Yona 3:1-10

  • Yona anamvera Mulungu nʼkupita ku Nineve (1-4)

  • Anthu a ku Nineve analapa atamva uthenga wa Yona (5-9)

  • Mulungu anaganiza zoti asawononge Nineve (10)

3  Yehova analankhula ndi Yona kachiwiri kuti:+ 2  “Nyamuka, upite kumzinda waukulu wa Nineve,+ ndipo ukalalikire uthenga umene ndikuuze.” 3  Choncho Yona ananyamuka nʼkupita ku Nineve+ pomvera mawu a Yehova.+ Mzinda wa Nineve unali waukulu kwambiri* ndipo mtunda wake unali woyenda masiku atatu. 4  Kenako Yona analowa mumzindawo nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.” 5  Anthu a ku Nineve anakhulupirira Mulungu+ ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli. 6  Uthengawo utafika kwa mfumu ya Nineve, mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu nʼkuvula chovala chake chachifumu. Kenako inavala chiguduli nʼkukhala paphulusa. 7  Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamula anthu kuti alengeze mu Nineve kuti:“Mfumu ndi akuluakulu ake alamula kuti: Munthu aliyense, ngʼombe, nkhosa komanso chiweto chilichonse zisadye chilichonse. Munthu aliyense kapena chiweto zisadye chakudya kapena kumwa madzi. 8  Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo aliyense asiye zinthu zoipa komanso zachiwawa zimene amachita. 9  Ndani angadziwe, mwina Mulungu woona asintha maganizo pa zimene amafuna kuchita ndipo abweza mkwiyo wake woyaka moto, moti satiwononga?” 10  Mulungu woona ataona zimene anachita, kuti anasiya kuchita zoipa,+ anasintha maganizo ake ndipo sanawabweretsere tsoka limene ananena kuti awabweretsera.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mulungu ankauona kuti ndi mzinda waukulu.”