Miyambo 6:1-35

6  Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza,+ ngati wagwirana chanza ndi mlendo pochita mgwirizano,+  ngati wakodwa ndi mawu a m’kamwa mwako,+ ngati wagwidwa ndi mawu a m’kamwa mwako,  uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse, pakuti wagwa m’manja mwa mnzako:+ Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+  Maso ako asapeze tulo, ndipo maso ako owala asagone.+  Dzipulumutse ngati insa m’manja mwa wosaka, ndiponso ngati mbalame m’manja mwa wosaka mbalame.+  Pita kwa nyerere+ waulesi iwe,+ ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.  Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira,  imakonza chakudya chake m’chilimwe.+ Imasonkhanitsa zakudya zake pa nthawi yokolola.  Kodi ugonabe mpaka liti, waulesiwe?+ Udzuka nthawi yanji kutulo tako?+ 10  Ukapitiriza kugona pang’ono, ukapitiriza katulo pang’ono, ukapitiriza kupinda manja pang’ono pogona,+ 11  umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,+ ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+ 12  Munthu wopanda pake,+ wochita zopweteka anzake, amayenda ndi mawu opotoka.+ 13  Amatsinzinira ena ndi diso lake,+ amapanga zizindikiro ndi phazi lake, ndiponso amapanga zizindikiro ndi zala zake.+ 14  Mumtima mwake muli zopotoka.+ Nthawi zonse amakhala akukonza zoipa.+ Amakhalira kuyambanitsa anthu.+ 15  N’chifukwa chake tsoka lake lidzabwere mwadzidzidzi.+ Adzathyoledwa modzidzimutsa, ndipo sadzachira.+ 16  Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.+ Zilipo zinthu 7 zimene moyo wake umanyansidwa nazo:+ 17  Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+ 18  mtima wokonzera ena ziwembu,+ mapazi othamangira kukachita zoipa,+ 19  mboni yachinyengo yonena mabodza,+ ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.+ 20  Mwana wanga, sunga lamulo la bambo ako,+ ndipo usasiye malangizo a mayi ako.+ 21  Ulimange pamtima pako nthawi zonse+ ndipo ulimange m’khosi mwako.+ 22  Lidzakutsogolera ukamayenda,+ lidzakulondera ukamagona,+ ndipo ukadzuka, lidzakusamalira. 23  Pakuti lamulolo ndilo nyale,+ ndipo malangizo ndiwo kuwala,+ komanso kudzudzula* kowongola zolakwa ndiko njira yamoyo,+ 24  kuti kukuteteze kwa mkazi woipa,+ komanso ku lilime losalala la mkazi wachilendo.+ 25  Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+ Asakukope ndi maso ake owala,+ 26  pakuti munthu amafika potsala ndi mkate wozungulira umodzi wokha chifukwa cha hule,+ koma mkazi wamwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali.+ 27  Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+ 28  Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa? 29  N’chimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake.+ Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa.+ 30  Anthu sanyoza munthu wakuba, akaba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala. 31  Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7. Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali za m’nyumba mwake.+ 32  Aliyense wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru mumtima mwake.+ Amene amachita zimenezi amawononga moyo wake.+ 33  Adzapeza tsoka ndi manyazi,+ ndipo kunyozeka kwake sikudzafufutika.+ 34  Pakuti nsanje ya mwamuna imautsa mkwiyo wake,+ ndipo sadzamva chisoni pa tsiku lobwezera.+ 35  Iye sadzavomera dipo* lamtundu uliwonse, ndipo sadzalola ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.