Miyambo 9:1-18

9  Nzeru yeniyeni+ yamanga nyumba yake.+ Yasema zipilala zake 7.  Yapha nyama yake ndipo yasakaniza vinyo wake. Kuwonjezera apo, yayala patebulo pake.+  Yatuma antchito ake aakazi kuti apite pamwamba pa zitunda za m’mudzi akaiitanire anthu, kuti:  “Aliyense wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense wopanda nzeru mumtima mwake,+ nzeru* ikumuuza kuti:  “Bwerani mudzadye chakudya changa ndiponso mudzamwe nawo vinyo amene ndasakaniza.+  Alekeni anthu osadziwa zinthu kuti mupitirize kukhala ndi moyo,+ ndipo yendani mowongoka m’njira yomvetsa zinthu.”+  Amene amalangiza wonyoza amadzichotsera yekha ulemu,+ ndipo amene amadzudzula woipa amadzibweretsera chilema.+  Usadzudzule wonyoza kuti angadane nawe.+ Dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.+  Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.+ Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira. 10  Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.+ Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.+ 11  Pakuti ine ndidzachititsa kuti masiku ako akhale ambiri+ ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.+ 12  Ngati wakhala wanzeru, nzeruzo zidzapindulitsa iweyo.+ Ngati uli wonyoza, iweyo ndiye udzavutike.+ 13  Mkazi wopusa amakhala wolongolola.+ Iye ndi woperewera nzeru ndipo sadziwa chilichonse.+ 14  Wakhala pampando pakhomo la nyumba yake, pachitunda cha m’mudzimo,+ 15  kuti aziitana anthu odutsa amene akuyenda panjira zawo atalunjika kutsogolo. Iye akuwauza kuti:+ 16  “Aliyense amene ali wosadziwa zinthu apatukire kuno.”+ Aliyense amene ali wopanda nzeru mumtima mwake,+ mkaziyo wamuuza kuti: 17  “Madzi akuba amatsekemera,*+ ndipo mkate wakudya mwakabisira umakoma.”+ 18  Koma mwamunayo sakudziwa kuti kumeneko kuli akufa, ndiponso kuti amene amaitanidwa ndi mkaziyu ali kumalo otsika a ku Manda.+

Mawu a M'munsi

M’Chiheberi, nzeru akuitenga ngati munthu wamkazi m’chaputala chino.
Ena amati “amanzuna.”