Ekisodo 35:1-35

35  Kenako Mose anaitana khamu lonse la ana a Isiraeli ndi kuwauza kuti: “Tamverani zimene Yehova walamula kuti muzichita:+  Muzigwira ntchito masiku 6,+ koma tsiku la 7 likhale lopatulika kwa inu, likhale sabata la Yehova lopuma pa ntchito zanu zonse. Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli adzaphedwa.+  Pa tsiku la sabata, musayatse moto m’malo anu alionse okhala.”  Pamenepo Mose anauza msonkhano wonse wa ana a Isiraeli kuti: “Yehova walamula kuti,  ‘Nonse mupereke zopereka kwa Yehova.+ Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa+ apereke kwa Yehova zinthu monga golide, siliva, mkuwa,+  ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ubweya wa mbuzi.+  Aperekenso zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe,  mafuta a nyale, mafuta a basamu opangira mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+  miyala ya onekisi, miyala yozika pa efodi*+ ndi pachovala pachifuwa.+ 10  “‘Onse aluso+ pakati panu abwere ndi kupanga zinthu zonse zimene Yehova walamula. 11  Zinthu zimenezo ndizo chihema chopatulika ndi chophimba chake, ngowe zake, mafelemu ake, mipiringidzo yake, nsanamira zake ndi zitsulo zake zokhazikapo mafelemu ndi mizati. 12  Apangenso likasa+ ndi mitengo yake yonyamulira,+ chivundikiro,+ nsalu yotchinga,+ 13  tebulo+ ndi zipangizo zake zonse ndi mitengo yake yonyamulira, mkate wachionetsero,+ 14  choikapo nyale+ zounikira ndi zipangizo zake, nyale zake, ndi mafuta+ a nyalezo. 15  Apangenso guwa lansembe zofukiza+ ndi mitengo yake yonyamulira, mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga pakhomo la chihema chopatulika, 16  guwa lansembe+ zopsereza ndi sefa wake wa zitsulo zamkuwa zolukanalukana, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse, beseni+ ndi choikapo chake. 17  Apange nsalu za mpanda wa bwalo,+ mizati yake ndi zitsulo zake zokhazikapo mizatiyo, nsalu yotchinga chipata cha bwalolo, 18  zikhomo za chihema chopatulika, zikhomo za bwalo ndi zingwe zake.+ 19  Apangenso zovala+ zosokedwa bwino zoti azivala potumikira m’malo opatulika, zovala zopatulika+ za Aroni wansembe ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.’” 20  Pamenepo msonkhano wonse wa ana a Isiraeli unachoka pamaso pa Mose. 21  Kenako aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa,+ komanso, aliyense amene anali ndi mzimu wofunitsitsa, anabwera ndipo anabweretsa zopereka kwa Yehova zoti zikagwire ntchito pachihema chokumanako ndi pa utumiki wonse wochitika pamenepo. Anabweretsanso zinthu zopangira zovala zopatulika. 22  Ndipo anali kubwerabe amuna pamodzi ndi akazi, aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa, amene anapereka nsembe yoweyula* yagolide kwa Yehova. Iwo anabweretsa zokometsera zomanga pazovala, ndolo, mphete, zokongoletsera za akazi, ndi zinthu zosiyanasiyana zagolide.+ 23  Ndipo onse amene anali ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.+ 24  Onse amene anapereka chopereka chasiliva ndi mkuwa anapereka zoperekazo kwa Yehova, ndipo onse amene anali ndi matabwa a mthethe oti akagwire ntchito pa utumiki wonse wa pachihema chopatulika anabwera nawo. 25  Akazi onse aluso+ anawomba nsalu ndi manja awo, ndipo anali kubweretsabe zingwe zopota za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri. 26  Ndipo akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi. 27  Atsogoleri anabweretsa miyala ya onekisi ndi miyala yozika pa efodi ndi pachovala pachifuwa,+ 28  mafuta a nyale, mafuta a basamu opangira mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira.+ 29  Mwamuna ndi mkazi aliyense wofunitsitsa kupereka kenakake ku ntchito zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose, anachita zimenezo. Ana a Isiraeli anabweretsa nsembe yaufulu kwa Yehova.+ 30  Kenako Mose anauza ana a Isiraeli kuti: “Yehova waitana ndi kutchula dzina Bezaleli,+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda. 31  Ndipo anam’patsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse. 32  Anam’patsa mzimuwo kutinso akhale wotha kulinganiza kapangidwe ka zinthu, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,+ 33  waluso lolemba pamiyala mochita kugoba ndi wodziwa kupanga mwaluso zinthu zina zilizonse zamatabwa.+ 34  Mulungu waika luso lophunzitsa mumtima mwa Bezaleli ndi mwa Oholiabu+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani. 35  Iye wawapatsa mtima wanzeru+ kuti akhale amisiri aluso pa ntchito zonse za mmisiri wolinganiza kawombedwe ka nsalu+ ndi mmisiri wopeta nsalu ndi ulusi wabuluu. Wawapatsa nzeru zimenezi kutinso achite ntchito za mmisiri wopeta nsalu ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ntchito za mmisiri wowomba nsalu. Watero kuti akhale amuna ogwira ntchito ina iliyonse ndi kulinganiza kapangidwe ka zinthu.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:5.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.