November
Lamlungu, November 1
Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.—Yer. 3:12.
Akulu amayesetsa kutsanzira chifundo cha Yehova akamachita zinthu ndi munthu yemwe wachotsedwa mumpingo. Mwachitsanzo, Yehova sanadikire kuti Aisiraeli alape iye asanachitepo kanthu kuti awathandize. M’malomwake, iye ndi amene anayamba kuchitapo kanthu iwo asanayambe n’komwe kusonyeza kulapa. Yehova anasonyeza chifundo pouza mneneri Hoseya kuti agwirizanenso ndi mkazi wake yemwe anali akuchitabe tchimo lalikulu. (Hos. 3:1; Mal. 3:7) Potsanzira Yehova, akulu amafunitsitsa kuthandiza munthu amene wachita tchimo kuti alape ndipo amachita zonse zomwe angathe kuti zisakhale zovuta kwa munthuyo kubwerera mumpingo. Mufanizo la Yesu la mwana wolowerera, bambo a mwanayo “anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa mwachikondi.” (Luka 15:20) Onani kuti bambowo sanadikire kuti mwanayo apemphe kaye kuti amukhululukire. M’malomwake, mofanana ndi bambo aliyense wachikondi, iwo ndi amene anayamba kuchitapo kanthu. w24.08 28 ¶7-8
Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu ndipo adzamupatsa, chifukwa iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka popanda kupezera aliyense zifukwa.—Yak. 1:5; mawu a m’munsi.
Monga mmene lembali likusonyeza, Yehova saumira nzeru zake. Iye amazipereka kwa anthu mowolowa manja. Ndipo lanenanso kuti Yehova akamapereka nzeru amachita zimenezo “mosatonza” kapena kuti “popanda kupezera aliyense zifukwa.” Iye satichititsa kuti tizidziona ngati osafunika chifukwa chakuti tamupempha kuti atitsogolere. Ndipotu amatilimbikitsa kuti tizimupempha nzeru. (Miy. 2:1-6) Kodi ifenso tingatsanzire Yehova pa nkhani yopatsa ena nzeru? (Sal. 32:8) Anthu a Yehova amakhala ndi mwayi wambiri wophunzitsa ena zimene akudziwa. Mwachitsanzo, timaphunzitsa atsopano mmene angalalikirire. Akulu amathandiza moleza mtima atumiki othandiza komanso abale obatizidwa kuti azisamalira bwino maudindo awo mumpingo. Komanso ena amene ali ndi luso la zomanga amaphunzitsa anzawo kuti azigwira nawo ntchito zomangamanga za gulu lathu. w24.09 28-29 ¶11-12
Timakukondani kwambiri.—1 Ates. 2:8.
Abale, kuti mukhale mkulu, muyenera ‘kukhala wopanda chifukwa chokunenezerani,’ zomwe zikutanthauza kukhala ndi mbiri yabwino mumpingo. (1 Tim. 3:2) Kuwonjezera apo, muyenera kukhalanso ndi mbiri yabwino kwa osakhulupirira. Anthu osakhulupirira akhoza kumanyoza zimene mumakhulupirira koma sayenera kukayikira ngati muli woona mtima kapena wakhalidwe labwino. (Dan. 6:4, 5) Ndiye muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndili ndi mbiri yabwino kwa anthu a mumpingo komanso osakhulupirira?’ Munthu “wokonda zabwino,” amaona zabwino mwa ena komanso kuwayamikira chifukwa cha makhalidwe awo abwino. (Tito 1:8) Amasangalalanso kuchitira ena zabwino, ngakhale zoposa zimene anthu amayembekezera. N’chifukwa chiyani akulu ayenera kukhala ndi khalidwe limeneli? Chifukwa chakuti nthawi zambiri amafunika kuchita maulendo aubusa komanso kusamalira abale ndi alongo awo mumpingo. (1 Pet. 5:1-3) Ngakhale kuti imeneyi ndi ntchito yaikulu, iwo amasangalala kutumikira komanso kuthandiza ena.—Mac. 20:35. w24.11 20 - 21 ¶3-5
Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.—Mac. 20:35.
Atumiki othandiza amagwira ntchito zofunika kwambiri mumpingo. N’zoonekeratu kuti mtumwi Paulo ankayamikira kwambiri amuna okhulupirikawa. Mwachitsanzo, m’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Filipi, iye anapereka moni kwa akulu komanso atumiki othandiza. (Afil. 1:1) Abale ambiri obatizidwa, kaya achikulire kapena achinyamata, amasangalala kwambiri akakhala atumiki othandiza. Mwachitsanzo, Devan anali ndi zaka 18 pamene anakhala mtumiki wothandiza. Pomwe M’bale Luis anakhala mtumiki wothandiza ali ndi zaka za m’ma 50. Pofotokoza mmene anamvera, M’bale Luis ananena kuti: “Ndikaganizira chikondi chimene mpingo umandisonyeza, ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala mtumiki wothandiza.” Umu ndi mmenenso abale ambiri amamvera. Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi mungayesetse kuti mukhale mtumiki wothandiza? w24.11 14 ¶1-3
Yehova, chonde ndikukupemphani kuti mukumbukire kuti . . . ndachita zabwino pamaso panu.—2 Maf. 20:3.
Mfumu Hezekiya ya ku Yuda ili ndi zaka 39 inadwala matenda aakulu. Mneneri Yesaya anamuuza uthenga wochokera kwa Yehova wonena kuti afa ndi matenda akewo. (2 Maf. 20:1) Hezekiya ayenera kuti ankaona kuti palibenso chabwino. Iye atamva uthenga wokhumudwitsawu analira kwambiri ndipo anapemphera kwa Yehova mochonderera. Yehova anakhudzidwa ndi kulira kwa Hezekiya ndipo mokoma mtima anamuuza kuti: “Ndamva pemphero lako ndipo ndaona misozi yako. Ndikuchiritsa.” Kudzera mwa Yesaya, Yehova analonjeza kuti adzatalikitsa moyo wa Hezekiya komanso kupulumutsa Yerusalemu m’manja mwa Asuri. (2 Maf. 20:4-6) Kodi mukuvutika chifukwa cha matenda aakulu omwe mukuona kuti simungachire? Muzipemphera kwa Yehova ngakhale mukugwetsa misozi. Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova yemwe ndi “Bambo wachifundo chachikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,” adzatitonthoza pa mayesero athu onse.—2 Akor. 1:3, 4. w24.12 24 ¶15-17
Ndili ndi chiyembekezo ngati chimenenso anthu awa ali nacho, kuti Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe.—Mac. 24:15.
Zidzakhalatu zosangalatsa kulandira anthu amene adzaukitsidwe. Tidzasangalalanso kuphunzira zambiri zokhudza Yehova kudzera m’zinthu zimene analenga. (Sal. 104:24; Yes. 11:9) Chosangalatsa kwambiri n’chakuti tizidzalambira Yehova popanda kudziimba mlandu chifukwa chakuti talakwitsa zinazake. Kodi mungalolere kutaya zonsezi chifukwa chongofuna ‘kusangalala kwa nthawi yochepa pochita machimo’? (Aheb. 11:25) Simungafune kuchita zimenezo. Tingalolere kutaya chilichonse panopa kuti tidzapeze madalitso amenewa. Kumbukirani kuti zimene tikuyembekezera m’Paradaiso tsiku lina zidzachitikadi. Tizidzatere tili m’Paradaiso. Zimenezi sizikanatheka Yehova akanapanda kutikonda n’kupereka mphatso ya Mwana wake. w25.01 29 ¶12
Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?—Num. 11:23.
Buku la Aheberi limatchula anthu ambiri amene ankakhulupirira Yehova. Mmodzi wa anthuwa ndi Mose. (Aheb. 3:2-5; 11:23-25) Iye ankadalira Mulungu, chifukwa Yehovayo anachita zinthu modabwitsa popereka madzi ndi chakudya kwa anthuwo m’chipululu. (Eks. 15:22-25; Sal. 78:23-25) Ngakhale kuti Mose anali ndi chikhulupiriro cholimba, pa nthawi ina anakayikira zoti Yehova angapereke nyama kwa anthu ake. Patatha pafupifupi chaka kuchokera pamene anatuluka ku Iguputo, Yehova analonjeza anthu ake kuti adzawapatsa nyama. Mose anakayikira ngati Yehova angapereke nyama yokwanira anthu mamiliyoni omwe anali m’chipululu. Poyankha, Yehova anafunsa Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?” (Num. 11:21-23) Apa tingati Yehova ankafunsa Mose kuti, ‘Kodi ukuganiza kuti sindingathe kuchita zomwe ndikunenazi?’ w25.03 26 ¶1-2
Mulungu sanalekerere dziko lakale lija osalipatsa chilango.—2 Pet. 2:5.
Kodi tiziona kuti chilichonse chomwe chinachitika mu nthawi ya Chigumula chinkaimira zinazake? Yankho ndi lakuti ayi. Chifukwa chiyani? Chifukwa palibe Malemba amene amafotokoza zimenezi. N’zoona kuti Yesu anayerekezera masiku a Nowa ndi zochitika za m’masiku otsiriza. Koma sanasonyeze kuti chilichonse chomwe chinachitika mu nthawi ya Nowa, monga kutsekedwa kwa chitseko cha chingalawa, kunali ndi tanthauzo linalake. (Mat. 24:37-39) Kodi Nowa anatani atamva uthenga wochenjeza wa Yehova? Iye anasonyeza chikhulupiriro pokhoma chingalawa. (Aheb. 11:7; 1 Pet. 3:20) Mofanana ndi zimenezi, anthu omwe akumva uthenga wabwino wa Ufumu ayenera kumatsatira zimene akuphunzira. (Mac. 3:17-20) Petulo ananena kuti Nowa “ankalalikira za chilungamo cha Mulungu.” Masiku anonso timagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse. Komabe, ngakhale titayesetsa bwanji, sitingathe kuuza munthu aliyense uthenga wabwino mapeto asanafike. w24.05 9-10 ¶3-5
Amalemekeza anthu amene amaopa Yehova.—Sal. 15:4.
Tiyenera kumapeza njira zosonyezera kukoma mtima komanso ulemu kwa anzake a Yehova. (Aroma 12:10) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Njira imodzi imene yatchulidwa pa Salimo 15:4, ndi yakuti munthu amene ndi mlendo mutenti ya Yehova, “sasintha zimene walonjeza ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.” Kusakwaniritsa zomwe talonjeza kungapweteke anthu ena. (Mat. 5:37) Mwachitsanzo, Yehova amayembekezera kuti anzake azilemekeza lumbiro la ukwati. Amasangalalanso makolo akamakwaniritsa zomwe alonjeza ana awo. Kukonda Mulungu komanso anzathu, kudzatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kukwaniritsa zomwe talonjeza. Njira inanso imene tingasonyezere kuti timalemekeza anzake a Yehova ndi kukhala ochereza komanso opatsa. (Aroma 12:13) Kucheza ndi abale ndi alongo athu kumathandiza kuti tizigwirizana nawo kwambiri komanso tizigwirizana ndi Yehova. Ndipotu tikakhala ochereza, timakhala tikutsanzira Yehova. w24.06 12 ¶15-16
Munthu ndi ndani kuti muzimuganizira.—Sal. 8:4.
Yehova amaulula choonadi chake kwa anthu odzichepetsa. (Mat. 11:25) Ifeyo tinadzichepetsa n’kulola kuti tiphunzitsidwe choonadi. (Mac. 8:30, 31) Koma tiyenera kukhala osamala kuti tisayambe kudzikuza. Kunyada kungatichititse kuona kuti maganizo athu ndi anzeru kuposa mfundo za m’Malemba komanso malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa. Kuti tikhalebe odzichepetsa tiyenera kukumbukira kuti ndife aang’ono kwambiri poyerekezera ndi Yehova. (Sal. 8:3, 4) Tiyeneranso kupemphera kuti tikhale ndi mtima wodzichepetsa komanso wophunzitsika. Yehova adzatithandiza kuti tiziona kuti maganizo ake, omwe timawaphunzira kuchokera m’Baibulo komanso m’gulu lake, ndi ofunika kwambiri kuposa maganizo athu. Mukamawerenga Baibulo, muzipeza umboni wotsimikizira kuti Yehova amakonda anthu odzichepetsa osati onyada kapena odzikuza. Tiyenera kuyesetsa kuti tikhalebe odzichepetsa tikalandira utumiki umene umatichititsa kuti tizionekera kwambiri kwa anthu. w24.07 10 ¶8-9
Wamngʼono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzapangitsa kuti zimenezi zichitike mofulumira pa nthawi yake.—Yes. 60:22.
Kuyambira mu 1919, Yesu wakhala akugwiritsa ntchito kagulu ka abale odzozedwa kuti azitsogolera ntchito yolalikira komanso kupereka chakudya chauzimu kwa otsatira ake. (Luka 12:42) Ndipo zikuonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchito yawo. (Yes. 65:13, 14) Tikanakhala kuti sitichita zinthu mwadongosolo sitikanakwanitsa kugwira ntchito imene Yesu watipatsa. (Mat. 28:19, 20) Mwachitsanzo, zikanakhala kuti kulibe magawo, bwenzi aliyense akulalikira kulikonse kumene akufuna. Magawo ena bwenzi akulalikidwa mobwerezabwereza ndi ofalitsa osiyanasiyana pomwe ena akanangosiyidwa. Kodi mukuganiza kuti kuchita zinthu mwadongosolo kumatithandizanso m’njira ziti? Zimene Yesu ankachita ali padzikoli zinkathandiza otsatira ake kuchita zinthu mwadongosolo ndipo akupitirizabe kuchita zimenezi masiku ano. w24.04 8-9 ¶2-4
Utasintha nʼkumachita zinthu zabwino, kodi sindingayambirenso kusangalala nawe? Koma ngati susintha nʼkumachita zinthu zabwino, uchimo wakubisalira pakhomo, ndipo ukufunitsitsa kukumbwandira.—Gen. 4:7.
Kaini anali mwana woyamba wa Adamu ndi Hava. Iye anatengera uchimo kuchokera kwa makolo akewa. Ponena za iye Baibulo limanenanso kuti: “Zochita zake zinali zoipa.” (1 Yoh. 3:12) Mwina n’chifukwa chake Yehova “sanasangalale ndi Kaini komanso nsembe yake ngakhale pangʼono.” M’malo mosintha zochita zake, “Kaini anapsa mtima kwambiri ndipo nkhope yake inagwa chifukwa cha chisoni.” Ndiye kodi kenako Yehova anachita chiyani? Iye analankhula ndi Kaini. (Gen. 4:3-7) Onani kuti Yehova analankhula ndi Kaini mokoma mtima, anamuuza kuti adzamudalitsa ngati atachita zabwino komanso anamuchenjeza za kuopsa kwa tchimo. N’zomvetsa chisoni kuti Kaini sanamvere. Iye sanalole kuti Yehova amuthandize kuti alape. Koma kodi Kaini atakana kumvera, Yehova anasiya kuthandiza anthu ena ochimwa kuti alape? Ayi sanatero. w24.08 10 ¶8
Musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.—Deut. 30:19.
Aisiraeli anali ndi tsogolo labwino kwambiri. Yehova akanawadalitsa kuti akhale kwa nthawi yaitali m’dziko limene anawalonjeza. Dzikolo linali lokongola kwambiri komanso lachonde. Ponena za dziko limenelo, Mose ananena kuti: “[Ndi] dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yabwino imene simunamange ndinu, yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zosiyanasiyana zabwino zimene simunagwirire ntchito, zitsime zimene simunakumbe ndinu komanso minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale ndinu.” (Deut. 6:10, 11) Mose anachenjezanso Aisiraeli kuti iwo ankafunika kumvera malamulo a Yehova n’cholinga choti apitirizebe kukhala m’dziko lokongolalo. Mose analimbikitsa Aisiraeli kuti ‘asankhe moyo’ pomvera Yehova komanso ‘pokhala okhulupirika kwa iye.’ (Deut. 30:20) Koma Aisiraeli anakana kumvera Yehova. Choncho patapita nthawi, Mulungu analola kuti Asuri komanso pambuyo pake Ababulo awagonjetse n’kupita nawo ku ukapolo.—2 Maf. 17:6-8, 13, 14; 2 Mbiri 36:15-17, 20. w24.11 9 ¶5-6
Palibe munthu amene angabwere kwa ine pokhapokha Atate amene anandituma atamukoka.—Yoh. 6:44.
Anthu ambiri omwe amati ndi Akhristu amaganiza kuti akhoza kupulumutsidwa chifukwa ‘chongokhulupirira [Yesu ]’ komanso kumuona kuti iye ndi mpulumutsi. (Yoh. 6:29) Komatu Ayuda ena omwe poyamba ankakhulupirira Yesu, anasiya kumutsatira. N’chifukwa chiyani anasiya kumutsatira? Anthu ambiri omwe Yesu anawadyetsa, ankangomutsatira kuti apeze zimene akufuna. Iwo ankangosangalala ndi kuchiritsidwa, kudya chakudya chaulere komanso kuphunzitsidwa zinthu zogwirizana ndi maganizo awo. Koma Yesu anasonyeza kuti munthu ayenera kuchita zambiri kuti akhale wophunzira wake. Iye sanabwere padzikoli kuti azidzangopereka zimene anthu akufuna. Iwo ankafunika kuvomera pempho lakuti ‘bwerani kwa ine,’ potsatira zonse zimene ankaphunzitsa.—Yoh. 5:40. w24.12 12 ¶12-13
Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu ngati mmenenso Khristu anakondera mpingo.—Aef. 5:25.
N’chiyani chingathandize mwamuna kuti asiye kuchitira nkhanza mkazi wake? Iye ayenera kuyesetsa kutsanzira Yesu. Kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi ophunzira ake nanga ankawalankhula bwanji? Kodi amuna angaphunzirepo chiyani? Yesu sanagwiritse ntchito mphamvu kuti ophunzira ake azimuopa. M’malomwake, ankawatumikira modzichepetsa. (Yoh. 13:12-17) Iye anauza ophunzira ake kuti: “Lolani kuti ndikuphunzitseni, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28-30) Onani kuti Yesu anali wofatsa. Munthu wofatsa si wofooka, koma amakhala ndi mphamvu zotha kudziletsa. Akaputidwa amakhala wodekha ndipo amadziletsa. w25.01 10 ¶10-11
Zochita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova.—Miy. 16:3.
Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, mavuto a zachuma aziwonjezereka. Zinthu monga mavuto a zandale, nkhondo, ngozi zam’chilengedwe kapena miliri, zingayambitse mavuto azachuma. Zingatiwonongere ndalama, katundu, nyumba kapenanso ntchito ingatithere. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tizidalira Yehova posankha zochita? Chinthu chofunika kwambiri chomwe mungachite ndi kupemphera kwa Yehova. Muzimupempha kuti akuthandizeni kusankha bwino zochita komanso kuti akuthandizeni kuti ‘musamavutike mumtima’ chifukwa cha mavuto anu. (Luka 12:29-31) Muzimupemphanso kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima woyamikira. (1 Tim. 6:7, 8) Muzifufuza m’mabuku athu kuti mudziwe zimene mungachite ngati mwakumana ndi mavuto a zachuma. Anthu ambiri amanena kuti nkhani za pa jw.org zinawathandiza pamene anakumana ndi mavuto a zachuma. w25.03 28-29 ¶10-11
Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti wodetsedwa kapena wonyansa.—Mac. 10:28.
Nthawi ya Yehova inali itakwana yoti anthu a mitundu ina omwe anali osadulidwa akhale mbali ya anthu a Mulungu. Mtumwi Petulo anatumidwa kukalalikira kwa Koneliyo, yemwe anali munthu woyamba mwa anthu a mitundu ina kukhala Mkhristu. Ayuda sankayenderana ndi anthu a mitundu ina, choncho n’zosadabwitsa kuti Petulo anafunika kukonzekeretsedwa bwino kuti achite utumiki umene anapatsidwawu. Petulo atazindikira zimene Mulungu ankafuna pa nkhaniyi anasintha maganizo ake. Zotsatirapo zake n’zakuti, Koneliyo atamupempha kuti apite kunyumba kwake, Petulo anapita ‘mosanyinyirika.’ (Mac. 10:28, 29) Iye analalikira kwa Koneliyo ndi anthu a m’banja lake ndipo iwo anabatizidwa. (Mac 10:21-23, 34, 35, 44-48) Patapita zaka, Petulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti akhale “amaganizo amodzi.” (1 Pet. 3:8) Monga anthu a Yehova, tingakhale ndi maganizo amodzi potsanzira maganizo a Yehova, omwe amafotokozedwa m’Mawu ake Baibulo. w25.03 9-10 ¶7-8
Musasocheretsedwe ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo.—Aheb. 13:9.
Masiku ano pali anthu amene amafalitsa nkhani zabodza zosemphana ndi mfundo zolungama za Yehova. (Miy. 17:15) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tizizindikira komanso kukana mfundo zimene otsutsa amagwiritsa ntchito pofuna kutifooketsa kapenanso kutisocheretsa. Tingachite bwino kutsatira malangizo amene mtumwi Paulo anapereka kwa Akhristu a Chiheberi oti apitirize kukula mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kumaphunzira mozama mfundo za choonadi komanso kumaganiza mmene Yehova amaganizira. Munthu amafunika kupitiriza kuchita zimenezi ngakhale pambuyo poti wadzipereka komanso kubatizidwa. Kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kumawerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. (Sal. 1:2) Kuphunzira patokha kungatithandize kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Khalidwe limeneli ndi lomwe Paulo anatsindika kwambiri m’kalata imene analembera Aheberi.—Aheb. 11:1, 6. w24.09 10 ¶7-8
Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.—Yak. 4:8.
Tikamakhulupirira kuti Yehova alikodi, zingakhale zosavuta kuti tikhale okhulupirika kwa iye. Umu ndi mmenenso zinalili ndi Yosefe. Iye anakanitsitsa kuchita zachiwerewere chifukwa ankadziwa kuti zochita zake zimakhudza Mulungu ndipo sankafuna kumukhumudwitsa. (Gen. 39:9) Kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova tiyenera kumapemphera komanso kuphunzira Mawu ake. Tikamachita zimenezi, ubwenzi wathu ndi iye udzakhala wolimba kwambiri. Choncho mofanana ndi Yosefe, tikakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, sitidzachita chilichonse chomwe chingamukhumudwitse. Munthu akaiwala kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo zimakhala zosavuta kuti asiye kukhala wokhulupirika kwa iye. Chitsanzo ndi zimene anachita Aisiraeli m’chipululu. Iwo ankadziwa kuti Yehova alipo koma anayamba kukayikira ngati iye angawasamaliredi. (Eks. 17:2, 7) Zotsatira zake n’zakuti iwo anasiya kumvera Mulungu. N’zodziwikiratu kuti sitingafune kutengera chitsanzo chawo choipachi.—Aheb. 3:12. w24.06 24 ¶14-15
Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.—Sal. 34:15.
Tili m’masiku omaliza enieni ndipo tikuyembekezera kuti zinthu zomwe zimatichititsa kuti tizilira ziziwonjezeka. Yehova amaona misozi yathu ndipo zimamukhudza tikamalira. Yehova amakumbukira misozi yathu. Choncho tikamakumana ndi zinthu zomwe zikuchititsa kuti tizida nkhawa, tizimuuza mmene tikumvera m’pemphero. Tisamakonde kudzipatula kwa abale ndi alongo anthu mumpingo. Ndipo tizipitiriza kupeza mawu olimbikitsa m’Baibulo. Tisamakayikire kuti tikapitiriza kupirira Yehova adzatidalitsa. Tizikhulupiriranso lonjezo losangalatsa lakuti posachedwapa iye adzapukuta misozi yathu yomwe imabwera chifukwa cha chisoni, kusakhulupirika kwa ena komanso chifukwa cha kuthedwa nzeru. (Chiv. 21:4) Pa nthawiyo, tizidzangogwetsa misozi yobwera chifukwa cha chisangalalo. w24.12 20 ¶3; 25 ¶19
“Inuyo ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.—Yes. 43:12.
Yehova watisankha kuti tikhale Mboni zake ndipo watilonjeza kuti azitithandiza kukhala olimba mtima. (Yes. 43:10, 11) Tiyeni tione njira 4 za mmene amatithandizira. Choyamba, Yesu amakhala nafe tikamalalikira uthenga wabwino. (Mat. 28:18-20) Chachiwiri, Yehova watuma angelo kuti azitithandiza. (Chiv. 14:6) Chachitatu, Yehova watipatsa mzimu woyera womwe umatithandiza kukumbukira zimene tinaphunzira. (Yoh. 14:25, 26) Cha 4, Yehova watipatsa abale ndi alongo omwe timalalikira nawo. Mothandizidwa ndi Yehova komanso abale ndi alongo athu, tili ndi chilichonse chomwe chingatithandize kugwira bwino ntchitoyi. Koma ngati mumagwa ulesi mukakhala kuti simukupeza anthu m’makomo, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi panopa anthu ayenera kuti ali kuti?’ (Mac. 16:13) ‘Kodi ali kuntchito kapena kokagula zinthu?’ Zikatero, n’kutheka kuti mungapeze anthu ambiri polalikira mumsewu. w24.04 17 ¶10-11
Ngati munthu sadziwa kuyangʼanira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?—1 Tim. 3:5.
Ngati muli ndi banja ndipo mukufuna kukhala mkulu, banja lanu liyeneranso kupereka chitsanzo chabwino. Choncho muyenera kukhala “mwamuna woyang’anira bwino banja lake.” Muyenera kukhala ndi mbiri yakuti mumakonda komanso kusamalira bwino banja lanu. Zimenezi zikuphatikizapo kuti muyenera kutsogolera pa zinthu zonse zokhudza kulambira. Ngati ndinu bambo, muyenera kukhala ‘woti ana anu amakumverani ndi mtima wonse.’ (1 Tim. 3:4) Muyenera kuwaphunzitsa mwachikondi. N’zoona kuti mofanana ndi ana onse, iwo azikonda kuseka kapena kusewera. Koma chifukwa chakuti mumawaphunzitsa bwino, iwo angakhale omvera, aulemu ndiponso a khalidwe labwino. Komanso muzichita zimene mungathe pothandiza ana anu kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, azitsatira mfundo za m’Baibulo ndiponso aziyesetsa kuti abatizidwe. w24.11 22 ¶10-11
Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.—Yoh. 15:13.
Tikamachita zambiri potumikira Yehova m’pamenenso timaona kuti akutithandiza kwambiri ndipo timayambanso kumukhulupirira kwambiri. (1 Akor. 3:9) Kumbukirani kuti Yehova amaona zimene zili mumtima mwanu ndipo sayerekezera zimene mumachita ndi zimene ena amachita. Iye amasangalala akamaona kuti mumayamikira mphatso ya dipo kuchokera pansi pa mtima. (1 Sam. 16:7; Maliko 12:41-44) Mphatso ya dipo ndi imene imachititsa kuti tikhululukidwe machimo, tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso tiziyembekezera moyo wosatha. Tiyeni tiziyamikira chikondi cha Yehova yemwe anachititsa kuti tipeze madalitso onsewa. (1 Yoh. 4:19) Tizisonyezanso kuti timayamikira Yesu yemwe anapereka moyo wake chifukwa chotikonda. w25.01 31 ¶16-18
Ndinkavutika tsiku lonse.—Sal. 73:14.
Taganizirani mmene wolemba Salimo 73 anamvera pa nthawi ina. Iye ankaona anthu ena omwe ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino ndipo sankada nkhawa. (Sal. 73:3-5, 12) Akaganizira zimenezo, ankangoona kuti kutumikira Yehova ndi kutaya nthawi. Maganizo amenewa ankachititsa kuti ‘azivutika tsiku lonse.’ (Sal. 73:13, 14) Ndiye kodi iye anatani? Wolemba salimoli anapita pamalo abata kukachisi wa Yehova. (Sal. 73:16-18) Atafika kumeneko anayamba kuganiza bwino. Iye anazindikira kuti ngakhale kuti anthu ena ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino, tsogolo lawo silinali labwino. Ataganizira zimenezi mtima wake unakhala m’malo ndipo anaona kuti anasankha bwino kuti azitumikira Yehova. Zimenezi zinamupatsa mphamvu kuti azipitiriza kutumikira Yehova.—Sal. 73:23-28. w24.10 27 ¶11-12
Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.—Sal. 83:18.
Yehova watisankha kuti tikhale “mboni” zake. (Yes. 43:10-12) Zaka zingapo zapitazo, kalata ina yochokera ku Bungwe Lolamulira inati: “Mwayi waukulu womwe aliyense angakhale nawo ndi wodziwika monga wa Mboni za Yehova.” N’chifukwa chiyani zili choncho? Taganizirani chitsanzo ichi. Ngati mutafuna kuti munthu wina akakhale mboni pa mlandu wanu kukhoti, mumasankha munthu yemwe mukumudziwa komanso kumukhulupirira, yemwe mbiri yake ingachititse kuti umboni wakewo ena aukhulupirire. Choncho potisankha kuti tikhale Mboni zake, zikusonyeza kuti Yehova amatidziwa bwino komanso kutikhulupirira kuti tingauze ena kuti iye yekha ndi amene ali Mulungu woona. Timaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala Mboni zake, ndipo timafuna kugwiritsa ntchito mpata uliwonse pothandiza ena kuti adziwe dzina lake komanso kutsutsa mabodza ambirimbiri omwe amanenedwa okhudza iye. Tikamachita zimenezi, timakhala tikuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu, lakuti Mboni za Yehova.—Aroma 10:13-15. w24.05 18 ¶13
Anachiritsa anthu onse amene ankadwala.—Mat. 8:16.
Yesu ankasangalala kwambiri chifukwa chotumikira anthu ena. Pa nthawi ina , Yesu anaphunzitsa anthu komanso kuwapatsa zofunika pa moyo. Iye anapereka chakudya ndipo anauza ophunzira ake kuti agawe chakudyacho kwa anthuwo. (Maliko 6:41) Pochita zimenezi, anaphunzitsa ophunzira ake kuti azitumikira ena. Iye anasonyeza kuti ntchito ngati zimene amagwira atumiki othandiza ndi zofunika. Atumwiwo ayenera kuti anasangalala kwambiri kugwira ntchito ndi Yesu yopereka chakudya moti mpaka anthuwo “anadya n’kukhuta.” (Maliko 6:42) Aka sikanali koyamba kuti Yesu aike patsogolo zofuna za ena. Pa moyo wake wonse ankatumikira anthu ena. (Mat. 4:23) Yesu ankasangalala kwambiri kuphunzitsa anthu komanso kuwathandiza kupeza zinthu zofunika. w24.11 16 ¶10-11
Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.—2 Tim. 3:1.
Pamene zinthu zikuipiraipira ‘m’masiku otsirizawa,’ mosakayikira tidzafunika kuthandizana ndi abale ndi alongo athu. Tingafunikenso kulimbikitsa abale athu amene akuda nkhawa komanso kuwathandiza kuti ubwenzi wawo ndi Yehova ukhale wolimba. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kuwalandira bwino pa Nyumba ya Ufumu. Choncho abale ndi alongo akafika pa misonkhano, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize kumva kuti amakondedwa komanso ndi otetezeka. Akulu akhoza kukhala malo othawirako kwa abale ndi alongo amene akukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Pakachitika ngozi zachilengedwe, kapena pakafunika thandizo la kuchipatala la mwamsanga, akulu amayesetsa kuti athandize abale ndi alongo. Iwo amawalimbikitsanso ndi mfundo za m’Baibulo. Abale ndi alongo amamasuka kupita kwa mkulu ngati akudziwa kuti iye ndi wofatsa, woganizira ena komanso amamvetsera. Makhalidwe ngati amenewa amathandiza ena kumva kuti amakondedwa ndipo zimakhala zosavuta kuti iwo atsatire malangizo ochokera m’Baibulo amene mkuluyo angapereke.—1 Ates. 2:7, 8, 11. w24.06 29 ¶12-13
Sanaumire ngakhale Mwana wake.—Aroma 8:32.
Tisamaganize kuti popeza Mulungu ndi wamphamvuyonse ndiye kuti samamva kupweteka. Anthufe tinalengedwa m’chifaniziro chake, choncho ngati ifeyo timamva kupweteka, nayenso amamva kupweteka mumtima. Baibulo limafotokoza kuti iye ‘amakhumudwa’ komanso ‘kumva chisoni.’ (Sal. 78:40, 41) Yehova ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri kuona Mwana wake akuzunzidwa ndi anthu oipa mpaka kufa. Dipo limatiphunzitsa kuti Yehova amatikonda kwambiri, moti palibe wachibale kapena mnzathu amene angatikonde choncho. (Aroma 8:32, 38, 39) Sitikayikira kuti Yehova amatikonda kwambiri kuposa mmene timadzikondera tokha. Kodi inuyo mukufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale? Dziwani kuti Yehova ndi amene amafuna kwambiri zimenezo. Kodi mumafuna kuti mukhululukidwe machimo anu? Yehova ndi amene amafuna kwambiri kukukhululukirani. Chomwe amangofuna n’chakuti tiziyamikira mphatso ya dipo, tizimukhulupirira komanso tizimumvera. Kunena zoona, dipo limasonyeza kuti Mulungu amatikonda kwambiri.—Mlal. 3:11. w25.01 22-23 ¶8-9
Nthawi zonse muzitsimikizira kuti chovomerezeka kwa Ambuye nʼchiti.—Aef. 5:10.
Nthawi zina tonsefe timasankha zinthu potengera zimene tikuona kapena kumva. Maso ndi mtima wathu zikhoza kutipusitsa. Tingayambe kunyalanyaza zimene Mulungu amafuna kapena malangizo ake. (Mlal. 11:9; Mat. 24:37-39) Koma tikamayenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro tikhoza kumasankha zinthu zomwe ndi ‘zovomerezeka kwa Ambuye.’ Tikamatsatira malangizo a Mulungu tidzakhala ndi mtendere wamumtima komanso tidzakhala ndi moyo wosangalala. (Sal. 16:8, 9; Yes. 48:17, 18) Ndipo tikapitiriza kuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro tidzapeza moyo wosatha. (2 Akor. 4:18) Kodi tingadziwe bwanji ngati tikuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro kapena zooneka ndi maso? Tiyenera kudzifunsa mafunso awa: Kodi ndimasankha zochita potengera chiyani? Kodi ndimasankha pongotengera zimene ndikuona basi? Kodi ndimadalira Yehova n’kumatsatira malangizo ake posankha zochita? w25.03 20-21 ¶3-4
Muzikhala mwamtendere pakati panu.—1 Ates. 5:13.
Aliyense wa ife ali ndi udindo wothandiza anthu kuti azikopeka ndi paradaiso wauzimu. Kuti tithe kuchita zimenezi, tiyenera kutsanzira Yehova. Iye sakakamiza anthu kuti alowe m’paradaisoyu, m’malomwake ‘amawakoka’ mwachikondi. (Yoh. 6:44; Yer. 31:3) Anthu a mitima yabwino omwe aphunzira za Yehova komanso makhalidwe ake abwino amayamba kukhala naye pa ubwenzi. Kodi tingatani kuti makhalidwe athu abwino azikopa ena kuti alowe m’paradaiso wauzimu? Njira imodzi ndi kukonda komanso kukomera mtima Akhristu anzathu. Anthu atsopano akafika pamisonkhano ya mpingo timafuna kuti azimva ngati mmene anamvera osakhulupirira omwe ayenera kuti anafika pamisonkhano ku Korinto. Iwo anati: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.” (1 Akor. 14:24, 25; Zek. 8:23) Choncho tiyenera kupitiriza kutsatira malangizo amulemba la lero. w24.04 23-24 ¶16-17

