Ekisodo 28:1-43
28 “Koma iwe patula Aroni m’bale wako pamodzi ndi ana ake pakati pa ana a Isiraeli, ndipo Aroniyo+ atumikire monga wansembe wanga pamodzi ndi ana akewo,+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara ndi Itamara.+
2 Aroni m’bale wako umupangire zovala zopatulika kuti zimupatse ulemerero ndi kum’kongoletsa.+
3 Ndipo iwe ulankhule ndi anthu onse aluso amene ndinadzaza mzimu wa nzeru+ m’mitima yawo kuti amupangire Aroni zovala zomuyeretsa, kuti atumikire monga wansembe wanga.+
4 “Zovala zoti apange ndi izi: chovala pachifuwa,+ efodi,*+ malaya akunja odula manja,+ mkanjo wamandalasi, nduwira+ ndi lamba wa pamimba.+ Apange zovala zopatulika za Aroni m’bale wako ndi ana ake, kuti atumikire monga wansembe wanga.
5 Ndipo iwo atenge golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.
6 “Ndipo apange efodi wopeta ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.+
7 Pakhale nsalu ziwiri za m’mapewa ndipo azilumikize pa efodiyo, azilumikize pamapewa.+
8 Ndipo lamba womangira efodi,+ wolumikiza ku efodiyo akhale wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Akhale wopangidwa ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.
9 “Utenge miyala iwiri ya onekisi+ ndi kulembapo+ mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba.+
10 Mayina 6 uwalembe pamwala umodzi ndipo mayina 6 otsalawo uwalembe pamwala winawo motsatira mmene anabadwira.+
11 Ugwiritse ntchito mmisiri wogoba kuti alembe mayina a ana a Isiraeli pamiyala iwiriyo mwaluso la wogoba miyala.+ Awalembe ngati mmene amagobera chidindo. Apange miyalayo moti izitha kulowa m’zoikamo zake zagolide.+
12 Ndipo ulowetse miyala iwiriyo pansalu za m’mapewa za efodi kuti ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Isiraeli.+ Poonekera kwa Yehova, Aroni azidzanyamula mayina awo pansalu ziwiri za m’mapewa ake kuti chikhale chikumbutso.
13 Upange zoikamo miyala zagolide,
14 ndi matcheni awiri agolide woyenga bwino.+ Uwapange ngati zingwe zopota mwaluso, ndipo ulumikize matcheni okhala ngati zingwewo ku zoikamo miyala.+
15 “Upange chovala pachifuwa chachiweruzo+ chopeta mwaluso. Uchipange mwaluso mofanana ndi efodi. Uchipange ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.+
16 Ukachipinda pakati chizikhala chofanana mbali zonse zinayi, m’litali mwake chizikhala chikhatho* chimodzi ndipo m’lifupi mwake chikhatho chimodzi.+
17 Uikepo miyala ndipo ikhale m’mizere inayi.+ Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rube,+ topazi+ ndi emarodi.+
18 Mzere wachiwiri ukhale ndi miyala ya nofeki,+ safiro+ ndi yasipi.+
19 Mzere wachitatu ukhale ndi miyala ya lesemu, sibu+ ndi ametusito.+
20 Mzere wa chinayi ukhale ndi miyala ya kulusolito,+ onekisi+ ndi yade. Zoikamo miyala zake zikhale zagolide.+
21 Miyalayo uiike malinga ndi mayina a mafuko a ana a Isiraeli, malinga ndi mayina a mafuko awo 12.+ Miyalayo ikhale yolembedwa mogoba ngati mmene amagobera chidindo, mwala uliwonse ukhale ndi limodzi mwa mayina a mafuko 12.+
22 “Pachovala pachifuwa upangepo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota.+
23 Upange mphete ziwiri zagolide pachovala pachifuwa,+ mphete ziwirizo uziike m’makona awiri a chovala pachifuwacho.
24 Ndiyeno upise zingwe ziwiri zagolide zija mumphete ziwiri zomwe zili m’makona a chovala pachifuwa.+
25 Ndipo ulowetse zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri zimene zili pansalu za m’mapewa za efodi chapatsogolo pake.+
26 Upange mphete ziwiri zagolide ndi kuziika m’makona awiri a chovala pachifukwa kumbali yopindira mkati yokhudzana ndi efodi.+
27 Upangenso mphete ziwiri zagolide ndi kuziika pansalu ziwiri za pamapewa za efodi m’munsi mwake, kutsogolo kwa nsaluzo, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa lamba wa efodi.+
28 Ndipo azimanga chovala pachifuwa ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chilowe mumphete za chovala pachifuwa ndi mphete za efodi, kuti chovala pachifuwacho chizikhala pamwamba pa lamba wa efodi, kutinso chisasunthe pa efodipo.+
29 “Ndipo Aroni azinyamula mayina a ana a Isiraeli pamtima pake, pachovala pachifuwa chachiweruzo, pamene akulowa m’Malo Oyera kuti chikhale chikumbutso pamaso pa Yehova nthawi zonse.
30 Ndiyeno uike Urimu+ ndi Tumimu m’chovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamalowa kukaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula ziweruzo+ za ana a Isiraeli pamtima pake poonekera kwa Yehova nthawi zonse.
31 “Ndiyeno upange malaya odula manja ndi ulusi wabuluu wokhawokha, ovala mkati mwa efodi.+
32 Malayawo akhale otsegula pamwamba pake, pakatikati. Potsegulapo pakhale popenderera m’mphepete mwake ndi nsalu yowomba. Pakhale potsegula ngati chovala cha kunkhondo chamamba achitsulo, kuti pasang’ambike.+
33 Mumpendero wake wa m’munsi upangemo makangaza* a ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri kuzungulira mpenderowo. Upangenso mabelu+ agolide pakati pa makangazawo kuzungulira mpenderowo.
34 Pakhale belu lagolide ndi khangaza, belu lagolide ndi khangaza kuzungulira mpendero wa m’munsi mwa malaya odula manjawo.+
35 Aroni azivala zimenezo kuti atumikire, ndipo mabeluwo azimveka iye akamalowa m’malo opatulika pamaso pa Yehova ndi pamene akutuluka, kuti asafe.+
36 “Upangenso kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, ndipo ulembepo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo, mawu akuti, ‘Chiyero n’cha Yehova.’+
37 Kachitsulo kameneko ukamangirire panduwira+ ndi chingwe chabuluu. Kazikhala patsogolo pa nduwirayo.
38 Chotero kachitsuloko kazikhala pamphumi pa Aroni, ndipo Aroni aziyankha mlandu wa machimo ochimwira zinthu zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli adzaziyeretsa. Izi ndizo mphatso zawo zonse zopatulika. Kachitsuloko kazikhala pamphumi pake nthawi zonse, kuti azichititsa anthuwo kukhala ovomerezeka+ pamaso pa Yehova.
39 “Kenako uwombe mkanjo wamandalasi ndi ulusi wabwino kwambiri. Upangenso nduwira ya nsalu yabwino kwambiri,+ ndiponso uwombe lamba+ wa mkanjo.
40 “Ana a Aroni uwapangire mikanjo+ ndi malamba ake. Uwapangirenso mipango*+ yokulunga kumutu kuti iwapatse ulemerero ndi kuwakongoletsa.+
41 Ndipo uveke Aroni m’bale wako pamodzi ndi ana ake zinthu zimenezi. Ukatero uwadzoze,+ uwapatse mphamvu*+ ndi kuwayeretsa, ndipo atumikire monga ansembe anga.
42 Ndipo uwapangire makabudula ansalu ofika m’ntchafu kuti azibisa maliseche awo.+
43 Aroni ndi ana ake azivala makabudula amenewa polowa m’chihema chokumanako kapena popita kuguwa lansembe kukatumikira pamalo oyera, kuti asapalamule mlandu ndi kufa. Limeneli ndi lamulo kwa iye ndi mbadwa zake mpaka kalekale.+
Mawu a M'munsi
^ Umenewu ndi utali wofanana ndi utali wochokera pansonga ya chala chamanthu cha dzanja lanu kudutsa pakati pa chikhatho chanu, kukafika pansonga ya chala chaching’ono, mutatambasula chikhatho. Utali umenewu ndi wokwana masentimita 22.2.
^ “Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ M’Chiheberi mawu amenewa kwenikweni amatanthauza “kudzaza manja,” ndipo amatchulidwa ponena za kupatsa mphamvu zonse anthu oti azitumikira monga ansembe.