Ekisodo 10:1-29
10 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao pakuti ndalola iye pamodzi ndi atumiki ake kuumitsa mitima yawo,+ kuti ndichite zizindikiro zanga pamaso pake.+
2 Ndachita zimenezi kuti mufotokozere ana anu, ndi ana a ana anu, mmene ndakhaulitsira Iguputo ndi zizindikiro zimene ndachitira Aiguputo.+ Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+
3 Choncho Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndi kumuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti, ‘Udzakana kundigonjera kufikira liti?+ Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.
4 Ukapitiriza kukaniza anthu anga kupita, mawa ndikutumizira dzombe m’dziko lako.+
5 Dzombelo lidzakuta nthaka yonse ndipo simudzatha kuona dothi. Lidzadya chilichonse chotsalira. Ndithu, lidzadya chilichonse chimene matalala anakusiyirani. Ndipo lidzadya mitengo yanu yonse imene yaphuka.+
6 Ndipo dzombelo lidzadzaza m’nyumba zanu, m’nyumba zonse za atumiki anu ndi m’nyumba za mu Iguputo monse. Lidzadzaza m’nyumbazi mpaka kufika poti makolo anu ndi makolo a makolo anu sanaonepo chibadwire chawo.’”+ Atatero, Mose anachoka pamaso pa Farao.+
7 Pamenepo atumiki a Farao anamuuza kuti: “Kodi munthu uyu akhala ngati msampha kwa ife kufikira liti?+ Lolani anthuwa apite kuti akatumikire Yehova Mulungu wawo. Kodi simukudziwabe kuti Iguputo wawonongeka?”+
8 Zitatero anabweretsanso Mose ndi Aroni kwa Farao ndipo iye anati: “Pitani, katumikireni Yehova Mulungu wanu.+ Ndani kwenikweni amene akupita?”
9 Pamenepo Mose anati: “Tipita ndi achinyamata athu ndi achikulire omwe. Tipita ndi ana athu aamuna ndi ana athu aakazi+ pamodzi ndi nkhosa ndi ng’ombe zathu,+ chifukwa tikukachitira Yehova chikondwerero.”+
10 Farao anawayankha kuti: “Ngati ndingalole n’komwe kuti inu pamodzi ndi ana anu mupite,+ ndiye kuti Yehova alidi ndi inu. Ndikudziwatu kuti zolinga zanu ndi zoipa.+
11 Sizitheka! Pitani amuna amphamvu nokhanokha, mukatumikire Yehova chifukwa ndi zimene mukufuna.” Atanena mawu amenewa, anawachotsa pamaso pa Farao.+
12 Chotero Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula+ dzanja lako ndi kuloza dziko la Iguputo, kuti dzombe ligwe m’dziko lonselo ndi kudya zomera zonse za m’dzikomo, chilichonse chimene matalala anasiya.”+
13 Pomwepo Mose analoza dziko lonse la Iguputo ndi ndodo yake, ndipo Yehova anachititsa mphepo yochokera kum’mawa+ kuwomba padziko lonselo, usana wonse ndi usiku wonse. M’mawa kutacha mphepoyo inabweretsa dzombe.
14 Ndipo dzombelo linayamba kufika m’dziko lonse la Iguputo ndi kutera m’madera onse a dzikolo.+ Linawasautsa kwambiri.+ Dzombe ngati limeneli linali lisanagwepo n’kale lonse ndipo sipadzagwanso lina ngati limeneli.
15 Dzombelo linakuta nthaka yonse ya m’dzikolo+ ndipo dziko linachita mdima.+ Dzombelo linadya zomera zonse za m’dzikolo ndi zipatso zonse za m’mitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala,+ moti sipanatsale chobiriwira chilichonse m’mitengo kapena pa zomera m’dziko lonse la Iguputo.+
16 Mwamsanga Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni n’kuwauza kuti: “Ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso ndachimwira inu.+
17 Chotero ndikhululukireni+ tchimo langa kamodzi kokha kano, ndipo chondererani+ Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wakuphawu.”
18 Pamenepo anachoka pamaso pa Farao ndipo anapita kukachonderera Yehova.+
19 Atatero Yehova anasintha mphepo yamphamvuyo kuti iziwomba kuchokera kumadzulo ndipo inatenga dzombelo ndi kulithira m’Nyanja Yofiira. Motero m’dera lonse la Iguputo simunatsale dzombe ngakhale limodzi.
20 Koma Yehova analola Farao kuumitsabe mtima wake,+ ndipo sanalole ana a Isiraeli kuchoka.
21 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza kumwamba+ kuti m’dziko lonse la Iguputo mugwe mdima wandiweyani.”
22 Nthawi yomweyo, Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza kumwamba, ndipo m’dziko lonse la Iguputo munachita mdima wandiweyani kwa masiku atatu.+
23 Anthu sanathe kuonana ndipo palibe anachoka pakhomo pake kwa masiku atatu. Koma kumene ana onse a Isiraeli anali kukhala kunali kuwala.+
24 Zitatero Farao anaitana Mose ndi kumuuza kuti: “Pitani, katumikireni Yehova.+ Koma nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu simupita nazo. Ana anu pitani nawo.”+
25 Koma Mose anati: “Inuyo mutipatse nyama zokapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kuti tikazipereke kwa Yehova Mulungu wathu.+
26 Komanso ziweto zathu tipita nazo.+ Sitidzasiya chiweto ngakhale chimodzi, chifukwa tiyenera kukatengapo zina ndi kukazigwiritsa ntchito polambira Yehova Mulungu wathu.+ Pakali pano sitikudziwa kuti tikapereka chiyani polambira Yehova mpaka titakafika kumeneko.”+
27 Pamenepo Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli achoke.+
28 Choncho Farao anauza Mose kuti: “Choka!+ Samala! Ndisadzakuonenso, chifukwa ndikadzangokuonanso udzafa.”+
29 Ndipo Mose anayankha kuti: “Chabwino. Sindidzayesanso kuonana nanu.”+