Ekisodo 29:1-46

29  “Tsopano uchite izi kwa iwo kuti uwayeretse atumikire monga ansembe anga: Utenge ng’ombe yaing’ono yamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo,+ zopanda chilema,+  mkate wopanda chofufumitsa, mkate wozungulira woboola pakati, wopanda chofufumitsa, wothira mafuta ndi timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa, topaka mafuta.+ Uzipange ndi ufa wa tirigu wosalala.  Zimenezi uziike m’dengu ndi kuzipereka zili m’dengu momwemo.+ Uchitenso chimodzimodzi ndi ng’ombe ndi nkhosa ziwiri zija.  “Ndiyeno ubweretse Aroni ndi ana ake pakhomo+ la chihema chokumanako, ndipo uwalamule kuti asambe ndi madzi.+  Kenako utenge zovala+ zija ndi kuveka Aroni. Umuveke mkanjo ndi malaya odula manja a mkati mwa efodi.* Umuvekenso efodi ndi chovala pachifuwa. Efodiyo um’mange bwino ndi lamba wake.+  Ndiyeno umuveke nduwira pamutu pake ndipo panduwirapo uikepo chizindikiro chopatulika cha kudzipereka.+  Kenako utenge mafuta odzozera+ ndi kuwathira pamutu pake ndi kum’dzoza.+  “Ukatero utenge ana ake ndi kuwaveka mikanjo.+  Ndiyeno Aroni ndi ana akewo uwamange malamba a pamimba. Ana akewo uwakulunge mipango kumutu kwawo ndipo unsembe udzakhala wawo. Limeneli ndi lamulo langa mpaka kalekale.+ Choncho upatse Aroni ndi ana ake mphamvu. + 10  “Kenako upereke ng’ombe patsogolo pa chihema chokumanako, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa ng’ombeyo.+ 11  Ndiyeno ng’ombeyo uiphe pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ 12  Ukatero utengeko magazi a ng’ombeyo+ ndi chala chako ndi kuwapaka panyanga za guwa lansembe.+ Otsalawo uwathire pansi, paguwa lansembe.+ 13  Utenge mafuta+ onse okuta matumbo,+ mafuta a pachiwindi,*+ impso ziwiri ndi mafuta ake, n’kuzitentha* paguwa lansembe.+ 14  Koma nyama ya ng’ombeyo, chikopa chake ndi ndowe zake uzitenthe ndi moto kunja kwa msasa.+ Ng’ombeyo ndi nsembe yamachimo. 15  “Ndiyeno utenge nkhosa imodzi,+ ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 16  Nkhosayo uiphe ndi kutenga magazi ake ndi kuwawaza mozungulira paguwa lansembelo.+ 17  Pamenepo uidule ziwaloziwalo. Kenako utsuke matumbo+ ndi ziboda zake ndi kuika chiwalo chilichonse pamodzi ndi chinzake, kuyambira kumiyendo mpaka kumutu. 18  Nkhosa yonseyo uitenthe paguwa lansembe. Imeneyo ndi nsembe yopsereza+ yoperekedwa kwa Yehova, fungo lokhazika mtima pansi.+ Ndiyo nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. 19  “Kenako utenge nkhosa inayo, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 20  Akatero, uphe nkhosayo ndi kutengako magazi ake ndi kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la Aroni, ndi m’munsi pamakutu a kudzanja lamanja a ana a Aroni. Uwapakenso pazala zawo za manthu kudzanja lamanja ndi pazala zawo zazikulu za kumwendo wa kumanja,+ ndipo uwaze magaziwo mozungulira paguwa lansembe. 21  Ndiyeno utengeko magazi amene ali paguwa lansembe ndi mafuta pang’ono odzozera,+ ndi kuwadontheza pa Aroni ndi pazovala zake. Uwadonthezenso pa ana ake ndi zovala zawo kuti Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake ndi zovala zawo akhale oyera.+ 22  “Ndiyeno kunkhosayo utengeko mafuta ndi mchira wa mafuta+ ndi mafuta okuta matumbo, mafuta a pachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja,+ pakuti nkhosayo ndi yowalongera unsembe.+ 23  M’dengu la mikate yosafufumitsa limene lili pamaso pa Yehova utengemo mtanda wobulungira wa mkate, mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta ndi mkate wopyapyala.+ 24  Zonsezi uziike m’manja mwa Aroni ndi m’manja mwa ana ake,+ ndi kuziweyulira* uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+ 25  Ndiyeno uzitenge m’manja mwawo ndi kuzitentha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza, kuti zikhale fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ Ndiyo nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.+ 26  “Kenako utenge nganga ya nkhosa yolongera Aroni unsembe,+ ndi kuiweyulira uku ndi uku monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyo ikhale gawo lako. 27  Pa nkhosa yolongera Aroni ndi ana ake unsembe,+ upatule nganga+ ya nsembe yoweyula imene anaweyula, ndi mwendo wa gawo lopatulika umene anapereka. 28  Zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake mwa lamulo mpaka kalekale. Ana a Isiraeli ayenera kutsatira lamulo limeneli chifukwa ndi gawo lopatulika.+ Lidzakhala gawo lopatulika loyenera kuperekedwa ndi ana a Isiraeli. Limeneli ndi gawo lawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova kuchokera pansembe zawo zachiyanjano.+ 29  “Zovala zopatulika+ za Aroni zidzakhala za ana ake+ obwera m’mbuyo mwake. Adzawadzoza+ ndi kuwapatsa mphamvu atavala zovala zimenezi.+ 30  Wansembe amene adzalowa m’malo mwake kuchokera pakati pa ana ake, amene adzalowa m’chihema chokumanako kukatumikira m’malo oyera azidzavala zovalazo kwa masiku 7.+ 31  “Kenako utenge nkhosa yowalongera unsembe ndi kuwiritsa nyama yake m’malo oyera.+ 32  Ndipo Aroni ndi ana ake adye+ nyama ya nkhosayo ndi mkate umene uli m’dengu, adyere pakhomo la chihema chokumanako. 33  Adye zinthu zimene aphimbira machimo kuti apatsidwe mphamvu ndi kuyeretsedwa.+ Koma munthu wamba asadye nawo, chifukwa ndi zinthu zopatulika.+ 34  Nyama ya nkhosa yowalongera unsembe ndi mkatewo, zikatsala mpaka m’mawa mwake, uzitenthe ndi moto.+ Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zinthu zopatulika. 35  “Uchite zimenezi kwa Aroni ndi ana ake malinga ndi zonse zimene ndakulamula.+ Udzatenga masiku 7 kuti uwapatse mphamvu. + 36  Choncho uzipereka ng’ombe ya nsembe yamachimo tsiku ndi tsiku kuti iphimbe machimo.+ Pamenepo uziyeretsa guwa lansembe ku machimo mwa kuliperekera nsembe yophimba machimo, ndipo uzilidzoza+ kuti likhale loyera. 37  Udzatenga masiku 7 poperekera guwa lansembelo nsembe yophimba machimo. Udzaliyeretse+ kuti likhale guwa lansembe loyera koposa.+ Aliyense wokhudza guwa lansembe azikhala woyera.+ 38  “Zimene uzipereka paguwa lansembelo ndi izi: ana a nkhosa a chaka chimodzi, awiri pa tsiku nthawi zonse.+ 39  Uzipereka mwana wa nkhosa mmodzi m’mawa,+ ndipo mwana wa nkhosa winayo madzulo kuli kachisisira.*+ 40  Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala,+ muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo anayi a vinyo wa nsembe yachakumwa.+ 41  Ndiyeno uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira. Um’pereke pamodzi ndi nsembe yambewu+ yofanana ndi ya m’mawa komanso ndi nsembe yake yachakumwa. Uzipereke monga fungo lokhazika mtima pansi, nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. 42  M’mibadwo yanu yonse, muzipereka nsembe yopsereza imeneyi nthawi zonse+ pakhomo la chihema chokumanako pamaso pa Yehova, kumene ndidzaonekera kwa inu kuti ndilankhule nanu.+ 43  “Chotero ndidzaonekera pamenepo kwa ana a Isiraeli, ndipo malo amenewa adzayeretsedwa ndi ulemerero wanga.+ 44  Ndidzayeretsa chihema chokumanako ndi guwa lansembe. Ndidzayeretsanso+ Aroni ndi ana ake kuti atumikire monga ansembe anga. 45  Choncho ndidzakhala pakati pa ana a Isiraeli, ndipo ndidzakhala Mulungu wawo.+ 46  Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo, amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo kuti ndikhale pakati pawo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wawo.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:7.
Mawu ake enieni, “kuzifukiza.”
“Chiwindi” ena amati “mphafa.”
Mawu akuti “kuweyula” akutanthauza kunyamula chinthu n’kuchiyendetsa mbali iyi ndi mbali inayo.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.
“Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi muyezo wokwana pafupifupi kilogalamu imodzi.
“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.