Ekisodo 32:1-35

32  Mose ali m’phirimo, anthu anaona kuti akuchedwa kutsika.+ Chotero anthuwo anasonkhana kwa Aroni ndi kumuuza kuti: “Tipangire mulungu woti atitsogolere,+ chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.”+  Pamenepo Aroni anawauza kuti: “Vulani ndolo* zagolide+ zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mubwere nazo kwa ine.”  Choncho anthu onse anayamba kuvula ndolo zagolide zimene anavala ndi kuzipereka kwa Aroni.  Pamenepo iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anam’panga+ kukhala fano la mwana wa ng’ombe+ lopangidwa ndi golide wosungunula. Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+  Aroni ataona zimenezi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa fanolo. Kenako iye anafuula kuti: “Mawa kuli chikondwerero cha Yehova.”  Choncho pa tsiku lotsatira, anthuwo anadzuka m’mamawa, ndi kuyamba kupereka nsembe zopsereza ndi zachiyanjano. Atatero, iwo anakhala pansi ndi kudya ndiponso kumwa. Kenako anaimirira n’kuyamba kusangalala.+  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Pita, tsika, chifukwa anthu ako amene unawatsogolera potuluka m’dziko la Iguputo achita zinthu zowawonongetsa.+  Apatuka mofulumira panjira imene ndawalamula kuyendamo.+ Iwo adzipangira fano la mwana wa ng’ombe lopangidwa ndi golide wosungunula. Akuligwadira ndi kupereka nsembe kwa fanolo, ndipo akunena kuti, ‘Aisiraeli inu, uyu ndiye Mulungu wanu amene anakutsogolerani potuluka m’dziko la Iguputo.’”+  Yehova anauzanso Mose kuti: “Ndawayang’ana anthu amenewa, ndipo ndaona kuti ndi anthu ouma khosi.+ 10  Ndileke tsopano kuti mkwiyo wanga uwayakire ndipo ndiwafafanize,+ koma iwe ndikupange kukhala mtundu waukulu.”+ 11  Pamenepo Mose anakhazika pansi mtima wa Yehova Mulungu wake.+ Iye anati: “N’chifukwa chiyani, inu Yehova, mukufuna kuti mkwiyo wanu+ uyakire anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Iguputo mwa mphamvu zazikulu ndiponso ndi dzanja lamphamvu? 12  Aiguputo+ anenerenji kuti, ‘Anawatulutsa m’dziko lino kuti akawaphe kumapiri ndi kuwafafaniza padziko lapansi’?+ Bwezani mkwiyo wanu woyaka motowo,+ ndipo mverani chisoni+ anthu anu kuti musawagwetsere tsoka. 13  Kumbukirani Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli atumiki anu, amene munawalumbirira pa inu mwini,+ powauza kuti, ‘Ndidzachulukitsa mbewu yanu ngati nyenyezi zakumwamba,+ ndipo dziko lonseli limene ndalipatula ndidzalipereka kwa mbewu yanu,+ kuti likhale lawo mpaka kalekale.’”+ 14  Pamenepo, Yehova anayamba kumva chisoni chifukwa cha tsoka limene ananena kuti agwetsera anthu ake.+ 15  Kenako, Mose anatembenuka n’kutsika m’phirimo+ atanyamula miyala yosema ya Umboni+ m’manja mwake. Miyalayo inali yolembedwapo mawu mbali zonse ziwiri. Inali yolembedwapo mawu mbali iyi ndi mbali inayo. 16  Miyalayo inapangidwa ndi Mulungu, ndipo mawuwo analembedwapo ndi Mulungu mochita kugoba.+ 17  Ndiyeno Yoswa anayamba kumva phokoso la kufuula kwa anthu, chotero anauza Mose kuti: “Kukumveka phokoso lankhondo+ kumsasa.” 18  Koma Mose anati:“Limeneli si phokoso la nyimbo ya kupambana,+Komanso si nyimbo yachisoni chifukwa chogonjetsedwa;Ndikumva ngati ndi kuimba kwa mtundu wina.” 19  Chotero atayandikira msasawo n’kuona mwana wa ng’ombe+ ndi anthu akuvina, mkwiyo wa Mose unayaka ndipo nthawi yomweyo anaponya pansi miyala ija ndi kuiswa ali m’tsinde mwa phiri.+ 20  Ndiyeno anatenga mwana wa ng’ombe amene iwo anapanga n’kumutentha ndi moto ndi kum’pera mpaka atakhala fumbi.+ Kenako anamwaza fumbilo pamadzi+ ndi kuwamwetsa Aisiraeli.+ 21  Atatero, Mose anafunsa Aroni kuti: “Kodi anthuwa akuchitira chiyani kuti udzetse tchimo lalikulu chonchi pa iwo?” 22  Ndipo Aroni anayankha kuti: “Mkwiyo wa mbuyanga usayake. Inuyo mukuwadziwa bwino anthuwa, kuti amakonda kuchita zoipa.+ 23  Iwo anandiuza kuti, ‘Tipangire mulungu woti atitsogolere,+ chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.’ 24  Choncho ndinawauza kuti, ‘Ndani wavala zagolide? Avule zimenezo ndi kundipatsa.’ Ndiyeno golideyo ndinamuponya pamoto n’kusanduka mwana wa ng’ombe ameneyu.” 25  Mose anaona kuti anthuwo akuchita zinthu motayirira, chifukwa Aroni anawalola kuchita zotayirira+ zomwe zinachititsa adani awo kuwatonza.+ 26  Ndiyeno Mose anakaima pachipata cha msasawo, ndipo anati: “Ndani ali kumbali ya Yehova? Abwere kwa ine!”+ Ndipo ana onse aamuna a Levi anayamba kusonkhana kwa Mose. 27  Pamenepo iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Aliyense wa inu amange lupanga lake m’chiuno mwake. Ndiyeno mudutse mkati mwa msasa ndi kuyenda mobwerezabwereza, kuchoka pachipata china kufika pachipata china, ndipo aliyense wa inu aphe m’bale wake, mnzake ndi mnzake wapamtima.’”+ 28  Pamenepo ana a Levi+ anachita zimene Mose anawauza, moti patsiku limenelo anthu pafupifupi 3,000 anaphedwa. 29  Zitatero Mose anati: “Dzilimbitseni* lero kuti muchite utumiki kwa Yehova,+ chifukwa aliyense wa inu waukira mwana wake ndi m’bale wake,+ kuti Mulungu akupatseni dalitso lero.”+ 30  Pa tsiku lotsatira, Mose anati kwa anthuwo: “Inuyo mwachita tchimo lalikulu.+ Choncho ndikwera kupita kwa Yehova kuti mwina ndikakam’chonderera angakukhululukireni tchimo lanu.”+ 31  Choncho Mose anabwerera kwa Yehova ndi kunena kuti: “Aa, anthuwa achita tchimo lalikulu, chifukwa adzipangira mulungu wagolide!+ 32  Komano ngati mukufuna kuwakhululukira tchimo lawo,+ . . . koma ngati simukufuna, ndifafanizeni+ chonde, m’buku lanu+ limene mwalemba.” 33  Komabe Yehova anauza Mose kuti: “Amene wandichimwirayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.+ 34  Tsopano atsogolere anthuwa kumalo amene ndakuuza. Taona! Mngelo wanga akhala patsogolo panu,+ ndipo pa tsiku langa lopereka chilango, ndidzawalangadi chifukwa cha tchimo lawo.”+ 35  Ndipo Yehova anagwetsera mliri pa anthuwo chifukwa cha mwana wa ng’ombe amene iwo anam’panga kudzera mwa Aroni.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masikiyo.”
Mawu ake enieni “dzazani manja anu ndi mphamvu.”