Ekisodo 34:1-35
34 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo ine ndidzalemba pamiyala yosemayo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija,+ imene iwe unaswa.+
2 Ndipo ukonzeke kuti mawa m’mawa ukakwere m’phiri la Sinai ndi kukakhala pafupi ndi ine kumeneko, pamwamba pa phirilo.+
3 Koma usakwere m’phirimo ndi wina aliyense, ndipo musapezeke wina aliyense mmenemo.+ Kuwonjezera apo, nkhosa kapena ng’ombe zisadye m’tsinde mwa phirilo.”+
4 Chotero Mose anasemadi miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo anadzuka m’mamawa ndi kukwera m’phiri la Sinai, atanyamula miyala iwiriyo m’manja mwake, monga momwe Yehova anam’lamulira.
5 Pamenepo Yehova anatsika+ mumtambo ndi kuimirira pafupi ndi Mose, n’kulengeza dzina lake lakuti Yehova.+
6 Ndipo Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wachisomo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ ndi choonadi.+
7 Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha,+ wokhululukira zolakwa ndi machimo,+ koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa.+ Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+
8 Nthawi yomweyo, Mose anagwada n’kuweramira pansi.+
9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+
10 Poyankha Mulungu anati: “Tsopano ndichita nanu pangano ili: Ndidzachita zinthu zodabwitsa pamaso pa anthu ako onse, zinthu zimene sizinachitikepo padziko lonse lapansi kapena m’mitundu yonse.+ Ndipo anthu onse okuzungulirani adzaonadi ntchito za Yehova, chifukwa ndidzachita nanu chinthu chochititsa mantha.+
11 “Koma inu sungani zimene ndikukulamulani lero.+ Inetu ndikuthamangitsa pamaso panu Aamori, Akanani, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+
12 Samalani kuti musachite pangano ndi anthu a m’dziko limene mukupitako+ kuopera kuti ungakhale msampha pakati panu.+
13 Koma maguwa awo ansembe mukawagwetse, zipilala zawo zopatulika mukaziphwanye ndipo mizati yawo yopatulika mukaidule.+
14 Pakuti simuyenera kugwadira mulungu wina,+ chifukwa Yehova, amene dzina lake ndi Nsanje, alidi Mulungu wansanje.*+
15 Samalani, kuopera kuti mungachite pangano ndi anthu okhala m’dzikomo, pakuti iwo adzachita chiwerewere ndi milungu yawo+ ndi kupereka nsembe kwa milungu yawo.+ Chifukwa mukachita nawo pangano, mosakayikira wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+
16 Kenako mudzatenga ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna,+ ndipo ana awo aakazi adzachita chiwerewere ndi milungu yawo, n’kuchititsa ana anu aamuna kuchita chiwerewere ndi milungu yawo.+
17 “Musadzipangire milungu ya mafano opangidwa ndi chitsulo chosungunula.+
18 “Muzisunga chikondwerero cha mkate wosafufumitsa.+ Monga momwe ndinakulamulirani, muzidya mkate wosafufumitsa masiku 7 m’mwezi wa Abibu*+ pa nthawi yoikidwiratu, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi wa Abibu.
19 “Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga,+ ngakhalenso mwana woyamba kubadwa wa ziweto zanu zonse, ng’ombe ndi nkhosa.+
20 Mwana woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa.+ Koma ngati simungamuwombole, muzimupha mwa kum’thyola khosi. Ndipo aliyense woyamba kubadwa mwa ana anu aamuna muzimuwombola.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa ine ali chimanjamanja.+
21 “Muzigwira ntchito zanu kwa masiku 6, koma pa tsiku la 7 muzisunga sabata.+ M’nyengo yolima ndi m’nyengo yokolola muzisunga sabata.+
22 “Muzichita chikondwerero cha masabata ndi tirigu woyamba kucha pa nyengo yokolola tiriguyo.+ Muzichitanso chikondwerero cha zokolola kumapeto kwa chaka.+
23 “Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azionekera+ kwa Ambuye woona, Yehova, Mulungu wa Isiraeli.
24 Pakuti ndidzathamangitsira mitunduyo kutali ndi inu,+ ndipo ndidzakuza dera lanu.+ Palibe aliyense adzasirira dziko lanu pamene mwachoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa chaka.+
25 “Popereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chofufumitsa.+ Ndipo nsembe ya chikondwerero cha pasika isamagone mpaka m’mawa.+
26 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa+ za m’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+
“Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.”+
27 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Dzilembere mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe ndi Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+
28 Choncho Mose anakhalabe m’phirimo ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku. Iye sanadye mkate kapena kumwa madzi.+ Ndipo Mulungu analemba mawu a pangano, Mawu Khumi,* pamiyala yosemayo.+
29 Ndiyeno Mose anatsika m’phiri la Sinai atanyamula miyala iwiri ija ya Umboni m’manja mwake,+ koma iye sanadziwe kuti nkhope yake inali kuwala chifukwa anali atalankhula ndi Mulungu.+
30 Aroni ndi ana onse a Isiraeli ataona Mose, anaona kuti nkhope yake ikuwala, ndipo anaopa kumuyandikira.+
31 Pamenepo Mose anawaitana. Chotero Aroni ndi atsogoleri onse a khamu la Isiraeli anabwerera kwa iye, ndipo Mose anayamba kulankhula nawo.
32 Kenako ana onse a Isiraeli anamuyandikira, ndipo iye anayamba kuwauza malamulo onse amene Yehova anam’patsa paphiri la Sinai.+
33 Mose akatha kulankhula nawo anali kuika chophimba pankhope yake.+
34 Koma Mose akamalowa kukaonekera kwa Yehova kuti akalankhule naye, anali kuchotsa chophimbacho mpaka atatulukamo.+ Kenako anali kupita kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza zimene walamulidwa.+
35 Ndipo ana a Isiraeli anali kuona kuti nkhope ya Mose ikuwala.+ Choncho Mose anali kuphimbanso nkhope yake mpaka atabwerera kukalankhula ndi Mulungu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”
^ Onani Zakumapeto 13.
^ Mawu akuti “Mawu Khumi” akutanthauza mawu khumi olamula, zinthu khumi zoyenera kuchita, kapena Malamulo Khumi.