Ekisodo 24:1-18
24 Choncho Mulungu anauza Mose kuti: “Kwera upite kwa Yehova, iweyo, Aroni, Nadabu, Abihu+ ndi akulu 70+ a Isiraeli, ndipo mugwade chapatali.
2 Mose yekha ayandikire kwa Yehova, koma enawo asayandikire. Anthu ena onse asakwere m’phiri.”+
3 Ndiyeno Mose anapita kwa anthu ndi kuwafotokozera mawu onse a Yehova ndi zigamulo zake zonse.+ Pamenepo anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.”+
4 Choncho Mose analemba mawu onse a Yehova.+ Ndiyeno anadzuka m’mawa kwambiri n’kumanga guwa lansembe ndi zipilala 12 zoimira mafuko 12 a Isiraeli, m’tsinde mwa phiri.+
5 Kenako anatuma anyamata a Isiraeli ndipo anyamatawo anapereka nsembe zopsereza komanso anapereka ng’ombe kuti zikhale nsembe zachiyanjano+ kwa Yehova.
6 Pamenepo Mose anatenga hafu ya magazi ndi kuwaika m’mbale zolowa,+ ndipo hafu inayo anawaza paguwa lansembe.+
7 Ndiyeno anatenga buku la pangano+ ndi kuwerengera anthuwo kuti amve.+ Zitatero anthuwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”+
8 Pamenepo Mose anatenga magaziwo ndi kuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndiwo magazi okhazikitsira pangano+ limene Yehova wapangana nanu mwa mawu onsewa.”
9 Choncho Mose, Aroni, Nadabu, Abihu ndi akulu 70 a Isiraeli anakwera m’phirimo,
10 ndipo anaona Mulungu wa Isiraeli.+ Pansi pa mapazi ake panali chinthu chooneka ngati miyala ya safiro yoyalidwa bwino, choyera ngati kumwamba.+
11 Mulungu sanawononge atsogoleri amenewo a ana a Isiraeli,+ koma iwo anaona masomphenya a Mulungu woona+ ndipo anadya ndi kumwa.+
12 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Kwera m’phiri muno ufike kwa ine ndi kukhala momwe muno, pakuti ndikufuna kukupatsa miyala yosema imene ndalembapo chilamulo kuti ndiphunzitse anthu.”+
13 Choncho Mose ndi Yoswa mtumiki wake ananyamuka, ndipo Mose anakwera m’phiri la Mulungu woona.+
14 Koma Mose anali atauza akuluwo kuti: “Tidikireni pompano mpaka titabwerako.+ Panotu muli ndi Aroni ndi Hura.+ Aliyense amene ali ndi mlandu wofuna kuweruzidwa afikire iwowa.”+
15 Motero Mose anakwera m’phirimo, mtambo utakuta phirilo.+
16 Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakutabe phirilo kwa masiku 6. Ndiyeno pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo.+
17 Kwa ana a Isiraeli, ulemerero wa Yehova unali kuoneka ngati moto wolilima+ pamwamba pa phiri.
18 Kenako Mose analowa mumtambomo ndi kukwera m’phirimo.+ Mose anakhala mmenemo masiku 40, usana ndi usiku.+