Ekisodo 7:1-25

7  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Taona, ndakuika kuti ukhale Mulungu kwa Farao,+ ndipo Aroni m’bale wako akhala mneneri wako.+  Iwe uzimuuza zonse zimene ndizikulamula,+ koma Aroni m’bale wako azikulankhulira kwa Farao,+ ndipo adzaloladi ana a Isiraeli kuchoka m’dziko lake.+  Koma ine ndidzamusiya Farao kuti aumitse mtima wake,+ ndipo ndidzachita zizindikiro ndi zozizwitsa zochuluka m’dziko la Iguputo.+  Komabe Farao sadzakumverani,+ motero ndidzaonetsa mphamvu ya dzanja langa pa Iguputo ndi kutulutsa makamu anga,+ anthu anga,+ ana a Isiraeli,+ m’dziko la Iguputo ndi ziweruzo zamphamvu.+  Pamenepo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzatambasula dzanja langa ndi kukantha Iguputo.+ Motero ndidzatulutsa ana a Isiraeli m’dzikolo.”+  Choncho Mose ndi Aroni anachitadi monga momwe Yehova anawalamulira.+ Anachitadi momwemo.+  Pa nthawi imene analankhula ndi Farao, Mose anali ndi zaka 80 ndipo Aroni anali ndi zaka 83.+  Ndiyeno Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti:  “Farao akakanena kuti, ‘Ndisonyezeni chozizwitsa,’+ iweyo ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako+ ndi kuiponya patsogolo pa Farao.’ Akakatero, idzasanduka njoka yaikulu.”+ 10  Chotero Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndi kuchita ndendende mmene Yehova anawalamulira. Pamenepo Aroni anaponya ndodo yake patsogolo pa Farao ndi atumiki ake, ndipo ndodoyo inasanduka njoka yaikulu. 11  Komabe, Farao nayenso anaitana amuna ake anzeru ndi amatsenga.+ Choncho ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo.+ 12  Aliyense wa iwo anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka njoka zazikulu. Koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zawo. 13  Ngakhale zinali choncho, Farao anaumitsabe mtima wake,+ ndipo sanawamvere, monga momwe Yehova ananenera. 14  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Farao waumitsa mtima wake.+ Iye wakana kuti ana a Isiraeli achoke.+ 15  M’mawa upite kwa Farao. Iyetu adzakhala akupita kumtsinje.+ Choncho iweyo ukaime poti ukathe kukumana naye m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo,+ ndipo udzatenge ndodo imene inasanduka njoka ija.+ 16  Kumeneko ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wandituma kwa iwe+ ndi uthenga wonena kuti: “Lola anthu anga kuchoka kuti akanditumikire m’chipululu,”+ koma kufikira tsopano sukundimvera. 17  Yehova wanena kuti:+ “Ndimenya madzi a mumtsinje wa Nailo+ ndi ndodo imene ili m’dzanja langa, ndipo madzi asanduka magazi.+ Zikatero udziwa kuti ine ndine Yehova.+ 18  Nsomba zimene zili mumtsinje wa Nailo zifa,+ ndipo mtsinje wa Nailo ununkha,+ moti Aiguputo safunanso kumwa madzi ake.”’”+ 19  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, utambasule dzanja lako+ ndi kuloza madzi a mu Iguputo. Uloze mitsinje yawo, ngalande zawo zochokera kumtsinje wa Nailo, zithaphwi zawo,+ ndi maiwe awo onse kuti asanduke magazi.’ Pamenepo madzi a m’dziko lonse la Iguputo, ngakhalenso madzi a m’mitsuko yawo ya mtengo ndi ya mwala adzakhala magazi.” 20  Nthawi yomweyo Mose ndi Aroni anachita zomwezo,+ monga momwe Yehova anawalamulira.+ Ndipo Aroni anatenga ndodo yake ndi kumenya madzi a mumtsinje wa Nailo, Farao ndi atumiki ake akuona.+ Pamenepo madzi onse a mumtsinje wa Nailo anasanduka magazi.+ 21  Zitatero nsomba za mumtsinje wa Nailo zinafa,+ ndipo mtsinje wa Nailo unayamba kununkha. Aiguputo sanathenso kumwa madzi a mumtsinje wa Nailo.+ M’dziko lonse la Iguputo munali magazi okhaokha. 22  Komano, ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo,+ moti Farao anaumitsabe mtima wake,+ ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, monga Yehova ananenera.+ 23  Pamenepo Farao anabwerera kunyumba kwake, ndipo sanafune m’pang’ono pomwe kumvanso za nkhani imeneyi.+ 24  Kenako Aiguputo onse anayamba kukumba zitsime m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo, kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sakanatha kumwa madzi a mumtsinje wa Nailo.+ 25  Kuchokera pamene Yehova anasandutsa madzi a mumtsinje wa Nailo kukhala magazi, panadutsa masiku 7.

Mawu a M'munsi