Ekisodo 4:1-31

4  Koma Mose anayankha kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupirira ndi kumvera mawu anga?+ Chifukwatu adzanena kuti, ‘Yehova sanaonekere kwa iwe.’”  Pamenepo Yehova anamufunsa kuti: “Chili m’dzanja lakocho n’chiyani?” ndipo Mose anayankha kuti: “Ndodo.”+  Kenako iye anati: “Iponye pansi.” Anaiponya pansi ndipo inasanduka njoka.+ Pamenepo Mose anayamba kuthawa.  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Igwire kumchira.” Choncho Mose anaigwira, ndipo inasandukanso ndodo m’dzanja lake.  Popitiriza Mulungu anati: “Ukachite zimenezi kuti akakhulupirire kuti Yehova Mulungu wa makolo awo,+ Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo,+ anaonekera kwa iwe.”+  Kenako Yehova anamuuzanso kuti: “Lowetsa dzanja lako m’malaya pachifuwa.” Choncho Mose analowetsa dzanja lake m’malaya. Koma politulutsa, dzanja lakelo linali litachita khate, ndipo linaoneka loyera kwambiri ngati chipale chofewa.+  Ndiyeno Mulungu anati: “Lowetsanso dzanja lako m’malayamo.” Choncho analowetsanso dzanja lake m’malaya. Atalitulutsa anaona kuti lakhalanso bwino ngati poyamba.+  Mulungu anapitiriza kuti: “Ngati sakakukhulupirira ndi kulabadira chizindikiro choyamba, akakhulupirira chizindikiro chachiwirichi.+  Komabe ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwirizi ndi kumvera mawu ako,+ ukatenge madzi a mumtsinje wa Nailo n’kuwathira panthaka youma. Ndipo madziwo, amene ukatenge mumtsinje wa Nailo, adzasanduka magazi panthakapo. Ndithu adzasanduka magazi.”+ 10  Ndiyeno Mose anauza Yehova kuti: “Pepani Yehova, ine sinditha kulankhula, kuyambira kalekale, kapena pamene mwalankhula ndi ine mtumiki wanu. Pakuti ndimalankhula movutikira ndipo ndine wa lilime lolemera.”+ 11  Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndani, kapena ndani amapanga munthu wosalankhula, wogontha, woona kapena wakhungu? Kodi si ine, Yehova?+ 12  Choncho pita. Ine ndidzakhala nawe polankhula ndipo ndidzakuuza zonena.”+ 13  Koma Mose anati: “Pepani Yehova. Chonde, tumizani wina aliyense amene mungam’tumize.” 14  Zitatero, Yehova anamukwiyira kwambiri Mose ndipo anati: “Kodi Aroni Mlevi si m’bale wako?+ Ndikudziwa kuti amatha kulankhula. Ndiponso, iye ali m’njira kudzakuchingamira. Akakuona, adzakondwera kwambiri mumtima mwake.+ 15  Ukalankhule naye ndi kumuuza zokanena.+ Ineyo ndidzakhala ndi iwe pamodzi ndi iye pamene mukulankhula,*+ ndipo ndidzakuuzani zochita.+ 16  Iyeyo ndiye azikalankhula kwa anthu m’malo mwa iwe.+ Choncho adzakhala ngati kamwa lako, ndipo iwe udzakhala ngati Mulungu kwa iye.+ 17  Ndipo ndodo iyi izikakhala m’dzanja lako kuti ukaigwiritse ntchito pochita zizindikiro.”+ 18  Chotero Mose anapita kwa Yetero apongozi ake ndi kuwauza kuti:+ “Ndikufuna kupita kwa abale anga ku Iguputo kuti ndikaone ngati akali moyo.”+ Choncho, Yetero anayankha Mose kuti: “Pita mu mtendere.”+ 19  Ndiyeno Yehova anamuuza Mose ali ku Midiyani kuti: “Nyamuka, bwerera ku Iguputo, chifukwa onse amene anali kufuna moyo wako anafa.”+ 20  Kenako Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake ndi kuwakweza pabulu, ndi kuyamba ulendo wobwerera ku Iguputo. Komanso, Mose anatenga ndodo ya Mulungu woona m’dzanja lake.+ 21  Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao,+ zozizwitsa zonse zimene ndakulola kukachita. Ndipo ine ndidzamusiya kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+ 22  Choncho ukamuuze Farao kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Isiraeli ndi mwana wanga wamwamuna, mwana wanga woyamba kubadwa.+ 23  Ndipo ndikukuuza kuti: Lola mwana wanga apite kuti akanditumikire. Koma ngati ukukana kumulola kuti apite, taona ndidzapha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba kubadwa.”’”+ 24  Ndiyeno ali pa ulendowo, atafika pamalo ogona,+ Yehova anakumana naye,+ ndipo anali kufunafuna njira yoti amuphere.+ 25  Zitatero, Zipora+ anatenga mwala wakuthwa n’kudula khungu+ la mwana wakeyo. Ndipo khungu analidulalo analiponya pamapazi ake n’kunena kuti: “Popeza ndinu mkwati wa magazi kwa ine.” 26  Atatero, Mulungu anam’siya mwanayo. Pamenepo Zipora anati: “Mkwati wa magazi,” chifukwa cha mdulidwewo. 27  Kenako Yehova anauza Aroni kuti: “Pita kuchipululu+ kukachingamira Mose.” Chotero Aroni ananyamuka ndipo anakumana ndi Mose paphiri la Mulungu woona,+ nam’psompsona. 28  Atakumana, Mose anauza Aroni mawu onse a Yehova, yemwe anam’tuma.+ Anamuuzanso zizindikiro zonse zimene anam’lamula kuchita.+ 29  Kenako Mose ndi Aroni anapita kukasonkhanitsa akulu onse a ana a Isiraeli.+ 30  Pamenepo Aroni anawauza mawu onse amene Yehova anauza Mose,+ ndipo iye anachita zizindikiro+ pamaso pa anthuwo. 31  Zitatero anthuwo anakhulupirira+ Mose. Atamva kuti Yehova wacheukira+ ana a Isiraeli, ndi kutinso waona nsautso yawo,+ anagwada ndi kuweramira pansi.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Ineyo ndidzakhala ndi pakamwa pako komanso pakamwa pake.”