Miyambo 22:1-29

22  Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.+ Kulemekezedwa kuli bwino kuposa siliva ndi golide.+  Munthu wolemera ndiponso munthu wosauka n’chimodzimodzi.+ Amene anapanga onsewa ndi Yehova.+  Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala,+ koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.+  Zotsatirapo za kudzichepetsa ndiponso kuopa Yehova ndizo chuma, ulemerero, ndi moyo.+  Minga ndi misampha zimakhala m’njira ya munthu wochita zopotoka,+ koma woteteza moyo wake amakhala nazo kutali.+  Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera.+ Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.+  Wolemera ndi amene amalamulira anthu osauka,+ ndipo wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.+  Wofesa zosalungama adzakolola zopweteka,+ ndipo ndodo ya ukali wake idzatha.+  Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+ 10  Thamangitsa wonyoza, kuti mikangano ithe ndiponso kuti milandu ndi kunyozedwa zilekeke.+ 11  Amene amakondwera kukhala ndi mtima woyera+ ndiponso amene mawu ake ndi okopa, adzakhala bwenzi la mfumu.+ 12  Maso a Yehova amateteza wodziwa zinthu,+ koma iye amawononga mawu a munthu wochita zachinyengo.+ 13  Waulesi amati:+ “Panja pali mkango!+ Ndithu undipha pakati pa bwalo la mzinda!” 14  Pakamwa pa akazi achilendo pali ngati dzenje lakuya.+ Wotsutsidwa ndi Yehova adzagweramo.+ 15  Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.+ Koma ndodo yomulangira* ndi imene imauthamangitsira kutali ndi iye.+ 16  Amene amabera mwachinyengo munthu wonyozeka kuti apeze zinthu zambiri,+ komanso wopereka mphatso kwa munthu wolemera, ndithu adzasauka.+ 17  Tchera khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzeru,+ kuti ulandire ndi mtima wonse nzeru zochokera kwa ine.+ 18  Pakuti n’chinthu chosangalatsa kuti uzisunge mumtima mwako,+ kuti zikhazikike pamilomo yako.+ 19  Lero ndakudziwitsa zinthu,+ kuti uzidalira Yehova. 20  Kodi sindinakulembere zinthu zolangiza ndi zophunzitsa,+ 21  n’cholinga chakuti ndikusonyeze kudalirika kwa mawu oona, kuti uthe kubwezera mawu oonadi kwa amene wakutuma?+ 22  Usabere munthu wonyozeka chifukwa chakuti ndi wonyozeka,+ ndipo usapondereze wosautsika pachipata cha mzinda.+ 23  Pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo,+ ndipo adzalanda moyo wa amene akuwabera.+ 24  Usamagwirizane ndi munthu aliyense wokonda kukwiya,+ ndipo usamayende ndi munthu waukali, 25  kuti usazolowere njira zake ndi kuikira moyo wako msampha.+ 26  Usakhale pakati pa anthu ogwirana chanza,+ pakati pa anthu amene amakhala chikole cha ngongole za anthu ena.+ 27  Ukadzalephera kulipira, adzakulanda ngakhale bedi limene umagonapo. 28  Usasunthire kumbuyo malire akalekale, amene makolo ako anaika.+ 29  Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu.+ Sadzaima pamaso pa anthu wamba.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.