Ekisodo 25:1-40
25 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:+
2 “Uza ana a Isiraeli kuti apereke zopereka kwa ine. Anthu inu mulandire zopereka zanga kwa munthu aliyense amene mtima wake wamulimbikitsa.+
3 Zopereka zimene muyenera kulandira kwa iwo ndi izi: golide,+ siliva,+ mkuwa,+
4 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ubweya wa mbuzi.+
5 Mulandirenso kwa iwo zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe,+
6 mafuta a nyale,+ mafuta a basamu+ opangira mafuta odzozera,+ ndi zofukiza zonunkhira.+
7 Komanso mulandire miyala ya onekisi ndi miyala yozika pa efodi*+ ndi pachovala pachifuwa.+
8 Ndipo mundipangire malo opatulika, popeza ndiyenera kukhala pakati panu.+
9 Mukapange chihema chopatulika ndi ziwiya zake mogwirizana ndendende ndi zonse zimene ndikukusonyeza.+
10 “Mundipangire Likasa la mtengo wa mthethe,+ mikono* iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi, ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.
11 Kenako ulikute ndi golide woyenga bwino.+ Mkati ndi kunja komwe ulikute ndi golide, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+
12 Ulipangire mphete zinayi zagolide ndi kuziika pamwamba pa miyendo yake inayi. Mphete ziwiri zikhale mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zikhale mbali inayo.+
13 Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide.+
14 Ulowetse mitengo yonyamulirayo mumphete zija za m’mbali mwa Likasa kuti azinyamulira Likasalo.
15 Mitengo yonyamulirayo izikhala mumphete za Likasalo. Isachotsedwemo.+
16 M’Likasamo uikemo umboni umene ndidzakupatsa.+
17 “Kenako upange chivundikiro chagolide woyenga bwino, mikono iwiri ndi hafu m’litali, ndi mkono umodzi ndi hafu m’lifupi.+
18 Upangenso akerubi awiri agolide. Akhale osula ndipo uwaike kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+
19 Uike kerubi mmodzi kumbali imodzi ya chivundikirocho ndi kerubi wina kumbali inayo.+ Akerubiwo uwaike kumbali zonse ziwiri za chivundikirocho.
20 Ndipo akweze mapiko awo m’mwamba ali otambasula, aphimbe chivundikirocho ndi mapiko awo, ndipo akhale moyang’anizana,+ koma nkhope zawo ziweramire pachivundikiro.
21 Chivundikirocho+ uchiike pamwamba pa Likasalo, ndipo m’Likasamo uikemo umboni umene ndidzakupatsa.
22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo ndi kulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikiro,+ pakati pa akerubi awiriwo amene ali pamwamba pa likasa la umboni. Kuchokera pamenepo ndidzakulamula zonse zokhudza ana a Isiraeli.+
23 “Ndiyeno upange tebulo+ la mtengo wa mthethe, mikono iwiri m’litali, mkono umodzi m’lifupi ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.
24 Ulikute ndi golide woyenga bwino, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.+
25 Ulipangirenso felemu, muyezo wake chikhatho* chimodzi m’lifupi mwake. Felemuli lizungulire tebulo lonse ndipo upange mkombero wagolide pafelemulo.+
26 Tebulolo ulipangire mphete zinayi zagolide ndi kuziika m’makona ake anayi mmene muli miyendo yake inayi.+
27 Mphetezo zikhale pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa mitengo yonyamulira tebulolo.+
28 Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide. Mitengo imeneyi azinyamulira tebulolo.+
29 “Ndiyeno upange mbale zake, zikho, mitsuko ndi mbale zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Uzipange ndi golide woyenga bwino.+
30 Ndipo patebulopo uziikapo mkate wachionetsero pamaso panga nthawi zonse.+
31 “Kenako upange choikapo nyale chagolide woyenga bwino. Chimenechi chikhale chosula.+ Choikapo nyalecho chikhale ndi tsinde, nthambi, masamba ofunga duwa, mfundo ndi maluwa.
32 Choikapo nyalecho chikhale ndi nthambi 6, kumbali ina kutuluke nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kutulukenso nthambi zitatu.+
33 Pamalo atatu a nthambi za mbali imodzi, pakhale masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa. Pamalo atatu a nthambi za mbali inayo, pakhalenso masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa.+ Nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyalecho zikhale zotero.
34 Ndipo pamalo anayi a choikapo nyalecho pakhale masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa.+
35 Mfundo imodzi ikhale pansi pa nthambi zake ziwiri, mfundo ina ikhalenso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mfundo inanso ikhale pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zikhale choncho ndi nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyale.+
36 Choikapo nyalecho chikhale ndi mfundo ndi nthambi. Chonsechi chisulidwe monga chiwiya chimodzi, chagolide woyenga bwino.+
37 Ndipo uchipangire nyale 7. Nyalezo ziziyatsidwa kuti ziziunikira patsogolo pake.+
38 Zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale, zikhale zagolide woyenga bwino.+
39 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi azipange pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente limodzi.*
40 Uonetsetse kuti wazipanga motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa m’phiri.+
Mawu a M'munsi
^ Katumbu ndi nyama yaubweya ya m’madzi, ndipo katumbu amene akutchulidwa pano ndi mtundu waukulu wa akatumbu amene amapezeka m’nyanja zikuluzikulu.
^ Zikuoneka kuti chimenechi chinali chovala chofanana ndi epuloni, ndipo chinali ndi nsalu yakutsogolo ndi yakumbuyo. Onani Zakumapeto 14.
^ “Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
^ “Chikhatho” chimenechi chinali muyezo wokwana masentimita 7.4.
^ “Talente limodzi” limalemera makilogalamu pafupifupi 34.2.