Ekisodo 21:1-36

21  “Ndipo izi ndizo zigamulo zoti uwaikire:+  “Ukagula kapolo wachiheberi,+ adzakhala kapolo wako kwa zaka 6, koma m’chaka cha 7 azimasuka ndipo azichoka osam’lipiritsa.+  Ngati anabwera ali yekha, adzachokanso ali yekha. Ngati ali ndi mkazi, mkazi wakeyo adzapita naye.  Ngati mbuye wake wamupatsa mkazi n’kubereka naye ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo ndi ana ake adzakhala a mbuye wake,+ ndipo mwamunayo adzachoka yekha.+  Koma kapoloyo akanena motsimikiza kuti, ‘Ndimam’konda kwambiri mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana anga, ndipo sindikufuna kuchoka monga womasulidwa,’+  pamenepo mbuye wakeyo azibwera naye pafupi ndi Mulungu woona ndi kufika naye pachitseko kapena pafelemu. Akatero mbuye wakeyo amuboole khutu ndi choboolera, ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.+  “Munthu akagulitsa mwana wake wamkazi kukhala kapolo,+ sadzachoka mmene akapolo aamuna amachokera.  Ngati mbuye wake sanakondwere naye kuti akhale mkazi wake wamng’ono+ koma wamulola kuwomboledwa, mbuyeyo alibe ufulu womugulitsa kwa anthu a mtundu wina chifukwa wam’chitira zachinyengo.  Koma akamupereka kwa mwana wake wamwamuna, azim’patsa ufulu wonse umene umaperekedwa kwa ana aakazi.+ 10  Mwana wamwamunayo akakwatira mkazi wina, woyambayo asaleke kum’patsa chakudya, zovala+ ndi mangawa ake+ a mu ukwati. 11  Koma ngati sakum’patsa zinthu zitatu zimenezi, mkaziyo achoke popanda kupereka chilichonse, popanda kumulipiritsa ndalama. 12  “Amene wamenya munthu mpaka munthuyo kufa ayenera kuphedwa ndithu.+ 13  Koma ngati sanachite kum’dikirira, ndipo Mulungu woona walola kuti mwangozi munthuyo afere m’manja mwake,+ pamenepo ndidzakukonzerani malo amene angathawireko.+ 14  Munthu amene wapsera mtima mnzake mpaka kumupha mwachiwembu,+ ngakhale atathawira kuguwa langa lansembe kuti atetezeke, muzimuchotsa n’kukamupha.+ 15  Womenya abambo ake ndi mayi ake aziphedwa ndithu.+ 16  “Wakuba munthu+ ndi kum’gulitsa+ kapena munthu amene wapezeka ndi munthu wobedwayo, aziphedwa ndithu.+ 17  “Wotemberera bambo ake ndi mayi ake aziphedwa ndithu.+ 18  “Anthu akayamba kukangana, wina n’kutema mnzake ndi mwala kapena khasu, mnzakeyo osafa koma wadwala ndipo wagona, 19  akadzuka n’kuyamba kuyendayenda kunja pogwiritsa ntchito ndodo, pamenepo amene anam’tema uja salandira chilango. Koma adzapereka malipiro a nthawi imene wotemedwayo wakhala wosagwira ntchito, mpaka mnzakeyo atachiriratu. 20  “Munthu akamenya+ kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo, kapoloyo n’kumufera, munthuyo azilangidwa ndithu.+ 21  Koma ngati kapoloyo wakhalabe ndi moyo tsiku limodzi kapena masiku awiri, mbuye wakeyo sayenera kulangidwa chifukwa kapoloyo ndi chuma chake. 22  “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi wapakati moti mkaziyo n’kubereka mwana+ koma palibe amene wamwalira, wovulaza mkaziyo azimulipiritsa ndithu malinga ndi zimene mwiniwake wa mkaziyo angagamule. Azikapereka malipirowo kudzera mwa oweruza.+ 23  Ngati wina wamwalira, pamenepo uzipereka moyo kulipira moyo.+ 24  Koma wina akavulaza mnzake koopsa, pazikhala diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi,+ 25  kutentha ndi moto kulipira kutentha ndi moto, chilonda kulipira chilonda, kumenya kulipira kumenya.+ 26  “Munthu akamenya kapolo wake wamwamuna kapena kapolo wake wamkazi padiso n’kumuvulaza kwambiri, azimasula kapoloyo ndi kumulola kuchoka monga malipiro a diso lake.+ 27  Ndipo akagulula dzino la kapolo wake wamwamuna kapena la kapolo wake wamkazi, azimasula kapoloyo ndi kumulola kuchoka monga malipiro a dzino lake. 28  “Ng’ombe ikagunda mwamuna kapena mkazi, munthuyo n’kumwalira, ng’ombeyo iziponyedwa miyala ndi kuphedwa+ ndithu, ndipo nyama yake isadyedwe. Zikatero mwiniwake wa ng’ombeyo sayenera kulangidwa. 29  Koma ngati ng’ombe inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwiniwake anachenjezedwapo koma sanali kuiyang’anira, ndiyeno yapha mwamuna kapena mkazi, ng’ombeyo iziponyedwa miyala ndipo mwiniwakeyo aziphedwanso. 30  Ngati waweruzidwa kuti apereke dipo,* ayenera kulipira mtengo wonse wowombolera moyo wake umene amugamula.+ 31  Kaya ng’ombeyo inagunda mwana wamwamuna kapena mwana wamkazi, mwiniwake aziweruzidwa malinga ndi chigamulo chimenechi.+ 32  Ngati yagunda kapolo wamwamuna kapena wamkazi, mwiniwake azilipira ndalama zokwana masekeli* 30+ kwa mbuye wa kapoloyo, ndipo ng’ombeyo iziponyedwa miyala. 33  “Munthu akasiya dzenje losavindikira, kapena akakumba dzenje koma osatsekapo, ndipo ng’ombe kapena bulu n’kugweramo,+ 34  mwiniwake wa dzenjelo azilipira.+ Malipirowo azipereka kwa mwiniwake wa ng’ombeyo, koma iye azitenga nyama yakufayo. 35  Ng’ombe ya munthu ikavulaza ndi kupha ng’ombe ya mnzake, pamenepo azigulitsa ng’ombe yamoyoyo ndi kugawana ndalamazo, ndipo azigawananso yakufayo.+ 36  Kapena ngati ng’ombe inali kudziwika ndi chizolowezi chogunda zinzake, koma mwiniwake sanali kuiyang’anira,+ azipereka ndithu+ ng’ombe kulipira ng’ombe, ndipo azitenga yakufayo.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.