Ekisodo 16:1-36

16  Kenako ananyamuka ku Elimu,+ ndipo pa tsiku la 15 la mwezi wachiwiri atachoka m’dziko la Iguputo, khamu lonse la ana a Isiraeli linafika kuchipululu cha Sini,+ chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai.  M’chipululumo khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udzira Mose ndi Aroni.+  Ndipo ana a Isiraeli anali kunena kwa Mose ndi Aroni kuti: “Zikanakhala bwino dzanja la Yehova likanatiphera+ m’dziko la Iguputo, kumene tinali kudya nyama+ ndipo tinali kudya mkate ndi kukhuta. M’malomwake mwatibweretsa m’chipululu muno kuti muphetse mpingo wonsewu ndi njala.”+  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Ndikuvumbitsirani mkate kuchokera kumwamba,+ ndipo anthu azipita kukatola. Aliyense azitola muyezo wom’kwanira pa tsikulo.+ Ndikuchita izi kuti ndiwayese ngati adzatsatira chilamulo changa kapena ayi.+  Pa tsiku la 6+ azikonzeratu zimene atola, ndipo muyezo wake uzikhala wowirikiza kawiri zimene amatola tsiku ndi tsiku.”+  Choncho Mose ndi Aroni anauza ana onse a Isiraeli kuti: “Madzulo ano mudziwa kuti Yehova ndiye anakutulutsani m’dziko la Iguputo.+  Ndipo m’mawa mudzaona ulemerero wa Yehova+ chifukwa wamva kung’ung’udza kwanu kotsutsana ndi Yehovayo. Ife ndife ndani kuti muziting’ung’udzira?”  Ndiyeno Mose anapitiriza kuti: “Mudzaona zimenezi Yehova akakupatsani nyama yoti mudye madzulo ano, ndi mkate wokwanira m’mawa, chifukwa Yehova wamva kung’ung’udza kwanu kumene mukum’ng’ung’udzira. Ife ndife ndani? Kung’ung’udza kwanu si kotsutsana ndi ife, koma n’kotsutsana ndi Yehova.”+  Chotero Mose anauza Aroni kuti: “Uza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova, chifukwa wamva kung’ung’udza kwanu.’”+ 10  Ndiyeno Aroni atangomaliza kulankhula ndi khamu lonse la ana a Isiraeli, iwo anatembenuka ndi kuyang’ana kuchipululu. Ndipo taonani! Ulemerero wa Yehova unaonekera mumtambo.+ 11  Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 12  “Ndamva kung’ung’udza kwa ana a Isiraeli.+ Auze kuti, ‘Madzulo kuli kachisisira* mudzadya nyama, ndipo m’mawa mudzadya mkate ndi kukhuta.+ Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+ 13  Choncho zinachitikadi kuti madzulo kunabwera zinziri+ zimene zinakuta msasa wonse, ndipo m’mawa kunachita mame kuzungulira msasa wonsewo.+ 14  Kenako mame aja anauma ndipo panthaka ya m’chipululumo panapezeka tinthu topyapyala ndi tolimba+ koma tosalala ngati mame+ amene aundana panthaka. 15  Ana a Isiraeli ataona tinthu timeneti anayamba kufunsana kuti: “N’chiyani ichi?” Chifukwa sanadziwe kuti chinali chiyani. Pamenepo Mose anawauza kuti: “Ndi chakudya chimene Yehova wakupatsani.+ 16  Yehova walamula kuti, ‘Tolani chakudya chimenecho, aliyense malinga ndi mmene amadyera.+ Muzitola malinga ndi chiwerengero cha anthu amene ali m’hema wanu. Munthu aliyense muzim’tolera muyezo wa omeri* limodzi.’” 17  Choncho ana a Isiraeli anayamba kuchita zomwezo. Anayamba kutola chakudyacho, moti ena anatola chambiri koma ena chochepa. 18  Akayeza chakudyacho pamuyezo wa omeri, munthu amene anatola chambiri sichinali kuposa muyezowo, ndipo amene anatola chochepa sichinali kuperewera.+ Aliyense anatola malinga ndi mmene amadyera. 19  Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Aliyense asasiyeko chakudyachi mpaka m’mawa.”+ 20  Koma iwo sanamvere Mose. Pamene anthu ena anasiyako chakudyacho mpaka m’mawa, chinatuluka mphutsi ndi kununkha,+ moti Mose anawakalipira kwambiri.+ 21  Ndipo m’mawa uliwonse+ anali kukatola chakudyacho, aliyense malinga ndi mmene amadyera. Dzuwa likatentha, chinali kusungunuka. 22  Pa tsiku la 6, anthuwo anatola muyezo wowirikiza kawiri,+ munthu aliyense maomeri awiri. Pamenepo atsogoleri onse a khamu la Isiraeli anabwera kwa Mose kudzanena. 23  Ndipo iye anawayankha kuti: “Ndi zimene Yehova wanena. Mawa tisunga sabata, sabata lopatulika la Yehova.+ Zimene mungaphike, phikani, ndipo zimene mungawiritse, wiritsani.+ Zotsala zonse muziike pambali ndi kuzisunga mpaka m’mawa.” 24  Choncho anasungadi chakudyacho mpaka m’mawa monga momwe Mose anawalamulira, ndipo sichinanunkhe kapena kuchita mphutsi.+ 25  Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Idyani chakudyachi lero, chifukwa lero ndi sabata+ la Yehova ndipo simukachipeza kunja kwa msasa. 26  Muzitola chakudyachi masiku 6, koma tsiku la 7 ndi sabata.+ Pa tsiku limeneli sichidzapezeka kunja kwa msasa.” 27  Komabe, pa tsiku la 7 anthu ena anapita kuti akatole chakudyacho, koma sanachipeze. 28  Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Kodi anthu inu mudzakanabe kusunga malamulo ndi malangizo anga kufikira liti?+ 29  Dziwani kuti Yehova wakupatsani sabata.+ N’chifukwa chake akukupatsani mkate wa masiku awiri pa tsiku la 6. Pa tsiku la 7 aliyense azikhala pamalo ake.+ Munthu asachoke pamalo ake.” 30  Ndipo anthu anasunga sabata tsiku la 7.+ 31  Chotero nyumba ya Isiraeli inayamba kutcha chakudyacho kuti “mana.”* Chinali choyera ngati njere ya mapira,* ndipo kukoma kwake kunali ngati makeke opyapyala othira uchi.+ 32  Pamenepo Mose anati: “Yehova walamula kuti, ‘Dzazani muyezo umodzi wa omeri ndi mana kuti asungidwe m’mibadwo yanu yonse,+ n’cholinga choti adzaone mkate umene ndinakudyetsani m’chipululu pamene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.’”+ 33  Ndiyeno Mose anauza Aroni kuti: “Tenga mtsuko ndi kuthiramo mana muyezo umodzi wa omeri ndi kuuika pamaso pa Yehova kuti asungidwe m’mibadwo yanu yonse.”+ 34  Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aroni anaikadi mtsukowo patsogolo pa Umboni*+ kuti manawo asungidwe. 35  Ndipo ana a Isiraeli anadya mana kwa zaka 40+ mpaka pamene analowa m’dziko lokhalidwa ndi anthu.+ Mana ndiwo anali chakudya chawo mpaka pamene anafika m’malire a dziko la Kanani.+ 36  Tsopano miyezo 10 ya omeri inali kukwana muyezo umodzi wa efa.*

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.
Muyezo wa “omeri” limodzi ndi wofanana ndi chitini cha malita awiri.
Zikuoneka kuti dzinali limatanthauza kuti “N’chiyani ichi?” Onani vesi 15.
Mawu ake enieni, “njere ya koriyanda.” Koriyanda ndi chomera chimene ena amati “masala,” ndipo njere yake ndi yoyera ngati mapira.
Kapena kuti “Chikumbutso.” Zikuoneka kuti limeneli linali bokosi losungiramo zolembalemba zofunika.
“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.