Ekisodo 23:1-33

23  “Usafalitse nkhani yabodza.+ Usagwirizane ndi munthu woipa mwa kukhala mboni yokonzera wina zoipa.+  Usatsatire khamu pochita zoipa.+ Pa mlandu usapereke umboni wopotoza chilungamo potsatira khamu la anthu.+  Usakondere munthu wosauka pa mlandu wake.+  “Ukapeza ng’ombe kapena bulu wa mdani wako atasochera, um’bweze ndithu kwa mwiniwake.+  Ukaona bulu wa munthu wodana nawe atagona pansi polemedwa ndi katundu, pamenepo usam’siye yekha munthu wodana naweyo. Uthandizane naye kumasula katunduyo.+  “Usapotoze chigamulo cha munthu wosauka wokhala pakati panu, pa mlandu wake.+  “Utalikirane ndi mawu onama.+ Usaphe munthu wosalakwa ndi munthu wolungama, chifukwa woipa sindidzamuyesa wolungama.+  “Usalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+  “Usapondereze mlendo wokhala pakati panu,+ popeza mukudziwa mmene zimakhalira ukakhala mlendo, chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+ 10  “Kwa zaka 6 uzilima munda wako ndi kukolola.+ 11  Koma chaka cha 7 usaulime, uusiye kuti ugonere.+ Osauka mwa anthu ako adye za m’mundamo ndipo zimene iwo asiya, zilombo zakutchire zidye.+ Uzichita zimenezi ndi munda wako wa mpesa ndi wa maolivi. 12  “Uzigwira ntchito masiku 6.+ Koma tsiku la 7 usamagwire ntchito, kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zizipuma, ndipo mwana wa kapolo wako wamkazi ndi mlendo azipumula.+ 13  “Muzisamalira zonse zimene ndakuuzani,+ ndipo musatchule dzina la milungu ina. Lisamveke pakamwa panu.+ 14  “Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+ 15  Muzichita chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda chofufumitsa+ masiku 7 pa nthawi yake m’mwezi wa Abibu,*+ monga momwe ndakulamulirani, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi umenewu. Ndipo palibe ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+ 16  Komanso muzichita chikondwerero cha zokolola, chokondwerera zipatso za ntchito ya manja anu zoyamba kucha+ zimene munabzala m’munda.+ Muzichitanso chikondwerero cha kututa kumapeto kwa chaka, pamene mututa zipatso za manja anu, zam’munda.+ 17  Katatu pa chaka mwamuna aliyense pakati panu azionekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova.+ 18  “Popereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. Ndipo mafuta a chikondwerero changa asamagone mpaka m’mawa.+ 19  “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+ “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+ 20  “Tsopano ndikukutumizira mngelo+ wokutsogolera kuti akuteteze m’njira ndi kukakulowetsa m’dziko limene ndakukonzera.+ 21  Samala ndipo umvere mawu ake. Usam’pandukire, chifukwa sadzalekerera zolakwa zanu,+ pakuti dzina langa lili mwa iye. 22  Koma ukalabadiradi mawu ake ndi kuchitadi zonse zimene ine ndidzanena,+ pamenepo ndidzalusira adani ako ndi kuvutitsa okuvutitsa.+ 23  Pakuti mngelo wanga adzakutsogolera ndi kukulowetsa m’dziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawafafaniza ndithu.+ 24  Usaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo usapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo,+ koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ 25  Muzitumikira Yehova Mulungu wanu,+ ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi.+ Ndipo ndidzachotsa matenda pakati panu.+ 26  M’dziko lanu simudzapezeka mkazi wopititsa padera kapena wosabereka.+ Ndipo ndidzachulukitsa masiku anu.+ 27  “Iwe usanafike, ndidzachititsa anthu kumva za ine+ ndipo adzanjenjemera. Ndidzasokoneza anthu onse amene udzawapeze. Adani ako onse adzachita mantha ndipo adzathawa.*+ 28  Iwe usanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso pako.+ 29  Sindidzawathamangitsa pamaso pako m’chaka chimodzi, kuti dzikolo lingakhale bwinja ndi kuti zilombo zakutchire zingachuluke ndi kukuvutitsa.+ 30  Ndidzawathamangitsa pamaso pako pang’onopang’ono kufikira mutaberekana ndi kulanda dzikolo.+ 31  “Dziko limene ndidzakupatsa lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita izi, chifukwa anthu okhala m’dzikomo ndidzawapereka m’manja mwako, ndipo iwe udzawathamangitsa pamaso pako.+ 32  Usachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo.+ 33  Asakhale m’dziko lako, kuti asakuchimwitse pamaso panga. Ukatumikira milungu yawo, umenewo udzakhala msampha kwa iwe.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.
Mawu ake enieni, “Ndidzakupatsa kumbuyo kwa makosi a adani ako onse.”
Mabaibulo a Septuagint ndi Vulgate amanena kuti, “ndidzatumizira anthuwo mavu.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.