Ekisodo 39:1-43

39  Ndiyeno anapanga zovala+ zosokedwa bwino zoti azivala potumikira m’malo oyera,+ pogwiritsa ntchito ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri.+ Motero anapanga zovala zopatulika+ za Aroni, monga mmene Yehova analamulira Mose.  Kenako anapanga efodi*+ wagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.  Ndiyeno anasula golide kukhala wopyapyala kwambiri, ndipo anam’lenzalenza kukhala ngati tizingwe kuti apetere limodzi ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wabwino kwambiri.+  Anapanganso nsalu za m’mapewa zolumikiza ku efodiyo. Anazilumikiza pamapewa.  Lamba womangira efodi, wolumikiza ku efodiyo anali wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Anali wagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.  Ndiyeno anakonza miyala ya onekisi+ ndi kuiika m’zoikamo zagolide. Pamiyalayo analembapo mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo.+  Ndipo miyalayo anailowetsa pansalu za m’mapewa za efodi kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana a Isiraeli, monga mmene Yehova analamulira Mose.  Kenako anapanga chovala pachifuwa+ ndipo anachipanga mwaluso mofanana ndi efodi. Chinali chagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+  Akachipinda pakati chinali chofanana mbali zonse zinayi. Chovala pachifuwacho anachipanga kuti akachipinda pakati, m’litali mwake chizikhala chikhatho* chimodzi ndipo m’lifupi mwake chikhatho chimodzi.+ 10  Ndiyeno pachovala pachifuwacho anaikapo mizere inayi ya miyala. Mzere woyamba unali ndi miyala ya rube, topazi ndi emarodi.+ 11  Mzere wachiwiri+ unali ndi miyala ya nofeki, safiro+ ndi yasipi.+ 12  Mzere wachitatu+ unali ndi miyala ya lesemu, sibu ndi ametusito. 13  Ndipo mzere wa chinayi+ unali ndi miyala ya kulusolito, onekisi+ ndi yade. Anaiika m’zoikamo zake zagolide. 14  Miyalayo anaiika malinga ndi mayina a mafuko a ana a Isiraeli, ndipo inalipo 12, malinga ndi mayina awo. Mwala uliwonse analembapo mochita kugoba limodzi mwa mayina a mafuko 12, ngati mmene amagobera chidindo.+ 15  Ndipo pachovala pachifuwa anapangapo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota mwaluso.+ 16  Anapanganso zoikamo miyala ziwiri zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anaika mphete ziwirizo m’makona awiri a chovala pachifuwacho.+ 17  Kenako anapisa zingwe ziwiri zagolide zija m’mphete ziwiri za m’makona a chovala pachifuwa.+ 18  Ndipo anamangirira zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri. Kenako anaika zoikamo miyala ziwirizo pansalu za m’mapewa za efodi, chapatsogolo pake.+ 19  Atatero anapanga mphete ziwiri zagolide ndi kuziika m’makona awiri a chovala pachifuwa, kumbali yopindira mkati yokhudzana ndi efodi.+ 20  Ndiyeno anapanga mphete ziwiri zagolide ndi kuziika pansalu ziwiri za pamapewa za efodi m’munsi mwake, kutsogolo kwa nsaluzo, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa lamba wa efodi.+ 21  Atatero anamanga chovala pachifuwacho ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chinalowa m’mphete za chovala pachifuwa ndi mphete za efodi, kuti chovala pachifuwacho chizikhala pamwamba pa lamba wa efodi, kutinso chisasunthe pa efodipo, monga mmene Yehova analamulira Mose.+ 22  Ndiyeno anapanga malaya odula manja+ ovala mkati mwa efodi, a nsalu yowomba ndi ulusi wabuluu wokhawokha. 23  Ndipo malaya odula manjawo anali otsegula pamwamba pake, pakatikati, ngati chovala cha kunkhondo chamamba achitsulo. Potsegulapo panali popenderera m’mphepete mwake kuti pasang’ambike.+ 24  Mumpendero wake wa m’munsi anapangamo makangaza a ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri, wopota pamodzi.+ 25  Kenako anapanganso mabelu agolide woyenga bwino ndi kuwaika pakati pa makangaza,+ kuzungulira mpendero wa m’munsi wa malaya odula manjawo, pakati pa makangaza. 26  Anaika belu ndi khangaza,* belu ndi khangaza, kuzungulira mpendero wa m’munsi mwa malaya odula manja.+ Malayawo ndi oti azivala potumikira, monga mmene Yehova analamulira Mose. 27  Kenako anawomba mikanjo ya Aroni ndi ana ake ya ulusi wabwino kwambiri.+ 28  Ndiyeno anapanga nduwira+ ya nsalu yabwino kwambiri, mipango yokongola yokulunga kumutu+ ya nsalu zabwino kwambiri ndi makabudula a nsalu+ za ulusi wopota wabwino kwambiri. 29  Anawombanso lamba wa pamimba+ ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri, monga mmene Yehova analamulira Mose. 30  Atatero anapanga kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka. Analembapo mawu akuti: “Chiyero n’cha Yehova.”+ Mawuwa anawalemba mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo. 31  Ndiyeno analowetsa chingwe chabuluu m’kachitsuloko kuti akamangirire panduwirayo,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 32  Chotero ntchito yonse ya chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako, inatha, chifukwa ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose.+ Anachitadi momwemo. 33  Pamenepo anabweretsa kwa Mose chihema chopatulika+ ndi zipangizo zake zonse,+ nsalu yake yophimba pamwamba,+ ngowe zake,+ mafelemu ake,+ mitengo yake yonyamulira,+ mizati yake ndi zitsulo zamphako zoika pansi.+ 34  Anabweretsanso chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto+ wofiira, chophimba chinanso cha pamwamba pake cha chikopa cha akatumbu,+ nsalu yotchinga,+ 35  likasa+ la umboni, mitengo yake yonyamulira,+ chivundikiro chake,+ 36  tebulo,+ ziwiya zake zonse+ ndi mkate wachionetsero. 37  Anabweretsanso choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino, nyale zake zondandalikidwa bwino,+ ziwiya zonse za choikapo nyalecho,+ mafuta a nyale,+ 38  guwa lansembe+ lagolide, mafuta odzozera,+ zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga+ pakhomo la chihemacho, 39  guwa lansembe+ lamkuwa, sefa wake wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana,+ mitengo yake yonyamulira,+ ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo,+ beseni losambira+ ndi choikapo chake.+ 40  Anabweretsanso nsalu zotchingira+ bwalo, mizati+ ndi zitsulo zokhazikapo mizatiyo,+ nsalu yotchinga+ pachipata cha bwalo, zikhomo za bwalo+ ndi zingwe zogwira mpanda,+ ziwiya zonse+ zogwiritsa ntchito pa utumiki wa pachihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako, 41  zovala+ zosokedwa bwino zoti azivala potumikira m’malo opatulika, zovala zopatulika+ za Aroni wansembe ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.+ 42  Ana a Isiraeli anachita utumiki wonse motsatira zonse zimene Yehova analamulira Mose.+ 43  Ndipo Mose ataona ntchito yonse, anaona kuti achita zonse monga mmene Yehova analamulira. Iwo anachitadi momwemo. Pamenepo Mose anawadalitsa.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:16.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:33.