Ekisodo 30:1-38

30  “Upange guwa lansembe la zofukiza.+ Ulipange ndi matabwa a mthethe.  M’litali mwake likhale mkono umodzi, m’lifupi mwake mkono umodzi. Mbali zake zonse zinayi zikhale zofanana, ndipo msinkhu wake ukhale mikono iwiri. Guwalo likhale ndi nyanga pamwamba pake.+  Ndiyeno ulikute ndi golide woyenga bwino pamwamba pake, ndi m’mbali mwake kuzungulira guwalo, komanso nyanga zake. Upange mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo.+  Kumbali ziwiri za guwalo upangeko mphete zagolide, ziwiri kumbali iyi ndi zinanso ziwiri kumbali inayo. Uzipange m’munsi mwa mkombero kuti muzilowa mitengo yonyamulira guwalo.+  Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo uikute ndi golide.+  Guwalo uliike kutsogolo kwa nsalu yotchinga imene ili pafupi ndi likasa la umboni.+ Likhale patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa Umboni,* pomwe ndidzaonekera kwa iwe.+  “Aroni azifukiza zofukiza zonunkhira paguwapo.+ M’mawa uliwonse akamasamalira nyale,+ azifukiza zofukizazo.  Aziteronso akamayatsa nyalezo madzulo.* Zimenezi ndi zofukiza zoyenera kuperekedwa kwa Yehova nthawi zonse m’mibadwo yanu yonse.  Paguwali usaperekepo zofukiza zosaloleka,+ nsembe yopsereza kapena nsembe yambewu, ndipo usathirepo nsembe yachakumwa. 10  Aroni azipaka ena mwa magazi a nyama ya nsembe yamachimo yophimbira machimo,+ panyanga za guwalo kuti aziphimbira machimo. Azichita zimenezi kamodzi pa chaka+ m’mibadwo yanu yonse. Kwa Yehova, guwalo ndi lopatulika koposa.” 11  Pamenepo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 12  “Ukamachita kalembera pa ana a Isiraeli, + aliyense wa iwo azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi yowawerengayo,+ kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo.+ 13  Owerengedwa onse ayenera kupereka zotsatirazi: hafu ya sekeli yolingana ndi sekeli la kumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli limodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+ 14  Aliyense amene wawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo azipereka choperekacho kwa Yehova.+ 15  Pamene mukupereka kwa Yehova chopereka chokuphimbirani machimo,+ anthu olemera asapereke zochuluka, ndipo osauka asapereke zosakwana hafu ya sekeli.+ 16  Choncho ulandire ndalama zasiliva zophimbira machimo kwa ana a Isiraeli ndi kuzipereka kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wa pachihema chokumanako+ monga dipo la miyoyo yanu, pophimba machimo anu, kuti Yehova akumbukire ana a Isiraeli.” 17  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 18  “Upange beseni losambira lamkuwa ndi choikapo chake chamkuwa.+ Uliike pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe, ndipo uthiremo madzi.+ 19  Pamenepo Aroni ndi ana ake azisamba m’manja ndi mapazi awo.+ 20  Polowa m’chihema chokumanako, kapena popita kukatumikira paguwa lansembe, kukapereka kwa Yehova nsembe yotentha ndi moto,+ azisamba kuti asafe. 21  Azisamba m’manja ndi mapazi awo kuti asafe.+ Limeneli ndi lamulo kwa iwo mpaka kalekale, likhale lamulo kwa Aroni ndi ana ake ku mibadwo yawo yonse.”+ 22  Ndipo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 23  “Koma iweyo utenge mafuta awa onunkhira, abwino koposa:+ madontho oundana a mule*+ masekeli 500, sinamoni*+ wonunkhira bwino hafu ya muyezo wa mule, kapena kuti masekeli 250, ndi kalamasi* wonunkhira+ wokwana masekeli 250. 24  Utengenso kasiya*+ masekeli 500 olingana ndi masekeli a kumalo oyera+ ndi mafuta a maolivi hini+ imodzi. 25  Zinthu zimenezi upangire mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika, mafuta onunkhira osakaniza mwaluso.+ Akhale mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika.+ 26  “Mafuta amenewa udzozere chihema chokumanako,+ likasa la umboni, 27  tebulo ndi ziwiya zake zonse, choikapo nyale ndi ziwiya zake zonse, guwa lansembe zofukiza, 28  guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, komanso beseni ndi choikapo chake. 29  Ndipo uziyeretse kuti zikhale zoyera koposa.+ Aliyense wogwira zinthu zimenezi azikhala woyera.+ 30  Udzoze Aroni+ ndi ana ake,+ ndipo uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga.+ 31  “Ndiyeno uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Mafuta awa akhale mafuta anga ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika m’mibadwo yanu yonse.+ 32  Musapake mafuta amenewa pakhungu la munthu aliyense, ndipo musapange mafuta ofanana nawo pogwiritsa ntchito zinthu zopangira mafutawa. Mafuta amenewa ndi opatulika. Apitirizebe kukhala opatulika kwa inu. 33  Aliyense wopanga mafuta ofanana ndi amenewa, ndiponso amene angapake munthu wamba, ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’”+ 34  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Tenga zonunkhira izi:+ madontho a sitakate,* onika, mafuta onunkhira a galibanamu ndi lubani*+ weniweni. Zonsezi zikhale za muyezo wofanana. 35  Zinthu zimenezi upangire zofukiza,+ msanganizo wa zonunkhiritsa zosakaniza mwaluso, wothira mchere,+ msanganizo weniweni wopatulika. 36  Kenako upere wina mwa msanganizo umenewu kuti ukhale ufa wosalala kwambiri. Uike wina mwa ufawo patsogolo pa Umboni m’chihema chokumanako,+ kumene ndidzaonekera kwa iwe.+ Msanganizowu ukhale wopatulika koposa kwa inu. 37  Musapange zofukiza zanuzanu pogwiritsa ntchito zinthu zopangira msanganizo umenewu.+ Inu muziona zofukiza zimenezi kukhala zopatulika kwa Yehova.+ 38  Aliyense wopanga zofukiza zofanana ndi zimenezi pofuna kudzisangalatsa ndi kununkhira kwake, adzaphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.”

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 16:34.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.
Onani Zakumapeto 12.
Kapena kuti “lolingana ndi sekeli lopatulika.” Umenewu unali muyezo wachikhalire umene anali kuusunga m’chihema chopatulika. N’kutheka kuti mawu akuti “lolingana ndi sekeli la kumalo oyera” anali kungotsindika kuti muyezowo uyenera kukhala wokwanira bwino. Yerekezerani ndi mawu a m’munsi pa 2Sa 14:26.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Sitakate” ndi utomoni wonunkhira wa mitengo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.