Miyambo 11:1-31
11 Sikelo yachinyengo imam’nyansa Yehova,+ koma mwala woyezera, wolemera mokwanira, umam’sangalatsa.
2 Kodi kudzikweza kwafika? Ndiye kuti manyazinso afika.+ Koma nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.+
3 Mtima wosagawanika wa anthu owongoka ndi umene umawatsogolera,+ koma kupotoza zinthu kwa anthu ochita zachinyengo kudzawawononga.+
4 Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+
5 Kulungama kwa munthu wopanda cholakwa n’kumene kudzawongole njira yake,+ koma woipa adzagwera m’zoipa zakezo.+
6 Kulungama kwa anthu owongoka mtima n’kumene kudzawapulumutse,+ koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+
7 Munthu woipa akafa, chiyembekezo chake chimawonongeka,+ ndipo zimene anali kuyembekezera kuchokera ku mphamvu zake sizichitika.+
8 Wolungama ndi amene amapulumutsidwa ku zowawa,+ ndipo woipa amalowa m’malo mwake.+
9 Wopanduka amawononga mnzake ndi pakamwa pake,+ koma anthu olungama amapulumutsidwa chifukwa chodziwa zinthu.+
10 Mudzi umakondwera chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,+ koma anthu oipa akawonongeka pamakhala mfuu yachisangalalo.+
11 Mudzi umakwezedwa chifukwa cha madalitso a anthu olungama,+ koma umagwetsedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oipa.+
12 Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amanyoza mnzake,+ koma munthu wozindikira bwino ndi amene amakhala chete.+
13 Amene amayendayenda n’kumanenera ena zoipa+ amaulula zinsinsi za anzake,+ koma wokhulupirika* amabisa nkhani.+
14 Pakakhala popanda malangizo anzeru, anthu amagwa.+ Koma pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.+
15 Munthu amene walonjeza kuti adzapereka ngongole ya mlendo iye akadzalephera kubweza,+ zinthu sizidzamuyendera bwino. Koma wodana ndi kugwirana chanza pochita mgwirizano sakhala ndi nkhawa.
16 Mkazi wachikoka amapeza ulemu.+ Koma anthu ochitira nkhanza anzawo amapeza chuma.
17 Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake,+ koma munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.+
18 Munthu woipa amapeza malipiro achinyengo,+ koma wofesa chilungamo amapeza malipiro enieni.+
19 Munthu wosasunthika pachilungamo adzapeza moyo,+ koma munthu wofunafuna zoipa adzafa.+
20 Anthu a mtima wopotoka amam’nyansa Yehova,+ koma anthu opanda cholakwa m’njira yawo amam’sangalatsa.+
21 Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake, munthu woipa sadzapewa chilango,+ koma ana a anthu olungama adzapulumuka ndithu.+
22 Monga momwe chimakhalira chipini* chagolide pamphuno ya nkhumba, ndi mmenenso amakhalira mkazi wokongola koma wosaganiza bwino.+
23 Zolakalaka za anthu olungama, ndithu n’zabwino.+ Chiyembekezo cha oipa chimabweretsa mkwiyo woopsa.+
24 Pali amene amapatsa mowolowa manja, komabe zinthu zake zimawonjezeka.+ Palinso amene safuna kupatsa ena zinthu zoyenera kuwapatsa, koma amangokhala wosowa.+
25 Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto,+ ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.+
26 Wokana kugulitsa mbewu zake kwa anthu, anthuwo adzam’temberera. Koma wolola kuzigulitsa adzalandira madalitso.+
27 Wofunafuna kuchitira ena zabwino, amafunafuna kuvomerezedwa ndi Mulungu.*+ Koma wofunafuna kuchita zoipa, zoipazo zidzam’bwerera.+
28 Wodalira chuma chake adzagwa,+ koma anthu olungama adzasangalala ngati masamba a zomera.+
29 Aliyense wochititsa nyumba yake kunyanyalidwa+ adzagwira mphepo,+ ndipo munthu wopusa adzakhala wantchito wa munthu wa mtima wanzeru.
30 Zipatso za munthu wolungama ndizo mtengo wa moyo,+ ndipo munthu wopulumutsa miyoyo ndi wanzeru.+
31 Wolungamatu adzalandira mphoto yake padziko lapansi.+ Ndiye kuli bwanji woipa ndi wochimwa?+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “wa mzimu wokhulupirika.”
^ “Chipini” ndi kachitsulo kapena kamtengo kokongoletsera kamene amakaika pabowo limene amaboola pamphuno.
^ Zingatanthauzenso kuvomerezedwa ndi anthu.