Miyambo 4:1-27
4 Ananu, mverani malangizo* a bambo anu.+ Mvetserani kuti mupeze luso lomvetsa zinthu.+
2 Pakuti ndithu ndidzakupatsani malangizo abwino.+ Musasiye lamulo langa.+
3 Pakuti ine ndinali mwana wabwino kwa bambo anga.+ Ndinali wokondedwa kwambiri ndiponso mmodzi yekhayo pamaso pa mayi anga.+
4 Bambo anga anali kundilangiza+ kuti: “Mtima wako+ ugwire mwamphamvu mawu anga.+ Sunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+
5 Upeze nzeru,+ upezenso luso lomvetsa zinthu.+ Usaiwale ndipo usapatuke pa mawu a m’kamwa mwanga.+
6 Nzeruzo usazisiye ndipo zidzakusunga. Uzikonde ndipo zidzakuteteza.
7 Nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri.+ Peza nzeru, ndipo pa zinthu zonse zimene upeze, upezenso luso lomvetsa zinthu.+
8 Uzilemekeze kwambiri ndipo zidzakukweza.+ Zidzakulemekeza chifukwa chakuti wazikumbatira.+
9 Zidzaika nkhata yamaluwa yokongola kumutu kwako.+ Zidzakuveka chisoti chachifumu chokongola.”+
10 Tamvera mwana wanga, ndipo utsatire mawu anga.+ Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka.+
11 Ndidzakutsogolera m’njira ya nzeru.+ Ndidzakuchititsa kuyenda m’njira zowongoka.+
12 Ukamayenda, sudzayenda mopanikizika+ ndipo ngati ukuthamanga sudzapunthwa.+
13 Gwira malangizo,+ usawataye.+ Uwasunge bwino chifukwa iwo ndiwo moyo wako.+
14 Usalowe panjira ya oipa,+ ndipo usalunjike kunjira ya ochita zoipa.+
15 Uipewe,+ uilambalale.+ Upatukepo, n’kupitirira.+
16 Pakuti iwo sagona kufikira atachita zoipa.+ Tulo sitiwabwerera mpaka atakhumudwitsa wina.+
17 Pakuti amadya mkate wa zoipa+ ndipo amamwa vinyo wachiwawa.+
18 Koma njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.+
19 Njira ya oipa ili ngati mdima.+ Iwo sadziwa chimene chimawapunthwitsa.+
20 Mwana wanga, mvetsera mawu anga.+ Tchera khutu lako ku zonena zanga.+
21 Zisachoke pamaso pako.+ Uzisunge mkati mwa mtima wako.+
22 Pakuti izo ndi moyo kwa amene amazipeza+ ndiponso ndi thanzi labwino kwa thupi lawo lonse.+
23 Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa,+ pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.+
24 Chotsa mawu opotoka pakamwa pako,+ ndipo milomo yachinyengo uiike kutali ndi iwe.+
25 Maso ako aziyang’ana patsogolo.+ Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.+
26 Salaza njira ya phazi lako,+ ndipo njira zako zonse zikhazikike.+
27 Usakhotere kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ Chotsa phazi lako pa zoipa.+