Ekisodo 9:1-35

9  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti,+ ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.  Koma ukapitiriza kukana kuti asapite, n’kuwaumirirabe,+  dziwa kuti, dzanja la Yehova+ lipha ziweto zanu zonse.+ Mliri waukulu kwambiri ugwera mahatchi,* abulu, ngamila, ng’ombe ndi nkhosa.+  Ndipo Yehova adzaika malire pakati pa ziweto za Isiraeli ndi ziweto za Iguputo, moti palibe chiweto cha ana a Isiraeli chimene chidzafa.”’”+  Komanso, Yehova anatchuliratu nthawi, kuti: “Mawa, Yehova adzachita zimenezi m’dzikoli.”+  Mogwirizana ndi mawu ake, Yehova anachitadi zimenezi tsiku lotsatira, ndipo ziweto zamitundu yonse za Aiguputo zinayamba kufa,+ koma palibe chiweto ngakhale chimodzi cha ana a Isiraeli chimene chinafa.  Pamenepo Farao anatumiza atumiki ake kukaona, ndipo anapezadi kuti palibe chiweto ngakhale chimodzi cha Aisiraeli chimene chinafa. Ngakhale zinali choncho, Farao anaumitsabe mtima wake,+ osalola ana a Isiraeli kupita.  Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Tengani mwaye wa mu uvuni wodzaza manja anu awiri,+ ndipo Mose auponye m’mwamba, Farao akuona.  Pamenepo udzachuluka ndi kugwa ngati fumbi padziko lonse la Iguputo. Ukatero udzayambitsa zithupsa zimene zizidzaphulika+ pa anthu ndi nyama zomwe, m’dziko lonse la Iguputo.” 10  Choncho iwo anatenga mwaye wa mu uvuni ndi kuima pamaso pa Farao. Pamenepo Mose anauponya m’mwamba, ndipo unayambitsa zithupsa zomaphulika,+ pa anthu ndi nyama. 11  Ndipo ansembe ochita zamatsenga sanathe kuonekera pamaso pa Mose chifukwa cha zithupsazo, popeza zinatuluka pa ansembewo ndi pa Aiguputo onse.+ 12  Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, monga momwe Yehova anauzira Mose.+ 13  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ukalawirire m’mawa kwambiri kukaonana ndi Farao,+ ndipo ukamuuze kuti: ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+ 14  Ukakana, nditumiza miliri yanga yonse pa iwe, pa atumiki ako ndi anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wofanana ndi ine padziko lonse lapansi.+ 15  Pofika pano ndikanatambasula kale dzanja langa ndi kukupha ndi mliri, iweyo ndi anthu ako, kukufafanizani padziko lapansi.+ 16  Koma ndakusiya ndi moyo+ kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+ 17  Kodi ukudzikwezabe pa anthu anga, pokana kuwalola kuti achoke?+ 18  Taona, mawa pa nthawi ngati ino ndigwetsa mvula yamphamvu kwambiri ya matalala, matalala amene sanayambe agwapo mu Iguputo m’mbiri yake yonse mpaka lero.+ 19  Tsopano tumiza atumiki ako kuti asonkhanitse ziweto zako zonse ndi zinthu zako zonse zimene zili kunja ndi kuzilowetsa m’malo otetezeka. Koma munthu aliyense amene adzapezeke kunja osati m’nyumba, ndi nyama iliyonse imene idzapezeke kunja, matalala+ adzawagwera ndipo adzafa.”’” 20  Aliyense amene anaopa mawu a Yehova pakati pa atumiki a Farao anaonetsetsa kuti ziweto zake ndi antchito ake athawira m’nyumba.+ 21  Koma aliyense amene sanalabadire mawu a Yehova anasiya atumiki ake ndi ziweto zake kunja.+ 22  Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako+ ndi kuloza kumwamba, kuti matalala+ agwe m’dziko lonse la Iguputo, kuti agwere anthu, nyama ndi zomera zonse m’dziko la Iguputo.” 23  Ndipo Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza kumwamba ndi ndodo yake. Atatero, Yehova anachititsa mabingu ndipo anagwetsa matalala+ ndi moto padziko lapansi. Choncho Yehova anapitiriza kugwetsa matalala padziko la Iguputo. 24  Motero panagwa matalala, ndipo panali kuwalima moto. Panagwa matalala amphamvu kwambiri amene sanaonekepo n’kale lonse m’dziko lonse la Iguputo.+ 25  Matalalawo anawononga dziko lonse la Iguputo. Anawononga china chilichonse, munthu kapena nyama, ndi mitundu yonse ya zomera zam’munda. Anagwetsanso mitundu yonse ya mitengo.+ 26  Koma kudera la Goseni kokha, kumene kunali ana a Isiraeli, sikunagwe matalala.+ 27  Kenako Farao anatumiza atumiki ake kukaitana Mose ndi Aroni ndi kuwauza kuti: “Tsopano ndachimwa.+ Yehova ndi wolungama,+ koma ine ndi anthu anga ndife olakwa. 28  M’chonderereni Yehova kuti aletse mabingu ndi matalala ake.+ Pamenepo ndikulolani kupita, ndipo simukhalanso kuno.” 29  Choncho Mose anamuyankha kuti: “Ndikangotuluka mumzinda uno, ndikweza manja anga kwa Yehova.+ Mabingu ndi matalala asiya, kuti mudziwe kuti dziko lapansi ndi la Yehova.+ 30  Koma ndikudziwa kuti ngakhale pamenepo inuyo ndi atumiki anu simudzasonyeza kuopa Yehova Mulungu.”+ 31  Pa nthawi imeneyo mbewu za fulakesi* ndi balere zinawonongeka, chifukwa balere anali atacha ndipo fulakesi anali atachita maluwa.+ 32  Koma tirigu*+ sanawonongeke, chifukwa amacha mochedwa. 33  Ndiyeno Mose anachoka pamaso pa Farao, n’kutuluka mumzindawo. Kenako anakweza manja ake kwa Yehova, ndipo mabingu ndi matalala zinasiya, mvulanso inasiya kugwa padziko lapansi.+ 34  Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zasiya, anachimwanso ndipo anaumitsa mtima wake,+ iyeyo ndi atumiki ake. 35  Chotero Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti ana a Isiraeli apite, monga momwedi Yehova ananenera kudzera mwa Mose.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
“Fulakesi” ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Mawu ake enieni, “tirigu ndi sipeloti.” Sipeloti ndi mtundu wa tirigu koma wosakoma ngati tirigu weniweni. Anthu a ku Iguputo kalekalelo anali kulima mbewuyi.