Miyambo 17:1-28
17 Kukhala ndi mkate wouma pali bata,+ kuli bwino kuposa nyumba yodzaza ndi nyama yansembe pali mkangano.+
2 Wantchito wochita zinthu mozindikira, adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi,+ ndipo adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.+
3 Siliva amamuyengera m’mbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera m’ng’anjo,+ koma Yehova ndiye amene amayesa mitima.+
4 Wochita zoipa amamvetsera mlomo wolankhula zopweteka ena.+ Wonama amamvetsera lilime loyambitsa mavuto.+
5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+
6 Chisoti chaulemu cha anthu okalamba ndicho zidzukulu zawo,+ ndipo ana amalemekezeka ndi bambo awo.+
7 Munthu aliyense wopusa, mlomo wowongoka sumuyenera.+ Ndiye kuli bwanji mlomo wachinyengo kwa munthu wolemekezeka?+
8 Mphatso ndiyo mwala wamtengo wapatali m’maso mwa mwiniwake wolemekezeka.+ Kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera bwino.+
9 Wophimba machimo akufunafuna chikondi,+ ndipo amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.+
10 Kudzudzula kumam’fika pamtima munthu womvetsa zinthu,+ kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+
11 Woipa amangofunafuna kupanduka,+ ndipo munthu amene watumidwa kuti akamulange sam’chitira chifundo.+
12 Ndi bwino kukumana ndi chimbalangondo chimene ana ake asowa,+ kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru chochita zopusa.+
13 Aliyense wobwezera zoipa pa zabwino,+ zoipa sizidzachoka panyumba pake.+
14 Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo.+ Choncho mkangano usanabuke, chokapo.+
15 Aliyense wonena kuti munthu woipa ndi wolungama+ ndiponso aliyense wonena kuti munthu wolungama ndi woipa,+ onsewa ndi onyansa kwa Yehova.+
16 N’chifukwa chiyani munthu wopusa ali ndi njira yopezera nzeru,+ chonsecho alibe zolinga zabwino?*+
17 Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse,+ ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.+
18 Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amagwirana chanza ndi munthu wina,+ ndipo amalonjeza pamaso pa mnzake kuti iye akhala chikole.+
19 Aliyense wokonda machimo akukonda kulimbana.+ Aliyense wotalikitsa khomo lake akufunafuna kuwonongedwa.+
20 Wa mtima wopotoka sadzapeza zabwino,+ ndipo wa lilime lokhota adzagwera m’tsoka.+
21 Bambo wa mwana wopusa amamva chisoni,+ ndipo bambo wa mwana wopanda nzeru sasangalala.+
22 Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa,+ koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.+
23 Woipa amatenga chiphuphu mobisa,+ kuti akhotetse njira za chiweruzo.+
24 Nzeru zimakhala pamaso pa munthu womvetsa zinthu,+ koma maso a munthu wopusa ali kumalekezero a dziko lapansi.+
25 Mwana wopusa amakhumudwitsa bambo ake,+ ndipo amamvetsa chisoni mayi ake amene anam’bereka.+
26 Komanso, kulipiritsa munthu wolungama si bwino.+ Kumenya anthu olemekezeka n’kosayenera.+
27 Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu,+ ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.+
28 Ngakhale munthu wopusa akakhala chete amaoneka ngati wanzeru,+ ndipo wotseka pakamwa pake amaoneka ngati womvetsa zinthu.
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “alibe mtima.”