Ekisodo 36:1-38

36  “Bezaleli komanso Oholiabu+ ndi mwamuna aliyense wa mtima wanzeru amene Yehova wam’patsa nzeru+ ndi kuzindikira+ pa zinthu zimenezi, ayenera kugwira ntchitoyi. Iwowa apatsidwa nzeru ndi kuzindikira kuti adziwe kuchita ntchito zonse zopatulika motsatira zonse zimene Yehova walamula.”+  Pamenepo Mose anaitana Bezaleli, Oholiabu ndi mwamuna aliyense wa mtima wanzeru amene Yehova anaika nzeru mumtima mwake.+ Anaitana aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa kugwira ntchitoyi.+  Ndipo iwo anatenga zopereka+ zonse zimene ana a Isiraeli anabweretsa kwa Mose, kuti azigwiritse ntchito pa utumiki wopatulika. Koma ana a Isiraeliwo anapitirizabe kubweretsa kwa Mose nsembe zawo zaufulu tsiku lililonse.  Chotero anzeru onse amene anali kuchita ntchito yonse yopatulika anayamba kubwera mmodzimmodzi, kuchokera ku ntchito zawo zimene anali kuchita.  Ndipo anauza Mose kuti: “Anthu akubweretsa zinthu zambiri kuposa zimene zikufunikira pa ntchito imene Yehova walamula kuti ichitike.”  Chotero Mose analamula kuti alengeze mumsasa wonsewo, kuti: “Abambo ndi amayi, musakonzenso zinthu zina za chopereka chopatulika.” Ndi mawu amenewa, anthu anawaletsa kubweretsa zinthuzo.  Choncho zinthuzo zinali zokwanira pa ntchito yonse yoyenera kuchitika, ndipo zinaposanso zinthu zofunikira pa ntchitoyo.  Ndipo onse a mtima wanzeru+ amene anali kuchita ntchitoyo anayamba kupanga chihema chopatulika,+ nsalu 10 zopetapo akerubi zophimba chihemacho, zopangidwa ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri. Iye* anapanga zonsezi.  M’litali mwake, nsalu iliyonse inali mikono 28, ndipo m’lifupi mwake inali mikono inayi. Nsalu zonse muyezo wake unali wofanana. 10  Nsalu zisanu anazilumikiza,+ ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zinanso zisanu. 11  Kenako anaika zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu imodzi yakumapeto mwa nsalu zolumikizanazo. Anachitanso chimodzimodzi m’mphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi.+ 12  Anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu ina imene inali polumikizirana nsalu ziwirizo. Zingwezo zinakhala moyang’anizana.+ 13  Kenako anapanga ngowe 50 zagolide ndi kulumikiza nsalu ndi ngowezo kuti nsaluzo zikhale chinsalu chimodzi cha chihema.+ 14  Ndiyeno anapanga nsalu za ubweya wa mbuzi zoyala pachihema chopatulika. Anapanga nsalu 11.+ 15  M’litali nsalu iliyonse inali mikono 30, ndipo m’lifupi nsalu iliyonse inali mikono inayi. Nsalu zonse 11 zija muyezo wake unali wofanana.+ 16  Analumikiza nsalu zisanu pazokha, ndi kulumikizanso nsalu 6 pazokha.+ 17  Kenako anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi. Ndipo anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe m’mphepete mwa nsalu inanso yakumapeto, imene inalumikizana ndi inayo.+ 18  Atatero anapanga ngowe 50 zamkuwa zolumikizira nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi.+ 19  Ndiyeno anapanga chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi chophimba chinanso cha pamwamba pake cha chikopa cha akatumbu.+ 20  Kenako anapanga mafelemu oimika a chihema chopatulika a matabwa a mthethe.+ 21  M’litali mwake, felemu lililonse linali mikono 10, ndipo m’lifupi mwake felemu lililonse linali mkono umodzi ndi hafu.+ 22  Felemu lililonse linali ndi mano awiri oyandikana. Mafelemu onse a chihema chopatulika anawapanga motero.+ 23  Choncho anapanga mafelemu 20 a chihema chopatulika omangira mbali ya kum’mwera ya chihemacho, yoyang’ana ku Negebu.+ 24  Kenako anapanga zitsulo 40 zasiliva zamphako zokhazikapo mafelemu 20 aja. Zitsulo ziwiri zokhazikapo felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri zokhazikapo felemu lina la mano awiri.+ 25  Ndipo anapanga mafelemu 20 kuti akhale kumbali inayo ya chihema chopatulika chakumpoto,+ 26  ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali zokhazikapo felemu limodzi la mano awiri, zitsulo zinanso ziwiri zokhazikapo felemu lina la mano awiri.+ 27  Ndipo kumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo, anapangirako mafelemu 6.+ 28  Ndiyeno anapanga mafelemu awiri kuti akhale mizati ya m’makona akumbuyo a chihema chopatulika.+ 29  Ndipo anali ofanana ndi ophatikana kuyambira pansi mpaka pamwamba, pamphete yoyamba. Mafelemu awiriwo amene anali mizati ya m’makona awiri, anawapanga motero.+ 30  Choncho panali mafelemu 8 ndi zitsulo 16 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zinakhala pansi pa felemu limodzi moyandikana ndi zitsulo zinanso ziwiri za felemu lina.+ 31  Ndiyeno anapanga mipiringidzo yamtengo wa mthethe, mipiringidzo isanu yogwira mafelemu a mbali imodzi ya chihema chopatulika,+ 32  ndi mipiringidzo inanso isanu yogwira mafelemu a mbali ina ya chihema chopatulika. Anapanganso mipiringidzo ina isanu yogwira mafelemu a kumbuyo kwa chihema chopatulika, chakumadzulo.+ 33  Kenako anapanga mpiringidzo wapakati wogwira mafelemu onse kuyambira kumapeto mpaka kumapeto.+ 34  Ndiyeno anakuta mafelemuwo ndi golide, ndipo anapanga mphete zake zagolide zolowetsamo mipiringidzo. Mipiringidzoyo anaikuta ndi golide.+ 35  Kenako anapanga nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pansaluyi anapetapo akerubi.+ 36  Ndiyeno nsalu imeneyi anaipangira mizati inayi ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyi tinali tagolide. Anapanganso zitsulo zinayi zasiliva zamphako, zokhazikapo mizati imeneyi.+ 37  Atatero anawomba nsalu yotchinga khomo la chihema. Nsaluyo inali ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 38  Anapanganso mizati yake isanu ndi tizitsulo take tokolowekapo nsalu yotchingayo. Mitu ya mizatiyo komanso mfundo zake anazikuta ndi golide. Koma zitsulo zake zisanu zamphako zokhazikapo mizatiyo zinali zamkuwa.+

Mawu a M'munsi

“Iye” akuimira Bezaleli.