Miyambo 26:1-28

26  Monga chipale chofewa m’chilimwe ndiponso mvula pa nthawi yokolola,+ momwemonso ulemerero suyenerera munthu wopusa.+  Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira, ndiponso namzeze* amakhala ndi chifukwa choulukira. Momwemonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.+  Chikwapu n’cha hatchi,+ zingwe n’za pakamwa pa bulu,+ ndipo ndodo ndi yokwapulira msana wa anthu opusa.+  Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake, kuti iweyo usafanane naye.+  Uzimuyankha wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake, kuti asadzione ngati wanzeru m’maso mwake.+  Munthu amene amakankhira nkhani m’manja mwa wopusa ali ngati munthu wopundula mapazi ake, ndiponso ngati munthu amene amamwa chiwawa.+  Mwambi wa m’kamwa mwa anthu opusa uli ngati munthu wa miyendo yolumala amene wasenza madzi.+  Munthu amene amapereka ulemerero kwa munthu wopusa ali ngati munthu wobisa mwala pamulu wa miyala.+  Mwambi wa m’kamwa mwa anthu opusa uli ngati chitsamba chaminga m’manja mwa munthu woledzera.+ 10  Wolemba ntchito munthu wopusa kapena munthu wongodutsa m’njira, ali ngati woponya muvi ndi uta amene amangolasa chilichonse.+ 11  Monga galu amene wabwerera ku masanzi ake, wopusa amabwereza uchitsiru wake.+ 12  Kodi waona munthu wodziona ngati wanzeru m’maso mwake?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu+ kuposa iyeyo. 13  Waulesi amati: “Panjira pali mkango wamphamvu. M’mabwalo a mzinda mukuyendayenda mkango.”+ 14  Chitseko chimazungulira pomwe anachimangirira, ndipo waulesi amangotembenukatembenuka pabedi pake.+ 15  Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera, koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa amaona kuti n’zotopetsa kwambiri.+ 16  Waulesi amadziona kuti ndi wanzeru kwambiri m’maso mwake+ kuposa anthu 7 oyankha zanzeru. 17  Munthu wongodutsa amene amalowerera mkangano womwe si wake n’kukwiya nawo, ali ngati munthu wogwira makutu a galu.+ 18  Monga munthu wamisala amene akuponya zida ndiponso mivi yamoto+ yakupha, 19  ndi mmenenso alili munthu amene amapusitsa mnzake, n’kunena kuti: “Inetu ndimangochita zocheza.”+ 20  Popanda nkhuni moto umazima, ndipo popanda munthu wonenera anzake zoipa mikangano imazilala.+ 21  Monga mmene amakhalira makala pamoto wonyeka ndiponso nkhuni pamoto woyaka, ndi mmenenso amakhalira munthu wokonda kuyambana ndi anthu pokolezera mikangano.+ 22  Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga, zimene zimatsikira mkatikati mwa mimba.+ 23  Milomo yonena zabwino mwachiphamaso koma mumtima muli zoipa, ili ngati siliva wokutira phale.+ 24  Munthu wodana nawe amadzibisa ndi milomo yake, koma mkati mwake mumakhala chinyengo.+ 25  Ngakhale azilankhula mawu okoma,+ usam’khulupirire+ chifukwa mumtima mwake muli zinthu 7 zonyansa.+ 26  Chidani chimaphimbidwa ndi chinyengo. Zoipa zake zidzaululika mumpingo.+ 27  Amene akukumba dzenje adzagweramo yekha,+ ndipo amene akugubuduza mwala udzabwerera kwa iye.+ 28  Lilime lonama limadana ndi amene lam’pweteka,+ ndipo pakamwa polankhula zabwino mokokomeza pamabweretsa chiwonongeko.+

Mawu a M'munsi

Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”