Miyambo 19:1-29
19 Wosauka amene akuyenda ndi mtima wosagawanika ali bwino kuposa munthu wa milomo yopotoka,+ komanso munthu wopusa.+
2 Ndiponso, si bwino kuti munthu akhale wosadziwa zinthu,+ ndipo woyenda mofulumira ndi mapazi ake akuchimwa.+
3 Kupusa kwa munthu wochokera kufumbi n’kumene kumapotoza njira yake,+ choncho mtima wake umakwiyira Yehova.+
4 Chuma chimachulukitsa mabwenzi,+ koma munthu wonyozeka amalekanitsidwa ngakhale kwa bwenzi lake.+
5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+ ndipo wolankhula mabodza sadzapulumuka.+
6 Anthu amene amakhazika pansi mtima wa munthu wolemekezeka ndi ambiri,+ ndipo aliyense amakhala bwenzi la munthu wopereka mphatso.+
7 Abale ake onse a munthu wosauka amadana naye,+ komanso anzake amatalikirana naye kwambiri.+ Iye amafuna kuwachonderera, koma iwo amamuthawa.+
8 Munthu amene wapeza mtima wanzeru+ akukonda moyo wake. Wopitiriza kusonyeza kuzindikira amapeza zabwino.+
9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+ ndipo wolankhula mabodza adzawonongedwa.+
10 Aliyense wopusa sayenera moyo wawofuwofu.+ Ndiye kuli bwanji kuti wantchito alamulire akalonga!+
11 Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake,+ ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.+
12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+ koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.+
13 Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake,+ ndipo mkazi wolongolola ali ngati denga* lodontha limene limathawitsa munthu.+
14 Cholowa chochokera kwa makolo ndicho nyumba ndi chuma,+ koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.+
15 Ulesi umachititsa tulo tofa nato,+ ndipo munthu waulesi amakhala ndi njala.+
16 Wosunga lamulo akusunga moyo wake.+ Wosasamala za njira zake adzaphedwa.+
17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+
18 Langa mwana wako padakali chiyembekezo,+ ndipo usalakelake imfa yake.+
19 Wamkwiyo waukulu ayenera kulipitsidwa,+ chifukwa ukam’pulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri.+
20 Mvera uphungu+ ndipo utsatire malangizo* kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo.+
21 Mumtima mwa munthu mumakhala zolinga zambiri,+ koma zolinga za Yehova n’zimene zidzakwaniritsidwe.+
22 Chinthu chosiririka mwa munthu wochokera kufumbi ndicho kukoma mtima kwake kosatha,+ ndipo munthu wosauka ali bwino kuposa munthu wonama.+
23 Kuopa Yehova kumapezetsa moyo.+ Munthu amagona mosatekeseka+ ndipo zoipa sizim’gwera.+
24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera,+ koma n’kulephera kulibweretsa pakamwa.+
25 Menya wonyoza+ kuti wosadziwa zinthu achenjere.+ Ndipo womvetsa zinthu uyenera kum’dzudzula kuti adziwe zinthu zowonjezereka.+
26 Wochitira zoipa bambo ake ndiponso wothamangitsa mayi ake,+ ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.+
27 Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo, ndiye kuti wapatuka pa mawu okudziwitsa zinthu.+
28 Mboni yopanda pake imanyoza chilungamo,+ ndipo pakamwa pa anthu oipa pamameza zinthu zopweteka ena.+
29 Zilango anazikhazikitsira anthu onyoza,+ ndipo zikwapu anazisungira msana wa anthu opusa.+