Miyambo 27:1-27

27  Usadzitame ndi zamawa+ chifukwa sukudziwa zimene zidzachitike mawa.+  Mlendo akutamande, osati pakamwa pako. Munthu wochokera kudziko lina achite zimenezo, osati milomo yako.+  Mwala umalemera ndiponso mchenga umalemera ukaunyamula,+ koma kusautsa kwa munthu wopusa kumalemera kwambiri kuposa zonsezi.+  Mkwiyo umasefukira ndipo ukali ndi wankhanza,+ koma nsanje ndani angaipirire?+  Kudzudzula munthu mosabisa mawu, kuli bwino+ kusiyana ndi kumukonda koma osamusonyeza chikondicho.  Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupirika,+ koma kuti munthu wodana nawe akupsompsone pamafunika kumuchonderera.+  Munthu akakhuta amapondaponda uchi wa kuchisa, koma kwa munthu wanjala chinthu chilichonse chowawa chimatsekemera.+  Monga mbalame imene ikuthawa pachisa pake,+ ndi mmenenso amakhalira munthu amene akuthawa kwawo.+  Mafuta ndi zofukiza zonunkhira+ n’zimene zimasangalatsa mtima, chimodzimodzinso kukoma kwa mnzako chifukwa cha malangizo ake ochokera pansi pa mtima, kumasangalatsa mtima.+ 10  Usasiye mnzako kapena mnzawo wa bambo ako, ndipo usalowe m’nyumba ya m’bale wako pa tsiku limene tsoka lakugwera. Munthu woyandikana naye nyumba amene ali pafupi ali bwino kuposa m’bale wako amene ali kutali.+ 11  Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga,+ kuti ndimuyankhe amene akunditonza.+ 12  Wochenjera amene waona tsoka amabisala.+ Koma anthu osadziwa zinthu amene amangopitabe amalangidwa.+ 13  Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo,+ umulande chovala chake. Ndiponso wochita zoipa ndi mkazi wachilendo umulande chikole.+ 14  Munthu amene amadalitsa mnzake mokuwa m’mawa kwambiri, anthu adzamuona ngati akutemberera.+ 15  Denga lodontha limene limathawitsa munthu pa tsiku la mvula yosalekeza, limafanana ndi mkazi wolongolola.+ 16  Aliyense wobisa mkaziyo wabisa mphepo, ndipo dzanja lake lamanja limagwira mafuta. 17  Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.+ 18  Amene akuteteza mtengo wa mkuyu adzadya zipatso zake,+ ndipo amene akuteteza mbuye wake adzalemekezedwa.+ 19  Monga momwe nkhope imaonekera chithunzi chake m’madzi, momwemonso mtima wa munthu umaonekera mumtima wa munthu wina. 20  Manda ndiponso malo a chiwonongeko+ sakhuta.+ Nawonso maso a munthu sakhuta.+ 21  Siliva amamuyengera m’mbiya yoyengera+ ndipo golide amamuyengera m’ng’anjo,+ momwemonso chitamando choperekedwa kwa munthu chimasonyeza mmene iye alili.+ 22  Ngakhale utasinja chitsiru mumtondo ndi musi limodzi ndi mbewu, uchitsiru wake sungachichokere.+ 23  Uyenera kudziwa bwino maonekedwe a ziweto zako. Ika mtima wako pa magulu a ziweto zako,+ 24  pakuti chuma sichidzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo chisoti chachifumu sichidzakhalapo ku mibadwo yonse. 25  Udzu wobiriwira wapita, udzu watsopano waoneka, ndipo zomera za m’mapiri zasonkhanitsidwa.+ 26  Nkhosa zamphongo zazing’ono zimakupezetsa zovala,+ ndipo mbuzi zamphongo ndizo malipiro ogulira munda. 27  Pali mkaka wa mbuzi wokwanira woti udye, woti ukhale chakudya cha banja lako, ndiponso wopezera zofunika+ za pa moyo wa atsikana ako.

Mawu a M'munsi