Ekisodo 15:1-27
15 Pa nthawiyo Mose ndi ana a Isiraeli anayamba kuimbira Yehova nyimbo iyi, kuti:+“Ndiimbira Yehova, pakuti iye wakwezeka koposa.+Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.+
2 Mphamvu ndi nyonga yanga ndi Ya,*+ pakuti wandipulumutsa.+Ameneyu ndi Mulungu wanga, ndidzam’tamanda.+ Ndiye Mulungu wa atate anga,+ ndidzam’kweza.+
3 Yehova ndi wankhondo.+ Dzina lake ndi Yehova.+
4 Magaleta a Farao ndi magulu ake ankhondo wawaponyera m’nyanja.+Asilikali a Farao osankhidwa mwapadera amizidwa mu Nyanja Yofiira.+
5 Amizidwa ndi madzi amphamvu.+ Amira pansi pa nyanja ngati mwala.+
6 Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, likusonyeza kupambana kwa mphamvu zake.+Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, limaphwanya mdani.+
7 Ndipo mu ukulu wanu wopambana mumagwetsa otsutsana nanu.+Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.+
8 Ndi mpweya wotuluka m’mphuno mwanu,+ madzi anaunjikika pamodzi.Madzi oyenda anaima ngati khoma.Madzi amphamvu anaundana pakatikati pa nyanja.
9 Mdaniyo anati, ‘Ndiwathamangira,+ ndi kuwapeza!+Ndigawa chuma chawo.+ Pamenepo moyo wanga ukhutira ndi zimene ndawachita!Ndisolola lupanga langa! Dzanja langa liwawononga!’+
10 Mwapemerera mpweya wanu,+ ndipo nyanja yawamiza.+Amira ngati mtovu m’madzi akuya.+
11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+
12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja,+ ndipo dziko lawameza.+
13 Mwa kukoma mtima kwanu kosatha, mwatsogolera anthu amene munawawombola.+Mwa mphamvu yanu, inu mudzatengera anthu anu kudziko lanu lopatulika kumene mudzakhala.+
14 Anthu adzamva+ ndipo adzatekeseka.+Okhala ku Filisitiya adzamva zopweteka ngati za pobereka.+
15 Pamenepo mafumu a ku Edomu adzasokonezeka.Ndipo olamulira amphamvu a ku Mowabu adzanjenjemera ndi mantha.+Ndithu, anthu onse okhala mu Kanani adzataya mtima.+
16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala chete ngati mwala.Kufikira anthu anu+ atadutsa, inu Yehova,Kufikira anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+
17 Mudzawabweretsa ndi kuwakhazikitsa m’phiri limene ndi cholowa chanu.+Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukakhalemo,+ inu Yehova.Malo opatulika+ amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa.
18 Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale. Adzalamulira mpaka muyaya.+
19 Mahatchi a Farao,+ magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi atalowa m’nyanja,+Yehova wabweza madzi a m’nyanjamo ndi kuwamiza.+Koma ana a Isiraeli ayenda panthaka youma pakati pa nyanja.”+
20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, mlongo wake wa Aroni,+ anatenga maseche m’manja mwake,+ ndipo akazi ena onse anam’tsatira akuimba maseche ndi kuvina.+
21 Ndipo pamene amuna anali kuimba, Miriamu anathirira mang’ombe kuti:+
“Imbirani Yehova+ pakuti wakwezeka koposa.+Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.”+
22 Kenako Mose anauza Isiraeli kuti anyamuke pa Nyanja Yofiira ndipo analowa m’chipululu cha Shura.+ Iwo anayenda m’chipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi.+
23 Kenako anafika ku Mara,+ koma sanathe kumwa madzi a ku Mara chifukwa anali owawa. N’chifukwa chake anatcha malowo kuti Mara.*+
24 Pamenepo anthu anayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Mose,+ kuti: “Timwa chiyani?”
25 Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anam’sonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko m’madzi moti madziwo anakhala okoma.+
Pamenepo Mulungu anawakhazikitsira lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo pa nthawiyo anawayesa.+
26 Ndiyeno anawauza kuti: “Ngati mudzamveradi mawu a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani miliri iliyonse imene ndinagwetsera Iguputo,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikukuchiritsani.”+
27 Kenako anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza.+ Iwo anamanga msasa pamenepo pafupi ndi madzi.
Mawu a M'munsi
^ M’Baibulo lonse, mawu akuti “Ya” akutchulidwa koyamba pavesi lino. Mawu amenewa ndi chidule cha dzina lakuti “Yehova,” ndipo ndi mbali yoyamba ya zilembo zinayi zoimira dzina lenileni la Mulungu, lakuti YHWH. Onani Zakumapeto 2.
^ Dzinali limatanthauza “Kuwawa.”