Ekisodo 22:1-31
22 “Munthu akaba ng’ombe kapena nkhosa, n’kuipha kapena kuigulitsa, azilipira ng’ombe zisanu pa ng’ombe imodzi imene waba, ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi imene waba.+
2 (“Wakuba+ akapezeka akuthyola nyumba kuti abe+ ndipo akakanthidwa n’kufa, amene wamuphayo alibe mlandu wa magazi.+
3 Ngati dzuwa linali litatuluka, amene wamuphayo ali ndi mlandu wa magazi.)
“Wakuba azilipira ndithu. Ngati alibe kalikonse, pamenepo azigulitsidwa kuti alipire zinthu zimene anabazo.+
4 Ngati zimene anabazo zapezeka ndi iyeyo zili zamoyo, kaya ndi ng’ombe, bulu kapena nkhosa, azilipira zowirikiza kawiri.
5 “Munthu akalekerera ziweto zake kukadya m’munda wa mpesa kapena wa mbewu zina, kapena watumiza nyama zake zonyamula katundu kukadya m’munda wa munthu wina, azilipira+ popereka zokolola zabwino koposa za m’munda wake wa mpesa kapena za m’munda wake wa mbewu zina.
6 “Moto ukabuka n’kugwirira zomera zaminga, ndipo wafalikira m’munda n’kutentha mitolo yambewu, mbewu zosadula kapena munda wonse,+ amene anayatsa motowo azilipira ndithu chifukwa cha zotenthedwazo.
7 “Munthu akapatsa mnzake ndalama kapena katundu wina kuti amusungire,+ zinthuzo n’kubedwa m’nyumba ya mnzakeyo, wakubayo akapezeka azilipira zowirikiza kawiri.+
8 Ngati wakubayo sanapezeke, azibweretsa mwininyumbayo pafupi ndi Mulungu woona*+ pofuna kuona ngati iyeyo sanatenge katundu wa mnzakeyo.
9 Koma pa milandu iliyonse+ yokhudza ng’ombe, bulu, nkhosa, chovala, kapena chilichonse chimene chinasowa chimene angachiloze kuti, ‘Ichi n’changa!’ awiri onsewo mlandu wawo uzifika pamaso pa Mulungu woona.+ Amene Mulungu adzamuweruze kuti ndiye woipa, azilipira mnzake zowirikiza kawiri.+
10 “Munthu akapatsa mnzake bulu, ng’ombe, nkhosa kapena chiweto chilichonse kuti amusungire, ndipo chafa, chalumala kapena chabedwa popanda woona zimene zachitika,
11 iye alumbire+ kwa mnzake pamaso pa Yehova kuti si iye amene wachita zimenezo pa katundu wa mnzake.+ Mwini wa katunduyo azivomereza lumbirolo ndipo mnzakeyo asalipire.
12 Koma ngati anachita kum’bera,* azilipira kwa mwini wa katunduyo.+
13 Ngati nyamayo inaphedwa ndi chilombo,+ azibweretsa nyama yakufayo monga umboni.+ Asalipire pa nyama iliyonse yophedwa ndi chilombo.
14 “Koma ngati munthu wabwereka chiweto kwa mnzake+ ndipo chalumala kapena chafa mwiniwake palibe, wobwerekayo azilipira ndithu.+
15 Ngati mwiniwake alipo, wobwerekayo asalipire. Ngati anafunika kupereka ndalama kuti abwereke, adzangopereka ndalama yobwerekera chiwetocho.
16 “Mwamuna akanyengerera namwali wosalonjezedwa kukwatiwa n’kugona naye,+ azim’tenga ndithu kukhala mkazi wake atapereka chiwongo.*+
17 Bambo a namwaliyo akakaniratu kum’patsa mwana wawo, iye aziperekabe chiwongo chimene amaperekera namwali.+
18 “Mkazi wamatsenga musam’lole kukhala ndi moyo.+
19 “Aliyense wogonana ndi nyama aziphedwa ndithu.+
20 “Wopereka nsembe kwa milungu ina osati kwa Yehova yekha aziphedwa ndithu.+
21 “Musachitire nkhanza mlendo wokhala pakati panu kapena kum’pondereza,+ chifukwa anthu inu munalinso alendo m’dziko la Iguputo.+
22 “Anthu inu musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye* aliyense.+
23 Mukamuzunza ngakhale pang’ono, iye n’kundilirira, ndidzamva ndithu kulira kwake.+
24 Pamenepo mkwiyo wanga udzakuyakirani,+ ndipo ndidzakuphani ndithu ndi lupanga, kuti akazi anu akhale akazi amasiye ndiponso ana anu akhale ana amasiye.+
25 “Ukabwereketsa ndalama kwa anthu anga, kwa munthu wovutika amene ali pafupi ndi iwe,+ usakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira* kwa iye. Usafunepo chiwongoladzanja.+
26 “Mnzako ukamulanda chovala chake monga chikole,+ uzim’bwezera dzuwa likamalowa.
27 Pakuti chofunda chake n’chomwecho.+ Imeneyo ndi nsalu yake yakunja. Adzafunda chiyani pogona? Ndiyeno akandilirira, ine ndidzamumvera ndithu, chifukwa ndine wachifundo.+
28 “Usatemberere Mulungu+ kapena kutemberera mtsogoleri amene ali pakati pa anthu ako.+
29 “Popereka zokolola zako zambirizo komanso zotuluka moponderamo mphesa ndi moyengeramo mafuta zochulukazo, usapereke monyinyirika.+ Mwana wako wamwamuna woyamba kubadwa uzim’pereka kwa ine.+
30 Zimene uzichita ndi mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe ndi wa nkhosa yako ndi izi:+ Azikhala ndi mayi wake masiku 7.+ Pa tsiku la 8 uzim’pereka kwa ine.
31 “Inuyo muzikhala anthu oyera pamaso panga+ ndipo musadye nyama imene yaphedwa ndi chilombo kuthengo.+ Imeneyo muziponyera agalu.+
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza kuti, kupita naye kwa oweruza oimira Mulungu woona.
^ Mwina chifukwa cha kusasamala kapena chifukwa cha zochitika zina zimene akanatha kuzipewa.
^ “Chiwongo” ndi ndalama zimene mwamuna amalipira pokwatira. Ena amati “chimalo.”
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
^ “Ngongole yakatapira” ndi ngongole imene munthu pobweza amayenera kuwonjezerapo ndalama zina zochuluka. Ena amati “kalowa.”