Ekisodo 37:1-29
37 Tsopano Bezaleli+ anapanga Likasa+ la mtengo wa mthethe, mikono iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi, ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.+
2 Kenako analikuta ndi golide woyenga bwino mkati ndi kunja komwe, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+
3 Ndiyeno analipangira mphete zinayi zagolide zoika pamwamba pa miyendo yake inayi. Mphete ziwiri zinali mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zinali mbali inayo.+
4 Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo anaikuta ndi golide.+
5 Mitengo yonyamulirayo anailowetsa m’mphete zam’mbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo.+
6 Kenako anapanga chivundikiro+ chagolide woyenga bwino, mikono iwiri ndi hafu m’litali, ndi mkono umodzi ndi hafu m’lifupi.+
7 Anapanganso akerubi awiri agolide. Anali osula ndipo anawapanga kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+
8 Kerubi mmodzi anali kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina kumbali inayo. Akerubiwo anawapanga kumbali zonse ziwiri za chivundikirocho.+
9 Mapiko a akerubiwo anali okweza m’mwamba ndi otambasula.+ Iwo anaphimba chivundikirocho ndi mapiko awo, ndipo anakhala moyang’anizana, koma nkhope zawo zinayang’ana pachivundikirocho.+
10 Ndiyeno anapanga tebulo la mtengo wa mthethe,+ mikono iwiri m’litali, mkono umodzi m’lifupi ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.+
11 Analikuta ndi golide woyenga bwino, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.+
12 Analipangiranso felemu, muyezo wake chikhatho* chimodzi m’lifupi mwake. Felemuli linazungulira tebulo lonse ndipo anapanga mkombero wagolide pafelemulo.+
13 Kuwonjezera pamenepo, analipangira mphete zinayi zagolide ndi kuziika m’makona ake anayi, mmene munali miyendo yake inayi.+
14 Mphetezo zinali pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa mitengo yonyamulira tebulolo.+
15 Ndiyeno anapanga mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide. Mitengo imeneyi inali yonyamulira tebulolo.+
16 Atatero anapanga ziwiya za patebulolo, mbale zake, zikho zake, mitsuko yake ndi mbale zake zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Anazipanga ndi golide woyenga bwino.+
17 Kenako anapanga choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino. Chimenechi chinali chosula. Choikapo nyalechi chinali ndi nthambi m’mbali mwake, ndiponso chinali ndi masamba ofunga duwa, mfundo ndi maluwa.+
18 Choikapo nyalechi chinali ndi nthambi 6. Kumbali ina kunatuluka nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kunatulukanso nthambi zitatu.+
19 Pamalo atatu a nthambi za mbali imodzi, panali masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa. Pamalo atatu a nthambi za mbali inayo, panalinso masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyalecho zinali zotero.+
20 Ndipo pamalo anayi a choikapo nyalecho panali masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa.+
21 Mfundo imodzi inali pansi pa nthambi zake ziwiri, mfundo ina inalinso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mfundo inanso inali pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zinali choncho ndi nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyale.+
22 Choikapo nyalecho chinali ndi mfundo ndi nthambi. Chonsechi chinali chiwiya chimodzi chosula, chagolide woyenga bwino.+
23 Ndiyeno anachipangira nyale 7, zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino.+
24 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi anazipanga pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente limodzi.*
25 Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe.+ M’litali mwake linali mkono umodzi, m’lifupi mwake mkono umodzi. Mbali zake zonse zinayi zinali zofanana, ndipo msinkhu wake unali mikono iwiri. Guwalo linali ndi nyanga pamwamba pake.+
26 Ndiyeno analikuta ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi m’mbali mwake kuzungulira guwalo, komanso nyanga zake. Analipangira mkombero wagolide wozungulira guwa lonselo.+
27 Kumbali ziwiri za guwalo anapangako mphete zagolide, ziwiri kumbali iyi ndi zinanso ziwiri kumbali inayo. Anazipanga m’munsi mwa mkombero kuti muzilowa mitengo yonyamulira guwalo.+
28 Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo anaikuta ndi golide.+
29 Kuwonjezera pamenepo, anapanganso mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika,+ ndi mafuta onunkhira+ osakaniza mwaluso.
Mawu a M'munsi
^ “Talente limodzi” linali kulemera makilogalamu pafupifupi 34.2.