Ekisodo 17:1-16

17  Ndipo khamu lonse la ana a Isiraeli linanyamuka kuchipululu cha Sini.+ Ulendowo anaugawa mitundamitunda, malinga ndi mmene Yehova anawauzira,+ ndipo anamanga msasa wawo pa Refidimu.+ Koma pamenepo panalibe madzi akumwa.  Ndiyeno anthu anayamba kukangana ndi Mose kuti:+ “Tipatse madzi timwe.” Koma Mose anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyesa Yehova?”+  Choncho anthu anamva ludzu pamenepo, ndipo anthuwo anapitiriza kung’ung’udzira Mose kuti: “N’chifukwa chiyani unatitulutsa mu Iguputo kuti udzatiphe ndi ludzu, ifeyo pamodzi ndi ana athu ndi ziweto zathu?”+  Chotero Mose anafuulira Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pang’ono kundiponya miyala!”+  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Yenda kutsogolo kwa anthu+ ndipo utenge ena mwa akulu a Isiraeli komanso ndodo yako imene unamenya nayo mtsinje wa Nailo.+ Uitenge m’dzanja lako ndipo uziyenda.  Tamvera! Ine ndidzatsogola kukaima pathanthwe ku Horebe.* Kumeneko ukamenye thanthwelo, ndipo padzatuluka madzi amene anthu adzamwa.”+ Chotero Mose anachitadi zomwezo, pamaso pa akulu a Isiraeli,  ndipo iye anatcha malowo Masa*+ ndi Meriba,*+ chifukwa ana a Isiraeli anakangana ndi Mose, komanso chifukwa cha kuyesa Yehova+ kuti: “Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?”+  Ndiyeno Aamaleki+ anabwera kudzamenyana ndi Isiraeli ku Refidimu.+  Zitatero Mose anauza Yoswa* kuti:+ “Tisankhire amuna, ndipo upite nawo+ kukamenyana ndi Aamaleki. Mawa ndikaima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu woona m’dzanja langa.”+ 10  Yoswa anachitadi zimene Mose anamuuza,+ kuti amenyane ndi Aamaleki. Mose, Aroni ndi Hura+ anapita pamwamba pa phiri. 11  Ndiyeno zimene zinali kuchitika n’zakuti, Mose akangokweza dzanja lake m’mwamba, Aisiraeli anali kupambana pankhondoyo,+ koma akangotsitsa dzanja lake, Aamaleki anali kupambana. 12  Manja a Mose atatopa, anatenga mwala ndi kumuikira, ndipo anakhalapo. Aroni ndi Hura anachirikiza manja ake, wina mbali ina winanso mbali ina, moti manja ake anakhalabe choncho mpaka dzuwa kulowa. 13  Motero ndi lupanga, Yoswa anagonjetsa Aamaleki ndi anthu amene anali kumbali yawo.+ 14  Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Lemba zimenezi m’buku monga chikumbutso+ ndi kumuuza Yoswa kuti, ‘M’kupita kwa nthawi ndidzafafaniziratu Aamaleki padziko lapansi* ndipo sadzakumbukika n’komwe.’”+ 15  Pamenepo Mose anamanga guwa lansembe n’kulitcha kuti Yehova-nisi,* 16  ndipo anati: “Popeza dzanja laukira mpando wachifumu+ wa Ya,+ Yehova adzamenya nkhondo ndi Aamaleki ku mibadwomibadwo.”+

Mawu a M'munsi

“Horebe.” Dzinali silikutanthauza phiri limene analandirirapo Malamulo Khumi koma dera lamapiri ambiri lozungulira phiri la Sinai. Derali limadziwikanso ndi dzina lakuti chipululu cha Sinai.
Dzinali likutanthauza kuti “Kuyesa,” kapena kuti “Chiyeso.”
Dzinali likutanthauza kuti “Kukangana; Ndewu,” kapena “Mikangano.”
Mawu ake enieni, “Yehoswa,” kutanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso”; Chigiriki, Ἰησοῦ (I·e·souʹ, “Yesu”).
“Padziko lapansi.” Mawu ake enieni, “pansi pa thambo.”
Zikuoneka kuti dzinali limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Mlongoti Womwe Ndi Chizindikiro Changa.”