Ekisodo 11:1-10

11  Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Patsala mliri umodzi wokha woti ndikanthe nawo Farao ndi Iguputo. Kenako adzakulolani kuchoka m’dziko lino.+ Pokulolani kuchoka ndi zonse zimene muli nazo, adzachita kukupitikitsani.+  Tsopano uza anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa mnzake zinthu zasiliva ndi zagolide.”+  Pamenepo Yehova anachititsa Aiguputo kukomera mtima Aisiraeli.+ Nayenso Mose analemekezeka kwambiri m’dziko la Iguputo, pamaso pa atumiki a Farao ndi pamaso pa Aiguputo onse.+  Choncho Mose anati: “Yehova wanena kuti, ‘Pakati pa usiku ndidzalowa mu Iguputo,+  ndipo mwana aliyense woyamba kubadwa+ m’dziko la Iguputo adzafa. Kuyambira mwana woyamba wa Farao, amene wakhala pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa kapolo wamkazi wokhala pamphero ndiponso mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse.+  Mudzakhala kulira kwakukulu m’dziko lonse la Iguputo, kulira kumene sikunachitikepo, ndiponso kumene sikudzachitikanso.+  Koma galu sadzauwa aliyense wa ana a Isiraeli, sadzauwa munthu kapena chiweto,+ kuti mudziwe kuti Yehova akhoza kuchitira ana a Isiraeli zinthu zosiyana ndi zimene angachitire Aiguputo.’+  Ndipo atumiki anu onsewa adzatsika ndi kubwera kwa ine, n’kundigwadira ndi kundiweramira.+ Iwo adzanena kuti, ‘Pita, iweyo ndi anthu onse amene amakutsatira.’ Zitatero ndidzapitadi.” Atanena mawu amenewa anachoka kwa Farao atakwiya.  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Farao sadzakumverani inu.+ Izi zili choncho kuti ndichite zozizwitsa zochuluka m’dziko la Iguputo.”+ 10  Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwitsa zonsezi pamaso pa Farao.+ Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, moti sanalole ana a Isiraeli kuchoka m’dziko lake.+

Mawu a M'munsi