Ekisodo 20:1-26

20  Ndipo Mulungu anayamba kulankhula mawu awa, kuti:+  “Ine ndine Yehova Mulungu wako,+ amene ndinakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+  Usakhale ndi milungu ina iliyonse+ kupatulapo ine.*  “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi.*+  Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+  Koma ndimasonyeza kukoma mtima kosatha ku mibadwo masauzande chifukwa cha anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.+  “Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala,+ pakuti Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake mosasamala osam’langa.+  “Pokumbukira kuti muyenera kusunga tsiku la sabata ndi kuliona kukhala lopatulika,+  muzichita ntchito zanu zonse masiku 6.+ 10  Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo wokhala mumzinda wanu.+ 11  Pakuti m’masiku 6 Yehova anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili mmenemo,+ ndipo anayamba kupuma pa tsiku la 7.+ N’chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la sabata ndi kulipanga kukhala lopatulika.+ 12  “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ kuti masiku ako atalike m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+ 13  “Usaphe munthu.*+ 14  “Usachite chigololo.+ 15  “Usabe.+ 16  “Usapereke umboni wonamizira mnzako.+ 17  “Usalakelake nyumba ya mnzako. Usalakelake mkazi wa mnzako,+ kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ng’ombe yake, bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”+ 18  Ndiyeno anthu onse anali kumva mabingu ndi kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa ndipo anali kuona kung’anima kwa mphezi ndiponso phiri likufuka utsi. Anthuwo atamva ndi kuona zimenezi ananjenjemera ndipo anaimabe patali.+ 19  Ndipo anthuwo anauza Mose kuti: “Iweyo uzilankhula ndi ife, ndipo ife tizimvetsera, koma Mulungu asalankhule ndi ife kuopera kuti tingafe.”+ 20  Pamenepo Mose anauza anthuwo kuti: “Musaope, chifukwa Mulungu woona wabwera+ kuti akuyeseni, ndi kuti mupitirizebe kumuopa kuti musachimwe.”+ 21  Choncho anthuwo anaimabe patali pomwepo, koma Mose anayandikira mtambo wakuda uja kumene kunali Mulungu woona.+ 22  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:+ “Ana a Isiraeli uwauze kuti, ‘Mwadzionera nokha kuti ine ndalankhula nanu kuchokera kumwamba.+ 23  Musadzipangire milungu yasiliva ndi milungu yagolide kuti muziipembedza pamodzi ndi ine.+ 24  Mundipangire guwa lansembe ladothi,+ ndipo muziperekapo nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zachiyanjano,* nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu.+ M’malo onse amene ndidzachititsa dzina langa kukumbukika ndidzabwera kwa inu ndipo ndidzakudalitsani ndithu.+ 25  Mukandipangira guwa lansembe lamiyala, musamangire miyala yosema. Mukangosema mwala wa guwalo, ndiye kuti mwaipitsa chinthu chopatulika.+ 26  Ndipo guwa langa lansembe lisakhale la masitepe, kuti pokwera pamenepo maliseche anu angaonekere.’

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “motsutsana ndi ine.”
Mawu ake enieni, “madzi a pansi pa dziko,” mwina chifukwa chakuti nyanja ndi mitsinje zimakhala pamalo olowa poyerekeza ndi mtunda.
Kapena kuti “Mulungu wansanje (wachangu); Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.”
Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
Kapena kuti “nsembe zamtendere,” kutanthauza nsembe zosonyeza kuti woperekayo ali pa mtendere ndi Mulungu.