Miyambo 13:1-25

13  Mwana amakhala wanzeru ngati akulandira malangizo* kuchokera kwa bambo ake.+ Koma amene sanamve chidzudzulo amakhala wonyoza.+  Munthu adzadya zipatso zabwino kuchokera pa zipatso za pakamwa pake.+ Koma moyo wa anthu ochita zachinyengo umalakalaka kuchita chiwawa.+  Amene amayang’anira pakamwa pake amasunga moyo wake.+ Amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+  Waulesi amalakalaka zinthu, chonsecho moyo wake ulibe chilichonse.+ Koma anthu akhama adzanenepa.+  Wolungama amadana ndi lilime lonama,+ koma anthu oipa amachita zinthu zochititsa manyazi ndipo amadzibweretsera manyazi.+  Chilungamo chimateteza munthu amene sachita zopweteka ena,+ koma wochimwa amawonongedwa ndi zoipa.+  Pali munthu amene amadzionetsera kuti ndi wolemera koma alibe kalikonse.+ Ndiponso pali munthu amene amaoneka ngati wosauka koma ali ndi zinthu zambiri zamtengo wapatali.  Moyo wa munthu udzawomboledwa ndi chuma chake,+ koma munthu wosauka sadzudzulidwa.+  Kuwala kwa anthu olungama kudzawachititsa kusangalala.+ Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+ 10  Chifukwa cha kudzikuza, munthu amangoyambitsa mavuto,+ koma anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.+ 11  Zinthu zamtengo wapatali zimene zimapezedwa m’njira yachinyengo zimacheperachepera,+ koma wozisonkhanitsa ndi dzanja lake ndi amene amazichulukitsa.+ 12  Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.+ Koma chomwe unali kufuna chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.+ 13  Wokana kusunga mawu,+ wangongole adzamulanda chikole. Koma munthu amene amaopa lamulo ndiye adzalandire mphoto.+ 14  Lamulo la munthu wanzeru ndilo kasupe wa moyo,+ chifukwa limapulumutsa munthu kumisampha ya imfa.+ 15  Munthu wozindikira bwino, anthu amam’komera mtima.+ Koma njira ya anthu ochita zachinyengo imakhala yodzaza ndi zopweteka ndiponso mavuto.+ 16  Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira,+ koma wopusa amafalitsa uchitsiru.+ 17  Mthenga woipa amayambitsa mavuto,+ koma nthumwi yokhulupirika imachiritsa.+ 18  Munthu wonyalanyaza malangizo amasauka ndipo amadzichotsera ulemu.+ Koma amene amamvera chidzudzulo ndi amene amalemekezedwa.+ 19  Zimene umakhumba zikapezeka, moyo umasangalala.+ Koma opusa, kusiya zoipa kumawanyansa.+ 20  Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru,+ koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.+ 21  Tsoka limatsatira ochimwa,+ koma olungama ndi amene amalandira mphoto zabwino.+ 22  Munthu wabwino adzasiyira cholowa zidzukulu zake, ndipo chuma cha wochimwa chimasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+ 23  Munda wa munthu wosauka akaulima umatulutsa chakudya chochuluka,+ koma pali munthu amene wasesedwa chifukwa chosowa chilungamo.+ 24  Munthu wosakwapula mwana wake ndiye kuti akumuda,+ koma womukonda ndi amene amamuyang’anira kuti amulangize.+ 25  Wolungama amadya n’kukhuta,+ koma mimba za anthu oipa zidzakhala zopanda kanthu.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.