathu, misonkhano yampingo, yadera komanso yachigawo. Tingathe kudya chakudya chauzimuchi tsiku lililonse ndipo zotsatira zake n’zakuti timakhala athanzi komanso timatsitsimulidwa. w24.04 21 ¶5-6

Mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima.—Akol. 4:6.

Ngati mukufuna kuyamba chibwenzi ndi munthu, mukhoza kukonza zoti mukakambirane ndi munthuyo kumalo amene kumapezeka anthu ena kapena kungomuimbira foni. Muyenera kumuuza momveka bwino kuti mukumufuna ndipo mungakonde kumudziwa bwino. (1 Akor. 14:9) Ngati ndi koyenera, muzimupatsa munthuyo nthawi yoti aganizire asanayankhe. (Miy. 15:28) Ndipo ngati munthuyo sakufuna kukhala nanu pa chibwenzi, muzilemekeza maganizo ake. Kodi mungatani ngati munthu wina wanena kuti akukufunani? Dziwani kuti munthuyo ayenera kuti anafunika kulimba mtima kuti afotokoze maganizo ake. Choncho muyenera kumuyankha mokoma mtima komanso mwaulemu. Mufotokozereni ngati mukuona kuti mukufunika nthawi kuti mukaganizire nkhaniyo. Koma muziyesetsa kuti mumuyankhe mwamsanga. (Miy. 13:12) Ngati simukufuna, mufotokozereni mokoma mtima komanso momveka bwino. Koma ngati mukufuna kukhala pa chibwenzi ndi munthuyo, muyenera kumufotokozera maganizo anu komanso zimene mukuyembekezera pa chibwenzi chanucho. Zomwe mukuyembekezera zingasiyane ndi za mnzanuyo. w24.05 23-24 ¶12-13

Ndikubwera kudzamenyana nawe mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.—1 Sam. 17:45.

Davide ali wachinyamata anapita kumsasa wa Aisiraeli. Iye anapeza asilikaliwo akuchita mantha chifukwa msilikali wamphamvu wa Afilisiti dzina lake Goliyati ‘ankanyoza asilikali a Isiraeli.’ (1 Sam. 17:​10, 11) Asilikaliwo ankachita mantha chifukwa ankaganizira kwambiri za maonekedwe a munthuyo komanso mawu onyoza omwe ankalankhula. (1 Sam. 17:​24, 25) Koma Davide ankaona zinthu mosiyana. Iye ankaona kuti Goliyati sankangonyoza asilikali a Aisiraeli koma ‘ankanyoza asilikali a Mulungu wamoyo.’ (1 Sam. 17:26) Davide ankaganizira kwambiri za Yehova. Iye ankakhulupirira kuti Mulungu amene anamuthandiza pamene ankaweta ziweto angamuthandizenso pa nthawiyi. Popeza ankakhulupirira kuti Mulungu amuthandiza, anapita kukamenyana ndi Goliyati ndipo anapambana.—1 Sam. 17:​45-51. w24.06 21 ¶7

Usachite mantha, chifukwa ndili ndi iwe. Usade nkhawa chifukwa ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa, ndithu ndikuthandiza, ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.Yes. 41:10.

Tiziganizira mmene moyo wathu ukanakhalira zikanakhala kuti sitikutumikira Yehova. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhalebe okhulupirika n’kunena ngati mmene wolemba masalimo ananenera kuti: “Kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.” (Sal. 73:28) Tingathe kupirira mavuto amene tingakumane nawo m’masiku otsiriza ano chifukwa ‘timatumikira Mulungu wamoyo ndi woona.’ (1 Ates. 1:9) Mulungu wathu amatikonda ndipo nthawi zonse azitithandiza. Iye anathandiza atumiki ake m’mbuyomu ndipo azitithandizanso masiku ano. Posachedwapa tikuyembekezera kuti padzikoli pachitika chisautso chachikulu. Koma sitidzakhala tokhatokha. Choncho tiyeni tonse “tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.’”—Aheb. 13:​5, 6w24.06 25 ¶17-18

Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa.—Mal. 3:18.

Baibulo limatiuza za amuna 40 omwe anakhala mafumu a Isiraeli. Mafumu ena abwino anachitanso zinthu zina zoipa. Chitsanzo ndi Davide yemwe anali mfumu yabwino. Yehova ananena kuti: “Davide mtumiki wanga . . . anasunga malamulo anga, kunditsatira ndi mtima wake wonse ndiponso kuchita zinthu zoyenera zokhazokha pamaso panga.” (1 Maf. 14:8) Komatu munthu ameneyu anachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake ndipo anakonza zoti mwamuna wa mkaziyo aphedwe kunkhondo. (2 Sam. 11:​4, 14, 15) Baibulo limatiuzanso za mafumu ambiri osakhulupirika omwe anachitanso zinthu zina zabwino. Chitsanzo ndi Mfumu Rehobowamu. Kwa Yehova “iye anachita zoipa.” (2 Mbiri 12:14) Koma Rehobowamu anamvera lamulo la Mulungu loti alole kuti ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli ukhale woima paokha. Anachitanso zinthu zothandiza mtundu wake pomanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. (1 Maf. 12:​21-24; 2 Mbiri 11:​5-12) Kodi n’chiyani chinkachititsa Yehova kuona mafumu ena kukhala okhulupirika? N’zosakayikitsa kuti ankayang’ana mtima wawo, kulapa kwawo komanso zimene ankachita popitirizabe kumulambira m’njira yolondola. w24.07 20 ¶1-3

Pitirizani kuwalera powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.—Aef. 6:4.

Kodi akulu angathandize bwanji ana obatizidwa osaposa zaka 18 omwe achita tchimo lalikulu? Bungwe la akulu lidzakonza zoti akulu awiri akumane ndi mwanayo ndi makolo ake ngati ali Akhristu. Akuluwo adzafufuza zimene makolowo achita pothandiza mwanayo kuti alape. Ngati mwanayo ali ndi maganizo abwino ndipo makolowo akumuthandiza, akuluwo akhoza kusankha kuti nkhaniyo ithere pomwepo. Ndipotu Mulungu anapereka kwa makolo udindo wolangiza ana awo mwachikondi. (Deut. 6:​6, 7; Miy. 6:20; 22:6; Aef. 6:​2-4) Nthawi zina akuluwo angamafunse makolowo kuti adziwe ngati mwanayo akuthandizidwa moyenera. Koma bwanji ngati mwanayo sakulapa ndipo akupitiriza kuchita zoipa? Zikatero komiti ya akulu idzakumana ndi mwanayo limodzi ndi makolo ake. w24.08 24 ¶18

Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.Mac. 20:35.

Tonse tikudziwa mmene timasangalalira tikalandira mphatso. Komabe, timasangalala kwambiri tikapatsa ena zinthu. Njira imene Yehova anatilengera imatithandiza kuti tizitha kuwonjezera chimwemwe chathu. Tingawonjezere chimwemwe chathu tikamafunafuna mipata yoti tipereke zinthu kwa ena. Kunena zoona, njira imene Yehova anatilengerayi ndi yabwino kwambiri. (Sal. 139:14) Malemba amatitsimikizira kuti kupatsa kumatithandiza kukhala osangalala, choncho n’zosadabwitsa kuti amafotokozanso kuti Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Iye ndi wopatsa wamkulu komanso amene anayambitsa kupatsa. Mtumwi Paulo ananena kuti chifukwa cha iye, “tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:28) Ndipotu “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro” zimachokera kwa Yehova. (Yak. 1:17) Tonsefe timafuna kukhala osangalala kwambiri chifukwa cha kupatsa. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kutsanzira Yehova pa nkhani yopatsa.—Aef. 5:1. w24.09 26 ¶1-4

Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.—Afil. 3:16.

Pambuyo poona makhalidwe ofunika kuti munthu akhale mkulu, atumiki othandiza ena akhoza kumaona kuti sangakwanitse kukhala mkulu. Koma kumbukirani kuti Yehova komanso gulu lake, sayembekezera kuti muzisonyeza makhalidwewa popanda kulakwitsa chilichonse. (1 Pet. 2:21) Ndipo mzimu wa Yehova, womwe ndi wamphamvu, ndi umene ungakuthandizeni kuti mukhale ndi makhalidwewa. (Afil. 2:13) Kodi pali khalidwe linalake lomwe mukufuna kuti muzilisonyeza kwambiri? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Muziphunzira zambiri zokhudza khalidwelo ndiponso kufunsa akulu ena kuti azikuthandizani. Ngati ndinu mtumiki wothandiza, yesetsani kuti mukhale mkulu. Muzipempha Yehova kuti akuphunzitseni n’cholinga choti muzichita zambiri pomutumikira komanso kutumikira abale ndi alongo anu. (Yes. 64:8) Yehova akudalitseni pamene mukuyesetsa kuti mukhale mkulu. w24.11 25 ¶17-18

Mulungu si wosalungama kuti angaiwale ntchito yanu ndiponso chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake, potumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira.—Aheb. 6:10.

Palibe aliyense amene ayenera kudziona kuti ndi woyenera kuchitiridwa chifundo ndi Yehova ngakhale atakhala kuti wamutumikira kwa zaka zambiri. Ngakhale zili choncho, Yehova amayamikira kukhulupirika kwathu. Iye anapereka Mwana wake ngati mphatso yaulere osati ngati malipiro a zimene timachita pomutumikira. Tikamaganiza kuti ndife oyenera kuchitiridwa chifundo kapenanso kuti ndife oyenera kuganiziridwa mwapadera, zingakhale ngati tikunena kuti Khristu sanafunike kutifera. (Yerekezerani ndi Agalatiya 2:21.) Mtumwi Paulo ankadziwa kuti iye si woyenera kuchitiridwa chifundo ndi Mulungu. Ndiye n’chifukwa chiyani ankachita khama kutumikira Yehova? Ankachita zimenezo pofuna kusonyeza kuti amayamikira kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova, osati chifukwa chakuti ankayenera kuchitiridwa chifundo. (Aef. 3:7) Mofanana ndi Paulo, timapitiriza kutumikira mwakhama pofuna kusonyeza kuyamikira, osati pofuna kusonyeza kuti ndife oyenera kuchitiridwa chifundo. w25.01 27 ¶5-6