Ekisodo 19:1-25

19  M’mwezi wachitatu kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo,+ pa tsiku lomwelo,* iwo analowa m’chipululu cha Sinai.+  Ananyamuka ku Refidimu+ n’kulowa m’chipululu cha Sinai+ ndi kumanga msasa wawo m’chipululumo. Aisiraeli anamanga msasawo pafupi ndi phiri la Sinai.+  Pamenepo Mose anakwera m’phirimo kukaonekera kwa Mulungu woona. Ndipo Yehova anayamba kumulankhula m’phirimo+ kuti: “Ukanene mawu awa kunyumba ya Yakobo, ana a Isiraeli kuti,  ‘Inu munaona nokha zimene ndinachitira Aiguputo,+ kuti ndikunyamuleni pamapiko a chiwombankhanga ndi kukubweretsani kwa ine.+  Tsopano ngati mudzalabadiradi+ mawu anga ndi kusunga pangano langa,+ pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse,+ chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa.+  Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyera.’+ Ukanene mawu amenewa kwa ana a Isiraeli.”  Choncho Mose anatsika n’kuitanitsa akulu onse+ a anthu, ndipo anawauza mawu onse amene Yehova anam’lamula.+  Kenako anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo.”+ Nthawi yomweyo Mose anatenga mawu a anthuwo ndi kubwerera nawo kwa Yehova.+  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Tamvera! Nditsikira kwa iwe mumtambo wakuda,+ kuti anthu amve pamene ndikulankhula ndi iwe,+ ndi kuti iwenso azikukhulupirira nthawi zonse.”+ Choncho Mose anali atanena mawu a anthuwo kwa Yehova. 10  Ndipo Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa anthu, uwayeretse lero ndi mawa, ndipo achape zovala zawo.+ 11  Pa tsiku lachitatu akhale okonzeka, chifukwa pa tsiku lachitatulo Yehova adzatsikira paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.+ 12  Ndipo anthuwo uwadulire malire kuzungulira phiri lonse, ndi kuwauza kuti, ‘Onetsetsani kuti musakwere m’phiri, ndipo musakhudze tsinde lake. Aliyense amene adzakhudza phirili adzaphedwa ndithu.+ 13  Palibe munthu amene ayenera kudzakhudza wolakwayo, chifukwa adzaponyedwa miyala kapena kulasidwa ndithu. Kaya ndi nyama kapena munthu, sadzayenera kukhala ndi moyo.’+ Lipenga la nyanga ya nkhosa likalira,+ anthu onse ayandikire kuphiri.” 14  Ndiyeno Mose anatsika m’phirimo kupita kwa anthu n’kuyamba kuyeretsa anthuwo. Ndipo iwo anayamba kuchapa zovala zawo.+ 15  Kenako anauza anthuwo kuti: “Pofika tsiku lachitatu mukhale okonzeka.+ Amunanu musayandikire akazi anu.”*+ 16  Pa tsiku lachitatu kutacha, kunayamba kuchita mabingu ndi mphezi.+ Mtambo wakuda+ unakuta phiri, ndipo kunamveka kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga la nyanga ya nkhosa,+ moti anthu onse mumsasawo anayamba kunjenjemera.+ 17  Zitatero Mose anatulutsa anthuwo mumsasa kuti akakumane ndi Mulungu woona, ndipo anapita kukaima m’tsinde mwa phirilo.+ 18  Pamenepo phiri la Sinai linafuka utsi ponseponse,+ chifukwa chakuti Yehova anatsikira paphiripo m’moto.+ Utsi wakewo unali kukwera kumwamba ngati utsi wa uvuni,+ ndipo phiri lonse linali kunjenjemera kwambiri.+ 19  Pamene kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kunali kupitiriza kukwererakwerera, Mose anayamba kulankhula, ndipo Mulungu woona anamuyankha ndi mawu amphamvu.+ 20  Pamenepo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamwamba pa phirilo. Kenako Yehova anaitana Mose kuti akwere pamwamba pa phirilo, ndipo Mose anakweradi.+ 21  Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tsika ukachenjeze anthuwo, kuti asayese kudumpha malire kufika kwa Yehova pofuna kuonetsetsa, chifukwa onse oterowo angafe.+ 22  Nawonso ansembe amene amayandikira kwa Yehova kawirikawiri adziyeretse,+ kuti mkwiyo wa Yehova usawayakire.”+ 23  Pamenepo Mose anauza Yehova kuti: “Anthuwa sangafike paphiri la Sinai, chifukwa inu munawachenjeza kale pamene munandiuza kuti: ‘Udule malire kuzungulira phiri kuti likhale lopatulika.’”+ 24  Koma Yehova anamuuza kuti: “Pita, tsika, ndipo ukabwerenso iweyo limodzi ndi Aroni. Koma ansembe ndiponso anthu asalumphe malire kuti akwere kwa Yehova, chifukwa mkwiyo wake ungawayakire.”+ 25  Mose anachitadi zomwezo, ndipo anatsikira kwa anthu n’kuwauza zonsezi.+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti mawu amenewa akutanthauza tsiku limene ananyamuka ku Refidimu.
Apa akunena za kugonana.