Miyambo 8:1-36

8  Nzerutu ikungokhalira kufuula,+ ndipo kuzindikira kukungokhalira kutulutsa mawu.+  Imaima pamwamba pa zitunda,+ m’mbali mwa njira ndi pamphambano za misewu.  Imafuula mokweza+ pambali pa zipata, pakhomo la mzinda ndi polowera kuzipata,+ kuti:  “Ndikufuulira anthu inu, ndipo mawu anga akupita kwa ana a anthu.+  Inu osadziwa zinthu, phunzirani kukhala ochenjera.+ Anthu opusa inu, pezani mtima womvetsa zinthu.+  Mvetserani chifukwa ndikulankhula zinthu zofunika kwambiri.+ Ndikutsegula pakamwa panga kuti ndinene zowongoka.+  Pakuti pakamwa panga pamalankhula choonadi motsitsa,+ ndipo milomo yanga imaipidwa ndi zoipa.+  Mawu onse otuluka pakamwa panga ndi olungama.+ Pa mawu anga palibe zokhota kapena zopotoka.+  Mawu anga onse ndi osavuta kumva kwa wozindikira, ndipo ndi owongoka kwa anthu odziwa zinthu.+ 10  Landirani malangizo* anga osati siliva, ndiponso kudziwa zinthu m’malo mwa golide wabwino kwambiri.+ 11  Pakuti nzeru n’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,+ ndipo zosangalatsa zonse sizingafanane nazo.+ 12  “Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera,+ ndimadziwa zinthu, ndiponso ndimatha kuganiza bwino.+ 13  Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+ 14  Ine ndili ndi malangizo+ ndi nzeru zopindulitsa.+ Ndimamvetsa zinthu,+ ndiponso ndili ndi mphamvu.+ 15  Chifukwa cha ine, mafumu amalamulira. Nazonso nduna zapamwamba zimakhazikitsa malamulo olungama.+ 16  Chifukwa cha ine, akalonga amalamulira,+ ndipo anthu onse olemekezeka amaweruza mwachilungamo.+ 17  Amene amandikonda, inenso ndimawakonda.+ Amene amandifunafuna ndi amene amandipeza.+ 18  Chuma ndi ulemerero zili ndi ine.+ Ndilinso ndi cholowa chamtengo wapatali ndi chilungamo.+ 19  Zipatso zanga n’zabwino kuposa golide. N’zoposa ngakhale golide woyengedwa bwino. Zokolola zanga n’zoposa siliva wabwino kwambiri.+ 20  Ndimayenda m’njira yachilungamo,+ komanso pakati pamisewu yachilungamo,+ 21  kuti ndichititse amene amandikonda kulandira zinthu zamtengo wapatali,+ ndipo ndimadzazitsa nkhokwe zawo.+ 22  “Yehova anandipanga monga chiyambi cha njira yake.+ Ine ndiye ntchito yoyambirira pa ntchito zake zimene anakwaniritsa kalekale kwambiri.+ 23  Ndinakhazikitsidwa kuyambira nthawi yosadziwika,+ kuyambira pa chiyambi, kuyambira nthawi zakale kuposa dziko lapansi.+ 24  Ndinabadwa ndi ululu wa pobereka kulibe madzi akuya,+ kulibe akasupe odzaza madzi. 25  Mapiri akuluakulu asanakhazikitsidwe,+ mapiri ang’onoang’ono asanakhalepo, ine ndinabadwa ndi ululu wa pobereka, 26  iye asanapange dziko lapansi,+ zigwa zopanda kanthu, ndi zibuma zoyamba za dothi lachonde la padziko lapansi.+ 27  Pamene anali kukonza kumwamba, ine ndinali pomwepo.+ Pamene anakhazikitsa lamulo lakuti pamwamba pa madzi akuya pazioneka pozungulira,+ 28  pamene analimbitsa mitambo yakumwamba,+ pamene anachititsa kuti akasupe a madzi akuya akhale olimba,+ 29  pamene anaikira nyanja lamulo lake lakuti madzi ake asapitirire pamene anawalamula,+ pamene anakhazikitsa maziko a dziko lapansi,+ 30  ine ndinali pambali pake monga mmisiri waluso.+ Tsiku ndi tsiku, iye anali kusangalala kwambiri ndi ine.+ Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.+ 31  Ndinali kusangalala ndi nthaka ya dziko lake lapansi,+ ndipo zinthu zimene zinali kundisangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.+ 32  “Tsopano ananu, ndimvereni. Ndithu, odala ndiwo amene amasunga njira zanga.+ 33  Mverani malangizo kuti mukhale anzeru,+ ndipo musawanyalanyaze.+ 34  Wodala ndi munthu amene amandimvetsera mwa kukhala maso pamakomo anga tsiku ndi tsiku, mwa kuyang’anitsitsa pamafelemu a makomo anga.+ 35  Pakuti wondipeza ine, ndithu adzapezanso moyo+ ndipo Yehova adzasangalala naye,+ 36  koma wolephera kundipeza akupweteka moyo wake.+ Onse odana ndi ine ndiye kuti amakonda imfa.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.