Miyambo 14:1-35

14  Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake,+ koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.+  Munthu woyenda mowongoka mtima amaopa Yehova,+ koma munthu amene amayenda m’njira zokhotakhota amanyoza Mulungu.+  Chikwapu cha kudzikuza chili m’kamwa mwa wopusa,+ koma anthu anzeru milomo yawo imawatsogolera.+  Ngati palibe ng’ombe, chodyeramo chimakhala choyera. Koma zokolola zimachuluka chifukwa cha mphamvu za ng’ombe yamphongo.  Mboni yokhulupirika ndi imene sinama,+ koma mboni yonyenga imanena bodza lokhalokha.+  Munthu wonyoza amafunafuna nzeru ndipo sazipeza. Koma kudziwa zinthu kumakhala kosavuta kwa munthu womvetsa zinthu.+  Choka pamaso pa munthu wopusa,+ chifukwa supeza nzeru m’mawu otuluka pakamwa pake.+  Nzeru za munthu wochenjera ndizo kuzindikira njira imene akuyendamo,+ koma kuganiza mopusa kwa zitsiru ndi chinyengo.+  Anthu opusa akapalamula mlandu amangoseka,+ koma pakati pa anthu owongoka mtima pali mgwirizano.+ 10  Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu,+ ndipo mlendo sangalowerere pamene mtimawo ukusangalala. 11  Nyumba za anthu oipa zidzawonongedwa,+ koma mahema a anthu owongoka mtima adzalemera.+ 12  Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu,+ koma mapeto ake ndi imfa.+ 13  Ngakhale pamene munthu akuseka, mtima wake ukhoza kukhala ukupweteka.+ Ndipo kusangalala kumathera m’chisoni.+ 14  Munthu wa mtima wosakhulupirika adzakhutira ndi zotsatira za njira zake,+ koma munthu wabwino adzakhutira ndi zotsatira za zochita zake.+ 15  Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse,+ koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.+ 16  Munthu wanzeru amachita mantha ndipo amapatuka pa choipa,+ koma wopusa amapsa mtima ndiponso amakhala wodzidalira.+ 17  Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+ koma munthu wotha kuganiza bwino amadedwa.+ 18  Anthu osadziwa zinthu, ndithu adzakhala opusa,+ koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chovala cha kumutu.+ 19  Anthu oipa adzagwadira abwino,+ ndipo oipa adzagwada pazipata za munthu wolungama. 20  Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake,+ koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.+ 21  Munthu wonyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,+ koma wodala ndi munthu wokomera mtima anthu osautsika.+ 22  Anthu okonza chiwembu amasochera,+ koma anthu okonzekera kuchita zabwino amapeza kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+ 23  Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa,+ koma kungolankhula mawu chabe kumasaukitsa. 24  Chisoti chaulemu cha anthu anzeru ndi chuma chawo. Zochita za anthu opusa zimawonjezera kupusa kwawo.+ 25  Mboni yoona imapulumutsa anthu,+ koma mboni yonama imangonena bodza.+ 26  Munthu woopa Yehova amakhulupirira Mulungu pa chilichonse,+ ndipo ana a munthu ameneyu adzapeza malo othawirako.+ 27  Kuopa Yehova ndiko chitsime cha moyo,+ chifukwa kumateteza moyo kumisampha ya imfa.+ 28  Kuchuluka kwa anthu kumakongoletsa mfumu,+ koma kuchepa kwa anthu kumawonongetsa nduna.+ 29  Wosafulumira kukwiya n’ngozindikira zinthu kwambiri,+ koma wokwiya msanga amalimbikitsa uchitsiru.+ 30  Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu,+ koma nsanje imawoletsa mafupa.+ 31  Wobera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+ koma wokomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+ 32  Woipa adzakankhidwa chifukwa cha kuipa kwake,+ koma wolungama adzapeza malo othawirako chifukwa cha mtima wake wosagawanika.+ 33  Mumtima mwa munthu womvetsa zinthu mumakhala nzeru,+ ndipo zimadziwika pakati pa anthu opusa. 34  Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,+ koma tchimo limachititsa manyazi mitundu ya anthu.+ 35  Mfumu imasangalala ndi wantchito wochita zinthu mozindikira,+ koma imakwiya ndi wantchito wochita zinthu zochititsa manyazi.+

Mawu a M'munsi