Ekisodo 26:1-37

26  “Ndiyeno upange chihema chopatulika ndi nsalu 10 zopangira hema.+ Nsaluzo zikhale zaulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ ndi ulusi wofiira kwambiri. Pansaluzo upetepo akerubi.+  M’litali mwake, nsalu iliyonse ikhale mikono 28, ndipo m’lifupi mwake ikhale mikono inayi. Nsalu zonse muyezo wake ukhale wofanana.+  Nsalu zisanu zikhale zolumikizana, ndipo zina zisanu zikhalenso zolumikizana.+  Ndipo uike zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe kumapeto kwa nsalu imodzi mwa nsalu zolumikizanazo. Uchitenso chimodzimodzi kumapeto kwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi.+  Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe kumapeto kwa nsalu imene ili polumikizirana nsalu ziwirizo. Zingwezo zikhale moyang’anizana.+  Upangenso ngowe 50 zagolide ndi kulumikiza nsalu za chihema chopatulika zija ndi ngowezo kuti nsaluzo zikhale chinsalu chimodzi cha chihema.+  “Upange nsalu za ubweya wa mbuzi+ zoyala pachihema chopatulika. Upange nsalu 11.  M’litali nsalu iliyonse ikhale mikono 30,+ ndipo m’lifupi nsalu iliyonse ikhale mikono inayi. Nsalu zonse 11 zija muyezo wake ukhale wofanana.  Ulumikize nsalu zisanu pazokha, kenako ulumikizenso nsalu 6 pazokha,+ ndipo upinde pakati nsalu ya 6 ya koyambirira kwa nsalu zolumikizanazo. 10  Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu yakumapeto kwenikweni kwa nsalu za chihema zolumikizanazo. Uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe kumapeto kwa nsalu zina zolumikizana, pomwe magulu awiri a nsalu zolumikizanalumikizanazo adzakumane. 11  Ndiyeno upange ngowe 50 zamkuwa+ ndi kuzilowetsa m’zingwe zopota zokolekamo ngowezo, n’kulumikiza nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi cha chihema.+ 12  Ndipo nsalu yotsala ya chinsalucho itsike mpaka m’munsi. Hafu yake yotsala ilendewere mpaka m’munsi, kumbuyo kwa chihema chopatulika. 13  Ndipo m’litali mwa chinsalu chija, mkono umodzi kumbali iyi ndi mkono umodzinso kumbali inayo, zikhale zolendewera mpaka m’munsi m’mbali mwa chihema chopatulika, kuphimba chihemacho mbali iyi ndi mbali inayo. 14  “Ndiyeno upange chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi chophimba chinanso pamwamba pake cha zikopa za akatumbu. 15  “Upange mafelemu oimika+ a chihema chopatulika a matabwa a mthethe. 16  M’litali mwake, felemu lililonse likhale mikono 10, ndipo m’lifupi mwake felemu lililonse likhale mkono umodzi ndi hafu. 17  Felemu lililonse likhale ndi mano awiri oyandikana. Mafelemu onse a chihema chopatulika uwapange motero. 18  Upange mafelemu 20 a chihema chopatulika omangira mbali ya kum’mwera ya chihemacho, yoyang’ana ku Negebu. 19  “Upange zitsulo 40 zasiliva zamphako+ zokhazikapo mafelemu 20 aja. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri pansi pa felemu lina la mano awiri. 20  Kumbali inayo ya chihema chopatulika, chakumpoto, kukhale mafelemu 20,+ 21  ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri pansi pa felemu lina la mano awiri.+ 22  Ndipo kumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo, upangireko mafelemu 6.+ 23  Ndiyeno upange mafelemu awiri kuti akhale ochirikiza m’makona akumbuyo a chihema chopatulika.+ 24  Lililonse la mafelemu amenewa likhale ndi matabwa awiri ofanana kuyambira pansi mpaka pamwamba. Matabwawo alumikizane pamphete yoyamba. Mafelemu awiriwo apangidwe mofanana ndipo akhale ochirikiza m’makona. 25  Pakhale mafelemu 8 ndi zitsulo zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo 16 zokhazikapo mafelemu, ziwiri zikhale pansi pa felemu limodzi la mano awiri, zinanso ziwiri pansi pa felemu lina la mano awiri. 26  “Upangenso mipiringidzo ya mtengo wa mthethe,+ mipiringidzo isanu yogwira mafelemu a mbali imodzi ya chihema chopatulika. 27  Mipiringidzo isanu yogwira mafelemu a mbali ina ya chihema chopatulika, mipiringidzo inanso isanu yogwira mafelemu akumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo.+ 28  Mpiringidzo wapakati ugwire mafelemu onse kuyambira kumapeto mpaka kumapeto. 29  “Ukute mafelemuwo ndi golide,+ ndipo mphete zake, zolowetsamo mipiringidzo, uzipange ndi golide. Mipiringidzoyo uikute ndi golide. 30  Umange chihema chopatulikacho motsatira pulani imene ndakuonetsa m’phiri.+ 31  “Upange nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pansaluyi upetepo akerubi.+ 32  Nsalu imeneyi uipachike pamizati inayi ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyi tikhale tagolide. Mizati imeneyi ikhale pazitsulo zinayi zasiliva zamphako. 33  Nsalu yotchingayi uipachike m’munsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la umboni+ kuseri kwa nsalu yotchingayi. Nsaluyi ikhale malire pakati pa Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+ 34  Ukatero uike chivundikiro pamwamba pa likasa la umboni m’Malo Oyera Koposa. 35  “Kenako uike tebulo kunja kwa nsalu yotchinga ndipo uikekonso choikapo nyale.+ Chimenechi chikhale moyang’anizana ndi tebulo kumbali ina ya chihema chopatulika, chakum’mwera. Tebulo uliike chakumpoto. 36  Ndiyeno uwombe nsalu yotchinga+ khomo la chihema. Nsaluyo ikhale ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ya ulusi wofiira kwambiri, ndi ya ulusi wopota wabwino kwambiri. 37  Nsalu yotchinga khomo la chihema uipangire mizati isanu ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyo tikhale tagolide. Ndipo upange zitsulo zamkuwa zisanu zamphako zokhazikapo mizatiyo.

Mawu a M'munsi