Ekisodo 1:1-22
1 Pamene Yakobo, kapena kuti Isiraeli anapita ku Iguputo, aliyense mwa ana ake aamuna anapitanso limodzi ndi banja lake. Mayina a ana a Yakobowo ndi awa:+
2 Rubeni,+ Simiyoni,+ Levi,+ Yuda,+
3 Isakara,+ Zebuloni,+ Benjamini,+
4 Dani,+ Nafitali,+ Gadi+ ndi Aseri.+
5 Yosefe anali kale ku Iguputo.+ Anthu onse otuluka m’chiuno mwa Yakobo+ analipo 70.
6 Patapita nthawi Yosefe anamwalira.+ Ndipo abale ake onse ndi m’badwo wonsewo anamwaliranso.
7 Ana a Isiraeli anaberekana ndipo anachuluka m’dzikomo. Iwo anapitiriza kuchulukana ndi kukhala amphamvu koposa, moti anadzaza m’dzikomo.+
8 Patapita nthawi, mfumu ina yomwe sinam’dziwe Yosefe inayamba kulamulira mu Iguputo.+
9 Mfumuyo inauza anthu ake kuti: “Taonani! Ana a Isiraeli achuluka kwambiri ndipo ndi amphamvu kuposa ife.+
10 Tiyeni tiwachenjerere,+ kuti asapitirize kuchulukana kuopera kuti pa nthawi ya nkhondo angadzagwirizane ndi adani athu ndi kumenyana nafe n’kuchoka m’dziko lino.”
11 Choncho anawaikira akulu owayang’anira pa ntchito yawo yaukapolo, kuti aziwanyamulitsa katundu mwankhanza.+ Ndipo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramese+ kuti ikhale mosungiramo zinthu.*
12 Koma pamene anali kuwazunza kwambiri m’pamenenso anali kuwonjezeka ndi kufalikira mowirikiza, mwakuti Aiguputo anachita mantha kwambiri ndi ana a Isiraeliwo.+
13 Chotero, Aiguputo anagwiritsa ana a Isiraeli ntchito yaukapolo mwankhanza.+
14 Iwo anasautsa moyo wa Aisiraeliwo powagwiritsa ntchito yowawa yaukapolo, yomwe inali yoponda matope+ ndi kuumba njerwa.* Anawagwiritsa ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse m’munda,+ ndi ukapolo wa mtundu uliwonse umene anatha kuwagwiritsa ntchito mwankhanza.+
15 Kenako mfumu ya Iguputo inalamula azamba*+ achiheberi, mmodzi wotchedwa Sifira ndipo wina wotchedwa Puwa,
16 kuti: “Pamene mukuthandiza amayi achiheberi kubereka, mukaona kuti mwana akubadwayo ndi wamwamuna muzimupha, koma ngati ndi wamkazi muzimusiya wamoyo.”
17 Koma, azambawo anali oopa Mulungu+ woona, ndipo sanachite zimene mfumu ya Iguputo inawauza.+ M’malomwake, ana aamuna anali kuwasiya amoyo.+
18 Patapita nthawi, mfumu ya Iguputo inaitana azamba aja ndi kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ana aamuna mwakhala mukuwasiya amoyo? Mwachitiranji zimenezi?”+
19 Poyankha azambawo anauza Farao kuti: “Amayi achiheberi sali ngati amayi achiiguputo. Popeza amayi achiheberi ndi amphamvu, mzamba asanafike iwo amakhala atabereka kale.”
20 Chotero Mulungu anawadalitsa azambawo,+ ndipo ana a Isiraeli anapitiriza kuwonjezeka ndi kukhala amphamvu.
21 Choncho chifukwa chakuti azambawo anaopa Mulungu woona, m’kupita kwa nthawi iye anawadalitsa ndi mabanja awoawo.+
22 Kenako Farao analamula anthu ake onse kuti: “Mwana aliyense wamwamuna wa Aheberi wobadwa kumene, muzim’ponya mumtsinje wa Nailo, koma mwana aliyense wamkazi muzimusiya wamoyo.”+
Mawu a M'munsi
^ M’mizinda imeneyi anamangamo nkhokwe ndi nyumba zina zosungiramo chakudya ndi zinthu zina.
^ Zimenezi zinali njerwa zosawotcha.